LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Ciŵili, October 7

Mukhale ndi khalidwe logwilizana ndi zimene Yehova amafuna.​—Akol. 1:10.

Mu 1919, anthu a Mulungu anamasuka ku Babulo Wamkulu. M’caka cimeneco, “kapolo wokhulupilika komanso wanzelu” anaikidwa kuti athandize anthu oona mtima kuyenda pa “Msewu wa Ciyelo” wamakono. (Mat. 24:45-47; Yes. 35:8) Nchito yokonza msewu umenewo imene amuna okhulupilika anagwila kalelo, ikuthandiza anthu oyenda pa msewu waukuluwo kuti adziŵe zambili zokhudza colinga ca Yehova. (Miy. 4:18) Iwo amathanso kusintha umoyo wawo kuti ugwilizane na miyeso ya Yehova. Yehova sayembekezela anthu ake kupanga masinthidwe onse panthawi imodzi. M’malo mwake, iye wakhala akuyenga anthu ake pang’ono-pang’ono. Tonsefe tidzakhala okondwa panthawi imene zocita zathu zonse zizikondweletsa Mulungu wathu! Kucokela mu 1919, nchito yokonza “Msewu wa Ciyelo” yakhala ikucitika, kuti anthu ambili acoke m’Babulo Wamkulu. w23.05 17 ¶15; 19 ¶16

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Citatu, October 8

Sindidzakusiyani.​—Aheb. 13:5.

Bungwe Lolamulila lakhala likuphunzitsa mwacindunji owathandiza m’makomiti awo osiyana-siyana. Abale othandiza amenewa akusenza maudindo akulu-akulu mokhulupilika. Iwo aphunzitsidwa bwino kuti apitilize kugwila nchito yosamalila nkhosa za Khristu. Odzozedwa akadzatha onse kutengedwa kupita kumwamba, cakumapeto kwa cisautso cacikulu, kulambila koyela kudzapitilizabe pano padziko lapansi. Ndife oyamikila kuti utsogoleli wa Khristu udzathandiza kuti olambila Mulungu adzapitilize kumulambila mokhulupilika. N’zoona kuti panthawiyo Gogi wa Magogi adzatiukila, amene ni mgwilizano wankhanza wa mitundu. (Ezek. 38:18-20) Koma kutiukila kwa kanthawi kumeneku sikudzapambana; sikudzalepeletsa anthu a Mulungu kulambila Yehova. Iye adzawapulumutsa ndithu! M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona “khamu lalikulu” lomwe ni gulu la nkhosa zina za Khristu. Yohane anauzidwa kuti “khamu lalikulu” limeneli ‘latuluka m’cisautso cacikulu.’ (Chiv. 7:9, 14) Inde, iwo adzatetezedwa! w24.02 5-6 ¶13-14

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cinayi, October 9

Musazimitse moto wa mzimu.​—1 Ates. 5:19.

Kodi tingatani kuti tilandile mzimu woyela? Mwa kuupempha, kuŵelenga Mawu a Mulungu ouzilidwa, komanso kugwilizana na gulu limene amalitsogolela na mzimu wake. Tikatelo, timakhala na “makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Mulungu amapatsa mzimu wake anthu okhawo oganiza bwino, komanso a khalidwe loyela. Iye sangapitilize kutipatsa mzimu woyela ngati tikhalabe na maganizo oipa. (1 Ates. 4:7, 8) Kuti tizilandilabe mzimu woyela, tiyenela kupewa ‘kunyoza mawu aulosi.’ (1 Ates. 5:20) Pa lembali, liwu lakuti ‘ulosi’ litanthauza mauthenga ouzilidwa na mzimu wa Mulungu. Aphatikizapo onena za tsiku la Yehova komanso masiku athu ano. Sitikankhila tsikulo kutsogolo, poganiza kuti Aramagedo sidzabwela pamene tili moyo. M’malo mwake, timakhalabe na makhalidwe abwino, komanso kutangwanika na ‘nchito zosonyeza kuti ndife odzipeleka kwa Mulungu.’​—2 Pet. 3:11, 12. w23.06 12 ¶13-14

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani