Kumanzele: Namondwe wochedwa Ian, ku Florida, America, September 2022 (Sean Rayford/Getty Images); pakati: Mayi akuthaŵa nkhondo na mwana wake ku Donetsk, ku Ukraine, July 2022 (Alex Chan Tsz Yuk/SOPA Images/LightRocket via Getty Images); kulamanja: Anthu ambili-mbili akupimitsa matenda a COVID-19 ku Beijing, China, April 2022 (Kevin Frayer/Getty Images)
KHALANI MASO!
2022: Caka ca Matsoka—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
M’caka ca 2022, nkhani zambili panyuzi zinali kukamba za nkhondo, mavuto azacuma, komanso ngozi zacilengedwe. Baibo yokha ndiyo imafotokoza tanthuzo lenileni la zocitika zimenezi.
Tanthauzo la zocitika za mu 2022
Zocitika za caka catha, zikupeleka umboni woonetselatu kuti tikukhala m’masiku omwe Baibo imawacha “masiku otsiliza.” (2 Timoteyo 3:1) Nyengo imeneyi inayamba m’caka ca 1914. Onani mmene zocitika zaposacedwa zikukwanilitsila ulosi wa m’Baibo wonena za nthawi yathu ino.
“Nkhondo.”—Mateyu 24:6.
“2022 ni Caka Cimene Tsoka la Nkhondo Linabwelelanso ku Europe.”a
Onani nkhani yakuti “Russia Athila Nkhondo Ukraine.”
“Njala.”—Mateyu 24:7.
“2022: Caka ca Njala Yadzaoneni.”b
Onani nkhani yakuti “Nkhondo ya ku Ukraine Iwonjezela Njala Padziko Lonse.”
“Milili.”—Luka 21:11.
“Matenda oyambukila akuculukila-culukila, ndipo anthu ali pa ciwopsezo cacikulu. Tikunena izi cifukwa matenda a polio abwelanso. Kwabukanso matenda a monkeypox, ndipo COVID-19 nayonso ikupitilizabe kuvutitsa anthu.”c
Onani nkhani yakuti “Anthu 6 Miliyoni Amwalila na COVID.”
“Kudzaoneka zoopsa.”—Luka 21:11.
“Kutentha kwa dzuŵa, zilala, moto walupsa, komanso kusefukila kwa madzi. Kutentha kwa m’caka ca 2022, sikudzaiŵalika cifukwa kwawononga zinthu zambili. Anthu ambili amwalila, ndiponso mamiliyoni ambili akusoŵa kokhala.”d
Onani nkhani yakuti “Kutentha Kodetsa Nkhawa Padziko Lonse.”
“Zipolowe.”—Luka 21:9.
Mu 2022, anthu ambili anacita zionetselo zodzudzula boma pokwiya na mavuto azacuma, maka-maka cifukwa ca kukwela kwa mitengo ya zinthu.”e
Onani nkhani yakuti “Kukwela Mitengo kwa Zinthu Padziko Lonse.”
Kodi caka camaŵa kudzakhala zotani?
Palibe angadziŵe kuti m’caka ca 2023 kudzacitika zotani. Koma cimene tikudziŵa mosapeneka konse, n’cakuti posacedwa Ufumu wa Mulungu, kapena kuti boma lakumwamba, lidzalowelelapo pa zocitika za padziko lapansi. (Danieli 2:44) Ndipo bomalo likadzabwela, lidzacotselatu zonse zobweletsa mavuto kwa anthu. Ndipo cifunilo ca Mulungu cidzacitika padziko lapansi.—Mateyu 6:9, 10.
Conco, tikukulimbikitsani kuti mutsatile langizo la Yesu Khristu lakuti “khalani maso,” kuti muone mmene zocitika za padziko lapansi zikukwanilitsila maulosi a m’Baibo. (Maliko 13:37) Tipezeni conde kuti muphunzile zambili za mmene Baibo ingakuthandizileni palipano, komanso mmene ingakupatsileni ciyembekezo ca tsogolo lowala pamodzi na banja lanu.
a AP Nyuzi ya December 8, 2022. “M’caka ca 2022 M’pamene Tsoka la Nkhondo Linabwelelanso ku Europe,” malinga n’kunena kwa Jill Lawless.
b “Njala ya Padziko Lonse,” inalengeza motelo World Food Programme.
c JAMA Health Forum, ya September 22, 2022. “Tikukhala M’nyengo ya Milili—Kunabwela COVID-19, Monkeypox, Polio, cotsatila ni matenda a X,” malinga n’kunena kwa Lawrence O. Gostin, JD.
d Earth.Org, ya October 24, 2022. “Kodi Cikucititsa Kutentha Kosaneneka kwa mu 2022 N’ciyani Maka-maka?” Anafunsa motelo Martina Igini.
e Cikalata Cofuna Mtendele wa Maiko Onse, ca pa December 8, 2022. “Mavuto Azacuma Ndiwo Anacititsa Zionetselo Zokwiyila Maboma Padziko Lonse mu 2022,” malinga n’kunena kwa Thomas Carothers, na Benjamin Feldman.