Kim Steele/The Image Bank via Getty Images
Mavuto a Zacuma—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzacitapo Ciyani?
Zungulile dziko lonse, anthu ambili akhala akuvutika kupeza ndalama zokwanila zogulila zinthu ndipo vutoli likukulila-kulilabe.
Malinga na lipoti lina laposacedwa padziko lonse,a mwezi ulionse ndalama zimene anthu amalandila zimacepela-cepla pa kukwanilitsa zofunikila. Lipotilo linati ngati sipangakhale kusintha kulikonse, ndiye kuti padzakhala kusiyana kwakukulu pakati pa anthu olemela na osauka, komanso umoyo wa mabanja ambili udzakhala wovuta kwambili.
Kodi maboma angakwanitse kuthetsa mavuto a zacuma amene akuculukila-culukilabe?
Baibo imakamba za boma limene lidzakwanitsa kucotsapo mavuto onse a zacuma kuphatikizapo kusiyana pakati pa olemela na osauka. Imati “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu,” boma limene lidzalamulila dziko lonse na kuthetsa mavuto onse. (Danieli 2:44) Ufumuwo ukadzayamba kulamulila dziko lonse lapansi, palibe amene adzaiŵalidwa kapena kunyanyalidwa. (Salimo 9:18) Anthu onse mu Ufumu wa Mulungu adzakhala na zonse zofunikila kuti asangalale na moyo. Iwo adzakondwela na madalitso obwela kaamba ka kulimbika kwawo pa nchito.—Yesaya 65:21, 22.
a International Labour Organization Global Wage Report 2022-23