LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 November masa. 22-27
  • “Ndiwe Munthu Wamtengo Wapatali Kwambili”!

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Ndiwe Munthu Wamtengo Wapatali Kwambili”!
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MMENE YESU ANATHANDIZILA ANTHU KUZINDIKILA KUTI NDI AMTENGO WAPATALI
  • ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUTI TIZIDZIONA MMENE YEHOVA AMATIONELA
  • Yehova “Amacilitsa Anthu Osweka Mtima”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Yehova Amakukonda Kwambili
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zimene Yesu Anacita M’masiku Ake 40 Othela Padziko Lapansi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 November masa. 22-27

NKHANI YOPHUNZILA 47

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

“ Ndiwe Munthu Wamtengo Wapatali Kwambili”!

“ Ndiwe munthu wamtengo wapatali kwambili.”​—DAN. 9:​23, mau a m’munsi.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kuthandiza anthu amene amadziona kuti ndi osafunika kumvetsa kuti ndi amtengo wapatali kwa Yehova.

1-2. N’ciani cingatithandize kukhala otsimikiza kuti ndife amtengo wapatali pamaso pa Yehova?

YEHOVA amaona atumiki ake kuti ndi amtengo wapatali. Ngakhale n’telo, ena amadziona ngati osafunika. Mwina amadziona conco cifukwa ca zimene anthu ena anawacita. Kodi inunso mumamva conco nthawi zina? Ngati n’telo, n’ciani cingakuthandizeni kukhala wotsimikiza kuti Yehova amakukondani kwambili?

2 Cimodzi cimene cingakuthandizeni ndi kuwelenga nkhani za m’Baibo zoonetsa mmene Yehova amafunila kuti anthu azicitila zinthu ndi ena. Mwana wake Yesu anali kucita zinthu ndi anthu mokoma mtima ndi mwaulemu. Mwakutelo, anaonetsa kuti iye ndi Atate wake amawaona kuti ndi amtengo wapatali anthu odzicepetsa amene amadziona kuti ndi otsika. (Yoh. 5:19; Aheb. 1:3) M’nkhani ino, tikambilana: (1) mmene Yesu anathandizila anthu kuti azidziona kuti ndi amtengo wapatali, komanso (2) mmene tingakhalile otsimikiza kuti Mulungu amationadi kuti ndife amtengo wapatali.​—Hag. 2:7.

MMENE YESU ANATHANDIZILA ANTHU KUZINDIKILA KUTI NDI AMTENGO WAPATALI

3. Kodi Yesu anawathandiza bwanji Agalileya amene anabwela kwa iye kudzafuna thandizo?

3 Pa ulendo wa Yesu wacitatu wokalalikila ku Galileya, khamu la anthu ocokela m’madela osiyana-siyana linabwela kudzamvetsela uthenga wa Yesu ndi kudzacilitsidwa. Yesu anati anthuwo “anali omyuka-myuka komanso otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Atsogoleli ao acipembedzo anali kuwaona ngati osafunika, ndipo anali kuwanena kuti ndi “otembeleledwa.” (Yoh. 7:​47-49) Koma Yesu anasonyeza kuti anali kuwaona kuti ndi amtengo wapatali mwa kuwaphunzitsa ndi kuwacilitsa. (Mat. 9:35) Kuonjezela apo, pofuna kuthandiza anthu ambili, iye anaphunzitsa ophunzila ake kulalikila ndipo anawapatsa mphamvu zotha kucilitsa odwala.​—Mat. 10:​5-8.

4. Tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene Yesu anali kucitila zinthu ndi anthu amene anali kuonedwa ngati otsika?

4 Yesu anali kucita zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu ndi anthu amene anali kumumvetsela. Izi zinaonetsa kuti iye ndi Atate wake amawaona kuti ndi amtengo wapatali anthu amene ena amawaona kuti ndi otsika. Ngati mukutumikila Yehova koma nthawi zina mumadziona ngati wosafunika, ganizilani mmene Yesu anacitila zinthu ndi anthu odzicepetsa amene anali kufuna kuphunzila kwa iye. Kucita zimenezi kungakuthandizeni kuona kuti ndinu ofunika kwambili pamaso pa Yehova.

5. Kodi zinthu zinali motani pa umoyo wa mzimai wa ku Galileya amene anakumana ndi Yesu?

5 Kuonjezela pa kuphunzitsa anthu monga gulu, Yesu anali kuphunzitsanso munthu aliyense payekha ndi kum’thandiza. Mwacitsanzo, pa utumiki wake wa ku Galileya, Yesu anakumana ndi mai amene anali kudwala matenda otaya magazi kwa zaka 12. (Maliko 5:25) Malinga ndi Cilamulo ca Mose, maiyo anali wodetsedwa. Ndipo aliyense wom’khudza anali kukhalanso wodetsedwa. Conco, iye ayenela kuti anali kukhala yekha nthawi zambili. Komanso, analibe mwai wolambila pamodzi ndi anthu ena ku sunagoge, kapena pa zikondwelelo. (Lev. 15:​19, 25) Mosakaikila, matendawa anali kumusautsa komanso kum’pangitsa kudziona ngati wosafunika.​—Maliko 5:26.

6. Kodi mzimai amene anali kudwala matenda otaya magazi anacita ciani kuti acilitsidwe?

6 Mzimai ameneyu anali kufuna kuti Yesu am’cilitse. Koma sanam’pemphe mwacindunji. N’cifukwa ciani? Mwina anacita manyanzi cifukwa ca matenda ake. Mwinanso, anaopa kuti Yesu angakane kum’cilitsa cifukwa malinga ndi Cilamulo, iye anali wodetsedwa ndipo sanali kufunika kupezeka pa gulu. Conco, anangogwila cobvala cake cakunja pokhulupilila kuti akacita zimenezo acila. (Maliko 5:​27, 28) Cifukwa ca cikhulupililo cake, iye anacilitsidwadi. Kenako, Yesu anafunsa kuti, “Ndani wagwila malaya anga akunja?’’ Pamenepo mzimaiyo anaulula kuti ndiye anam’gwila. Kodi Yesu anatani atadziwa zimenezi?

7. Kodi Yesu anacita zinthu motani ndi mai amene anali kudwala matenda aakulu? (Maliko 5:34)

7 Yesu anacita zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu ndi maiyo. Iye anaona kuti maiyo “anacita mantha n’kuyamba kunjenjemela.” (Maliko 5:33) Poganizila mmene anali kumvela, Yesu analakhula naye mokoma mtima. Kuonjezela pamenepo, anam’chula kuti “mwanawe.” Mauwa anaonetsa ulemu, kukoma mtima, ndi cikondi. (Welengani Maliko 5:34.) M’Baibo yonse, apa ndipo pokha pomwe Yesu anauza mkazi kuti ‘mwanawe.’ Ayenela kuti anagwilitsa nchito mau amenewa poona kuti mzimaiyu anacita mantha kwambili. Izi ziyenela kuti zinam’khazika mtima pansi! Zimene Yesu anakamba ziyenela kuti zinapangitsa kuti mzimaiyu asadziimbe mlandu cifukwa cogwila cobvala cake komanso kupezeka pa gulu. Zinathandizanso maiyo kuona kuti Atate wake wakumwamba anali kum’konda kwambili.

8. N’zobvuta ziti zimene mlongo wina wa ku Brazil anakumana nazo?

8 Masiku anonso, atumiki a Mulungu ena akudwala matenda amene amawapangitsa kudziona ngati osanunkha kanthu. Maria,a mpainiya wa nthawi zonse wa ku Brazil, amene anabadwa wopanda miyendo ndi dzanja la kumanzele, anakamba kuti: “Nthawi zonse anzanga a kusukulu anali kundibvutitsa cifukwa cokhala wolemala. Iwo anali kundicha maina amene anali kundikhumudwitsa kwambili. Nthawi zina, ngakhale a m’banja langa anali kucita zinthu zimene zinali kundipangitsa kudziona ngati wacabe-cabe.”

9. N’ciani cinathandiza Maria kudziwa kuti ndi wamtengo wapatali kwa Yehova?

9 Kodi n’ciani cinam’thandiza Maria? Atakhala Mboni ya Yehova, abale anam’limbikitsa ndi kum’thandiza kuyamba kudziona mmene Yehova amamuonela. Iye anati: “Pali anthu ambili amene anandithandiza moti sindingathe kuwawelenga. Conco, ndimayamikila Yehova ndi mtima wanga wonse pondipatsa banja lauzimu.” Abale ndi alongo a Maria anam’thandiza kuzindikila kuti ndi wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.

10. Kodi Mariya Mmagadala anali ndi bvuto lotani? Nanga anali kudziona bwanji? (Onaninso zithunzi.)

10 Ganizilani mmene Yesu anathandizila munthu winanso dzina lake Mariya Mmagadala. Iye anali ndi ziwanda 7! (Luka 8:2) Mwacionekele, mzimaiyo anali kucita zinthu zacilendo cifukwa ziwandazo zinali kum’lamulila. Conco, anthu ambili anali kumupewa. Pa nthawi yobvuta imeneyi, ayenela kuti anali kudziona kuti ndi wosalidwa, wosakondedwa, komanso wopanda wom’thandiza. Yesu anatulutsa ziwandazo mwa iye, ndipo anakhala wophunzila wake wodzipeleka kwambili. N’ciani cina cimene Yesu anacita comwe cinathandiza Mariya Mmagadala kuona kuti ndi wamtengo wapatali kwa Mulungu?

Zithunzi: 1. Yesu akuyang’ana mzimai wina dzina lake Mariya Mmagadala. Mzimaiyu wagwada pakanjila kodutsa pakati pazimango pomwe pali kamdima. 2. Mariya Mmagadala akuyenda ndi Yesu limodzi ndi ophunzila ake ndipo akumwetulila.

Kodi Yesu anam’thandiza bwanji Mariya Mmagadala kuzindikila kuti anali wofunika pamaso pa Yehova? (Onani ndime 10-11)


11. Kodi Yesu anamuonetsa bwanji Mariya Mmagadala kuti ndi wamtengo wapatali kwa Mulungu? (Onaninso zithunzi.)

11 Yesu anapatsa Mariya Mmagadala mwai wolalikila naye limodzi mudzi ndi mudzi.b Conco iye anapitilizabe kupindula ndi zimene Yesu anali kuphunzitsa anthu ena. Cinanso, Yesu atangoukitsidwa, tsiku lomwelo anaonekela kwa maiyu. Iye anali mmodzi mwa ophunzila amene Yesu analankhula nao atangoukitsidwa. Yesu anam’tuma kuti akauze atumwi ake kuti iye waukitsidwa. Uwu unali umboni wamphamvu wakuti Yehova anali kumuona kuti ndi wamtengo wapatali!​—Yoh. 20:​11-18.

12. Fotokozani zimene zinapangitsa Lidia kuyamba kudziona ngati wacabe-cabe.

12 Monga mmene zinalili kwa Mariya Mmagadala, ambili masiku ano amabvutika ndi maganizo odziona ngati acabe-cabe. Mlongo wina wa ku Spain, dzina lake Lidia, ananena kuti iye asanabadwe, amai ake anafuna kumupha mwa kucotsa mimba. Iye akumbukila kuti ali mwana kwambili, amai ake anali kumucita nkhanza komanso kumulankhula mau oipa. Mlongo Lidia anati: “Colinga canga cinali kupeza anthu amene angandikonde ndi kukhala mabwenzi anga. Cifukwa cakuti amai anali kundiuza kuti ndine munthu woipa, n’nali kuona kuti palibe amene angandikonde.”

13. N’ciani cinathandiza Lidia kuyamba kudziona kuti ndi wofunika kwambili pamaso pa Yehova?

13 Lidia ataphunzila coonadi, pemphelo, phunzilo la munthu mwini, komanso mau ndi zocita za abale ndi alongo zoonetsa kukoma mtima, zinam’thandiza kuyamba kudziona kuti ndi wofunika kwambili pamaso pa Yehova. Iye anati: “Mwamuna wanga nthawi zambili amandiuza kuti amandikonda. Nthawi ndi nthawi amandikumbutsa makhalidwe abwino amene ndili nao. Naonso anzanga amacita cimodzi-modzi.” Kodi pali munthu wina amene mungafunike kumuthandiza kuti ayambe kudziona kuti ndi wamtengo wapatali pamaso pa Yehova?

ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUTI TIZIDZIONA MMENE YEHOVA AMATIONELA

14. Kodi lemba la 1 Samueli 16:7 lingatithandize bwanji kuti tizidziona mmene Yehova amationela? (Onani bokosi lakuti “N’cifukwa Ciani Yehova Amaona Anthu Ake Kukhala Ofunika Kwambili?”)

14 Kumbukilani kuti Yehova sakuonani mmene anthu a m’dzikoli amakuonelani. (Welengani 1 Samueli 16:7.) Anthu a m’dzikoli amaona kuti munthu ndi wofunika cifukwa ca maonekedwe ake, cuma cimene ali naco, kapena maphunzilo amene anapata. Koma umu si mmene Yehova amationela. (Yes. 55:​8, 9) Conco, m’malo modziona mmene anthu a m’dzikoli amakuonelani, muzidziona mmene Yehova amakuonelani. Mungacite bwino kuwelenga nkhani za anthu a m’Baibo monga Eliya, Naomi, ndi Hana, amene panthawi ina anali kudziona ngati osafunika, koma Yehova anali kuwakonda. Mungalembenso zocitika zimene zimakutsimikizilani kuti Yehova amakukondani ndi kukuonani kuti ndinu amtengo wapatali. Kuonjezela apo, mungawelenge nkhani m’zofalitsa zathu zimene zingakuthandizeni kupewa maganizo odziona ngati wosafunika.c

N’cifukwa Ciani Yehova Amaona Anthu Ake Kukhala Ofunika Kwambili?

Yehova analenga anthu mosiyana kwambili ndi nyama. Anatilenga m’njila yakuti tizitha kukhala naye pa ubwenzi. (Gen. 1:27; Sal. 8:5; 25:14; Yes. 41:8) Ici n’cifukwa comveka cokhulupilila kuti Yehova amationa kuti ndife ofunika. Cifukwa cina cacikulu n’cakuti tikasankha kuyandikila Yehova, kumumvela, ndi kudzipeleka kwa iye, timakhala ofunika kwambili pamaso pake.​—Yes. 49:15.

15. N’cifukwa ciani Yehova anali kuona kuti Danieli ndi “munthu wamtengo wapatali kwambili”? (Danieli 9:​23, mau a m’munsi)

15 Dziwani kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wofunika cifukwa ca kukhulupilika kwanu. Pa nthawi ina, mneneli Danieli ali ndi zaka za m’ma 90, anafooka kwambili ndipo anataya mtima. (Dan. 9:​20, 21) Kodi Yehova anamulimbikitsa bwanji? Anatumiza mngelo Gabirieli kuti akakumbutse Danieli kuti ndi “munthu wamtengo wapatali kwambili,” komanso kuti Mulungu wamva mapemphelo ake. (Welengani Danieli 9:​23, mau a m’munsi.) N’cifukwa ciani Mulungu anali kuona Danieli kukhala munthu wofunika kwambili? Cifukwa Danieli anali wolungama ndi wokhulupilika. (Ezek. 14:14) Yehova anaonetsetsa kuti nkhani ya Danieli yalembedwa m’Mau ake kuti izitilimbikitsa. (Aroma 15:4) Mofananamo, Yehova amamva mapemphelo anu, ndipo amakuonani kuti ndinu wofunika cifukwa mumakonda cilungamo komanso mumam’tumikila mokhulupilika.​—Mika 6:​8,mau a munsi; Aheb. 6:10.

16. Nciani cingakuthandizeni kuona Yehova kukhala Tate wanu wacikondi?

16 Muziona kuti Yehova ndi Atate wanu amene amakukondani. Iye amafuna kukuthandizani osati kukupezani zifukwa. (Sal. 130:3; Mat. 7:11; Luka 12:​6, 7) Kuganizilani zimenezi kwathandiza anthu ambili amene anali ndi maganizo odziona ngati osafunika. Mwacitsanzo, ganizilani za mlongo wina wa ku Spain dzina lake Michelle. Iye anali kudziona ngati wacabe-cabe komanso wosakondedwa cifukwa kwa zaka zambili mwamuna wake anali kumunyoza kwambili. Iye anati, “Ndikayamba kudziona ngati wosafunika, ndimayelekeza kuti ndikuona Yehova atandinyamula m’manja mwake n’kumandionetsa cikondi komanso kunditeteza.” (Sal. 28:9) Mlongo wina wa ku South Africa, dzina lake Lauren, akayamba kudziona wosafunika, mumtima mwake amati: “Popeza Yehova anandikokela kwa iye mwacikondi, ndipo wandithandiza kukhalabe naye pa ubwenzi kwa zaka zonsezi, ndipo wafika ngakhale pondigwilitsa nchito kuphunzitsa ena, ndiye kuti mosakaikila amandiona kuti ndine wofunika kwambili.”​—Hos. 11:4.

17. Nciani cingakuthanzeni kutsimikiza kuti Yehova amakukondani? (Salimo 5:12) (Onaninso cithunzi.)

17 Khalani wotsimikiza kuti Yehova amasangalala nanu. (Welengani Salimo 5:12.) Davide anati Yehova amasangalala ndi anthu olungama ndipo amawateteza ndi “cishango cacikulu.” Kudziwa kuti Yehova amasangalala nanu ndiponso kuti amakuthandizani, kungakutetezeni ku maganizo odziona kuti ndinu wosafunika. Kodi mungatsimikize bwanji kuti Yehova amakukondani? Monga taonela, Yehova amatitsimikizila kuti amatikonda pogwilitsa nchito Mau ake. Iye amagwilitsanso nchito akulu, mabwenzi athu apamtima, komanso anthu ena potitsimikizila kuti ndife ofunika pamaso pake. Kodi tiyenela kutani tikalandila thandizo lao?

Mlongo akucoka pa Nyumba ya Ufumu akumwetulila. Akupita mu utumiki ndi mlongo wina yemwe wam’kumbatila.

Kudziwa kuti Yehova amasangalala nafe kungatithandize kupewa maganizo odziona ngati osafunika (Onani ndime 17)


18. N’cifukwa ciani simuyenela kukana ena akakuyamikilani?

18 Anthu amene amakudziwani bwino komanso kukukondani akakuyamikilani, musakane ciyamikilo cao poganiza kuti akungokokomeza. Muzikumbukila kuti Yehova angawagwilitse nchito pokuthandizani kutsimikiza kuti iye amakukondani. Michelle, amene tam’chulapo kale m’nkhani ino, anati: “Pang’ono m’pang’ono ndayamba kukhulupilila mau okambidwa mokoma mtima amene ena amandiuza. Nthawi zina zimakhala zobvuta, koma ndidziwa kuti ndi zimene Yehova afuna kuti ndizicita.” Michelle wapindulanso cifukwa ca thandizo la akulu. Iye pano ndi mpainiya wanthawi zonse ndipo amathandizila pa nchito za pa Beteli ali kunyumba.

19. N’cifukwa ciani simuyenela kukaikila kuti ndinu amtengo wapatali pamaso pa Mulungu?

19 Yesu anatikumbutsa kuti Atate wathu wakumwamba amationa kuti ndife ofunika kwambili. (Luka 12:24) Conco, sitiyenela kukaikila kuti Yehova amationa kuti ndife amtengo wapatali. Conde, musamaiwale mfundo imeneyi! Tiyeni tonse tiziyesetsa mmene tingathele kuthandiza ena kuona kuti ndi ofunika kwambili pamaso pa Yehova!

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yesu anawathandiza bwanji anthu kuzindikila kuti anali amtengo wapatali?

  • Kodi Yesu anam’thandiza bwanji mai amene anali kudwala matenda otaya magazi?

  • N’ciani cingatithandize kuti tizidziona mmene Yehova amationela?

Nyimbo 139 Yelekeza Uli M’dziko Latsopano

a Maina ena asinthidwa.

b Zioneka kuti Mariya Mmagadala anali mmodzi mwa azimai amene anali kuyenda ndi Yesu. Azimai amenewa anali kusamalila Yesu ndi atumwi ake pogwilitsa nchito cuma cao.​—Mat. 27:​55, 56; Luka 8:​1-3.

c Mwacitsanzo, onani mutu 24 m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova. Komanso welengani malemba ndi nkhani za m’Baibo pansi pa kamutu kakuti “Kudzikaikila,” m’buku lakuti Mfundo Zothandiza pa Umoyo Wacikhristu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani