KHALANIBE MASO!
Anthu 6 Miliyoni Amwalila na Mlili wa COVID—Kodi Baibo Ikambapo Ciyani?
Bungwe Loona Zaumoyo Padziko Lonse, la WHO, linati pofika pa May 23, 2022, anthu okwana 6.27 miliyoni anamwalila na mlili wa COVID-19. Komabe m’lipoti lawo la pa May 5, 2022, anaonetsa kuti ciŵelengelo cake ceniceni n’cacikulu kwambili kuposa pamenepa. Bungweli linakamba kuti mkati mwa 2020 na 2021, “anthu onse amene anamwalila na COVID-19 yeniyeniyo, komanso omwe analinso kale na matenda ŵena . . . anakwana pafupifupi 14.9 miliyoni.” Kodi Baibo ikambapo ciyani pa milili yoopsa yotele?
Baibo inakambilatu kuti kudzabwela milili yoopsa
Yesu ananenelatu kuti kudzakhala “milili,” kapena kuti matenda ofalikila, pa nthawi ya “masiku otsiliza.”—Luka 21:11; 2 Timoteyo 3:1
Ulosi wa Yesu umenewu ukukwanilitsidwa masiku ano. Kuti mudziŵe zambili ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Chizindikiro cha ‘Masiku Otsiriza,’ Kapena kuti ‘Nthawi ya Mapeto’ N’chiyani?”
Baibo Imapeleka Citonthozo
“Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 Akorinto 1:3, 4.
Anthu ambili omwe atayikidwa wokondedwa wawo mu imfa, apeza citonthozo mu uthenga wa m’Baibo. Kuti mudziŵe zambili ŵelengani nkhani yakuti, “Zimene Mungacite Palipano Mukafedwa,” komanso yakuti, “Thandizo Lodalilika Kwambili kwa Ofedwa.”
Baibo Imatiunikila Njila Imene Idzathetselatu Matenda Onse
“Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.”—Mateyu 6:10.
Posacedwa, “Ufumu wa Mulungu” udzaonetsetsa kuti “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: “Ndikudwala.” (Maliko 1:14, 15; Yesaya 33:24) Kuti mudziŵe zambili zokhudza boma lakumwamba limeneli, komanso zimene lidzacite, tambani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
Tikukulimbikitsani kuti muphunzile zambili zomwe Baibo imanena, kotelo kuti inuyo na banja lanu mupindule na ulangizi wake wothandiza, komanso kuti mudziŵe malonjezo ake ocititsa cidwi.