KHALANI MASO!
Zimene Zingakuthandizeni Kukhalabe Acimwemwe pa Nthawi Zovuta—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
M’nthawi zovuta zino, sitingathe kupewelatu zovuta zonse zimene zingatigwele. Komabe, cimwemwe cathu cimadalila kwambili mmene timaonela zinthu kuposa mmene zinthu zilili. Baibo imakamba kuti “munthu amene ali ndi mtima wosangalala amacita phwando nthawi zonse” mosasamala kanthu za mavuto amene akukumana nawo. (Miyambo 15:15) Kodi tingacite ciyani kuti tionjezele cimwemwe cathu? Onani mmene malangizo a m’Baibo angakuthandizileni.
Kucepetsa nkhawa
Baibo imakamba kuti: “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauwelamitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.”—Miyambo 12:25.
Baibo ingakuthandizeni kucepetsa nkhawa. Kuti muone mmene ingakuthandizileni, welengani nkhani yakuti “Zimene Baibo Imakamba pa Nkhani ya Nkhawa.”
Kucepetsa vuto losowa woceza naye
Baibo imati: “Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.
Baibo ili ndi malangizo amene angatithandize kulimbitsa ubwenzi ndi anthu ena, zimene zingacititse kuti tithetse vuto losowa woceza naye. Welengani nkhani yakuti “Baibo Ingakuthandizeni Kupeza Anzanu Abwino Kuti Muthetse Vuto Losowa Woceza Naye.”
Muzikonda Mulungu komanso anzanu
Baibo imati: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndi maganizo anu onse. . . . Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”a—Mateyo 22:37-39.
Pemphelo lingatithandize kuti tizimukonda kwambili Mulungu. Kuti mudziwe zambili, welengani nkhani yakuti “Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Athu?”
Timaonetsa cikondi kwa ena tikamacita nawo zinthu monga mmene Yesu anakambila. Kuti mudziwe zambili, welengani nkhani yakuti “Kodi Yesu Anapeleka Lamulo Lotani Lokhudza Kucita Zinthu ndi Ena?”
Kodi mungakonde kudziwa zambili za mmene Baibo ingakuthandizileni kukhala ndi cimwemwe pa nthawi zovuta? Ngati n’conco, tikukupemphani kuti muyambe kuphunzila Baibo kwaulele.
a Yehova ndilo dzina la Mulungu. Salimo 83:18.