TheCrimsonMonkey/E+ via Getty Images
Zacilengedwe Zikuwonongeka—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzacitapo Ciyani?
“Kusintha kwa nyengo kukubweletsa mavuto kwa anthu, mizinda na zacilengedwe. Cifukwa ca kusintha kwa nyengo kuopsa kwa mvula zamkuntho kukuwonjezeka, ndipo zikuwononga nyumba komanso zikupangitsa umoyo wa anthu kukhala wovuta padziko lonse. Madzi a m’nyanja zamcele akuyamba kutentha. Izi zikupeleka ciwopsezo cacikulu ku zamoyo m’nyanja, moti zambili zikufa.”—Anatelo Inger Andersen, wacitatu kwa kalembela wamkulu wa bungwe la United Nations amenenso ni mkulu woyang’anila bungwe la UN Environment Programme, pa July 25, 2023.
Kodi maboma angagwilizane kuti athetse mavutowa omwe akukhudza dziko lonse? Kodi angaipezedi njila yothetsela mavutowa?
Baibo imakamba za boma limene lidzakwanitsa kucotsapo mavuto onse okhudza zacilengedwe. Imati “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu,” boma limene lidzalamulila dziko lonse na kuthetsa mavuto onse. (Danieli 2:44) Ufumuwo ukadzayamba kulamulila dziko lonse lapansi, anthu ‘sadzavulazana kapena kuwononga’ dziko lapansi.—Yesaya 11:9.