Citatu, October 8
Sindidzakusiyani.—Aheb. 13:5.
Bungwe Lolamulila lakhala likuphunzitsa mwacindunji owathandiza m’makomiti awo osiyana-siyana. Abale othandiza amenewa akusenza maudindo akulu-akulu mokhulupilika. Iwo aphunzitsidwa bwino kuti apitilize kugwila nchito yosamalila nkhosa za Khristu. Odzozedwa akadzatha onse kutengedwa kupita kumwamba, cakumapeto kwa cisautso cacikulu, kulambila koyela kudzapitilizabe pano padziko lapansi. Ndife oyamikila kuti utsogoleli wa Khristu udzathandiza kuti olambila Mulungu adzapitilize kumulambila mokhulupilika. N’zoona kuti panthawiyo Gogi wa Magogi adzatiukila, amene ni mgwilizano wankhanza wa mitundu. (Ezek. 38:18-20) Koma kutiukila kwa kanthawi kumeneku sikudzapambana; sikudzalepeletsa anthu a Mulungu kulambila Yehova. Iye adzawapulumutsa ndithu! M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona “khamu lalikulu” lomwe ni gulu la nkhosa zina za Khristu. Yohane anauzidwa kuti “khamu lalikulu” limeneli ‘latuluka m’cisautso cacikulu.’ (Chiv. 7:9, 14) Inde, iwo adzatetezedwa! w24.02 5-6 ¶13-14
Cinayi, October 9
Musazimitse moto wa mzimu.—1 Ates. 5:19.
Kodi tingatani kuti tilandile mzimu woyela? Mwa kuupempha, kuŵelenga Mawu a Mulungu ouzilidwa, komanso kugwilizana na gulu limene amalitsogolela na mzimu wake. Tikatelo, timakhala na “makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Mulungu amapatsa mzimu wake anthu okhawo oganiza bwino, komanso a khalidwe loyela. Iye sangapitilize kutipatsa mzimu woyela ngati tikhalabe na maganizo oipa. (1 Ates. 4:7, 8) Kuti tizilandilabe mzimu woyela, tiyenela kupewa ‘kunyoza mawu aulosi.’ (1 Ates. 5:20) Pa lembali, liwu lakuti ‘ulosi’ litanthauza mauthenga ouzilidwa na mzimu wa Mulungu. Aphatikizapo onena za tsiku la Yehova komanso masiku athu ano. Sitikankhila tsikulo kutsogolo, poganiza kuti Aramagedo sidzabwela pamene tili moyo. M’malo mwake, timakhalabe na makhalidwe abwino, komanso kutangwanika na ‘nchito zosonyeza kuti ndife odzipeleka kwa Mulungu.’—2 Pet. 3:11, 12. w23.06 12 ¶13-14
Cisanu, October 10
Kuopa Yehova ndi ciyambi ca nzelu.—Miy. 9:10.
Pokhala Akhristu, kodi tiyenela kucita ciyani zithunzi zamalisece zikaonekela pa cipangizo cathu? Tisaziyang’ane ngakhale pang’ono! Cingatithandize kutelo ni kukumbukila kuti ubale wathu na Yehova ni wamtengo wapatali. Ndipo ngakhale zithunzi zimene si zamalisece kwenikweni zingadzutse cilakolako ca kugonana. N’cifukwa ciyani nazonso tiyenela kuzipewa? Cifukwa sitifuna ngakhale pang’ono kuganizila zocita zaciwelewele. (Mat. 5:28, 29) Mkulu wina ku Thailand dzina lake David anati: “Nimadzifunsa kuti: ‘Olo kuti zithunzi zimenezi si zamalisece kwenikweni, kodi Yehova angakondwele nikapitiliza kuziyang’ana?’ Funso ngati limeneli limanithandiza kucita mwanzelu.” Mantha oyenela oopa kukhumudwitsa Yehova, amatithandiza kucita mwanzelu. Mantha aumulungu otelo ndiwo “ciyambi ca nzelu.” w23.06 23 ¶12-13