LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 November tsa. 31
  • Mafunso Ocokela kwa Owelenga

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mafunso Ocokela kwa Owelenga
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Nkhani Zofanana
  • Buku la Chivumbulutso—Cimene Cidzacitikila Adani a Mulungu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Musamaope Zilombo Zoopsa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 November tsa. 31

Mafunso Ocokela kwa Owelenga

Kodi m’tsogolomu ndi “maganizo” ati amene Yehova adzaike m’mitima ya olamulila?

Ponena za mmene cisautso cacikulu cidzayambile, lemba la Chivumbulutso 17:​16, 17 limati: “Nyanga 10 zimene waziona zija komanso cilombo, zidzadana ndi hulelo. Zidzatenga zinthu zake zonse nʼkulisiya lamalisece ndipo zidzadya minofu yake nʼkulipsyeleza ndi moto. Cifukwa Mulungu anaika pulani mʼmitima yao kuti zicite mogwilizana ndi maganizo ake komanso kuti zikwanilitse maganizo ao ofanana aja, popeleka ufumu wao kwa cilombo.” Kale, zofalitsa zathu zinali kufotokoza kuti “maganizo” amene Yehova adzaike m’mitima ya olamulila a dziko ndi akuti olamulilawo aononge zipembedzo zonyenga.

Komabe, tifunika kusintha kamvedwe kathu pankhaniyi. “Maganizo” omwe Yehova adzaike m’mitima ya olamulila a dziko ndi oti iwo “adzapeleke ufumu wao kwa cilombo.” Kuti timvetse mmene izi zidzacitikile, tiyeni tiganizile mafunso awa.

Kodi ulosiwu ukunena za ndani maka-maka? “Hulelo,” lochedwanso “Babulo wamkulu,” liimila ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga. “Cilombo cofiila kwambili” ciimila bungwe lokhazikitsa mtendele la League of Nations limene linakhazikitsidwa mu 1919, ndipo panopa limachedwa United Nations. (Chiv. 17:​3-5) “Nyanga 10” zikuimila maboma onse amene ali ku mbali ya cilombo.

Kodi pali ubale wotani pakati pa hulelo ndi cilombo cofiila kwambili? Hulelo lakhala lili pamsana pa cilomboco. Limacidalitsa, kuciuza zocita, ngakhale kucilamulila kumene.

N’ciani cidzalicitikile hulelo? Cilomboco limodzi ndi nyanga 10 zimene zimacicilikiza “zidzadana nalo hulelo.” Iwo adzalanda cuma cake conse ndi kuonetsa poyela kuipa kwake. Ndipo adzaliononga kothelatu mogwilizana ndi cifunilo ca Yehova. (Chiv. 17:1; 18:8) Awa adzakhala mapeto a zipembedzo zonyenga. Koma izi zisanacitike, Yehova adzapangitsa maboma kucita cinthu cimene sicinacitikepo m’mbili yonse ya anthu pankhani ya ulamulilo.

Kodi Yehova adzacititsa olamulila a dziko kutani? Adzaika “maganizo ake” m’mitima ya nyanga 10. Maganizo akewo ndi akuti nyanga 10 zimenezo ‘zipeleke mphamvu zao ndi ulamulilo wao kwa cilombo [cofiila kwambili],’ cimene ciimila bungwe la United Nations. (Chiv. 17:13) Kodi izi zitanthauza kuti maboma adzapanga ciganizo pa okha copeleka mphamvu zao ndi ulamulilo wao kwa cilomboco? Ayi! Ulosiwu uonetsa kuti Mulungu ndiye adzawapangitsa kucita zimenezi. (Miy. 21:1; yelekezelani ndi Yesaya 44:28.) Kodi adzapeleka mphamvu zao mwapang’ono-pang’ono? Ayinso! Izi zidzacitika mwadzidzidzi. Kenako, cilombo cimene cidzakhala citangopatsidwa kumene mphamvu zoculuka, cidzaononga zipembedzo zonse zonyenga kothelatu.

Ndiye tiyembekezele zotani? Tisayembekezele kuti padzakhala malipoti a panyuzi otidziwitsa kuti maboma ayamba kupeleka pang’ono-pang’ono mphamvu zao ku bungwe la United Nations. Koma tiyembekezele izi: Mwadzidzidzi, Yehova adzapangitsa maboma kupeleka mphamvu zao kwa cilombo. Zimenezi zikadzacitika, tidzadziwe kuti cisautso cacikulu catsala pang’ono kuyamba. Conco, “tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino” cifukwa posacedwapa zinthu zisintha mwadzidzidzi!​—1 Ates. 5:6.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani