LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Ciŵelu, August 16

Adzakulimbitsani.​—1 Pet. 5:10.

Kudziunika moona mtima kungakuthandizeni kuti muone pamene muyenela kuongolela, koma musalefuke. “Ambuye ndi wokoma mtima,” ndipo adzakuthandizani kuti muongolele. (1 Pet. 2:3) Mtumwi Petulo anatitsimikizila kuti “Mulungu . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani.” Panthawi ina, Petulo anaziona wosayenela kukhala pamodzi na Mwana wa Mulungu. (Luka 5:8) Koma cifukwa ca thandizo la Yehova komanso la Yesu, anakwanitsa kutsatila Khristu mokhulupilika. Zotsatila zake zinali zakuti Yehova ‘anam’tsegulila khomo kuti aloŵe mwaulemelelo mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.’ (2 Pet. 1:11) Mphoto yosangalatsa zedi! Ngati mwaikilapo mtima mmene Petulo anacitila komanso kulola Yehova kuti akuphunzitseni, inunso mudzalandila mphoto ya moyo wosatha. Ndipo “cikhulupililo canu cidzacititsa kuti miyoyo yanu ipulumuke.”​—1 Pet. 1:9. w23.09 31 ¶16-17

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Sondo, August 17

Lambilani Iye amene anapanga kumwamba, [ndi] dziko lapansi.​—Chiv. 14:7.

Cihema cinali na bwalo lomwe linali locingidwa na mpanda mmene ansembe anali kucitila utumiki wawo. Guwa lansembe lamkuwa lofukizilapo nsembe linali m’bwalo limeneli pamodzi na beseni lamkuwa lomwe ansembe anali kuseŵenzetsa podziyeletsa asanayambe kugwila nchito yawo yopatulika. (Eks. 30:17-20; 40:6-8) Masiku ano, otsalila odzodzedwa a Khristu amatumikila mokhulupilika padziko lapansi m’bwalo lamkati la kacisi wauzimu asanapite kukatumikila monga ansembe na Yesu kumwamba. Beseni la madzi lomwe linali pacihema limakumbutsa odzodzedwa komanso Akhristu onse kuti ayenela kukhala oyela m’makhalidwe komanso mwauzimu. Koma kodi “a khamu lalikulu”, amalambilila kuti? Mtumwi Yohane anawaona “ataimilila pamaso pa mpando wacifumu,” limene ni bwalo lakunja la kacisi wa Yehova, komwe “akumucitila utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kacisi wake.” (Chiv. 7:9, 13-15) Ndife oyamikila ngako kuti tili na malo m’makozedwa a Yehova akulambila koyela! w23.10 28 ¶15-16

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Mande, August 18

Cifukwa ca lonjezo la Mulungu, . . . cikhulupililo cakeco cinamupatsa mphamvu.​—Aroma 4:20.

Njila imodzi imene Yehova amatipatsila mphamvu ni kupitila mwa akulu. (Yes. 32:1, 2) Conco, mukakhala na nkhawa afotokozeleni akulu. Muzilandila thandizo lawo moyamikila. Yehova angakulimbikitseni kupitila mwa iwo. Ciyembekezo cathu cozikika pa Baibo codzakhala m’paradiso pano pa dziko lapansi, kapena cokakhala kumwamba cingatipatse mphamvu. (Aroma 4:3, 18, 19) Ciyembekezo cathu cimeneci cimatilimbikitsa kupilila mavuto, kulalikila uthenga wabwino, komanso kucita mautumiki osiyani-siyani mu mpingo. (1 Ates. 1:3) Ciyembekezo cimeneci n’cimene cinalimbikitsa mtumwi Paulo. Iye ‘anapanikizidwa,’ ‘kuthedwa nzelu,’ ‘kuzunzidwa,’ komanso ‘kugwetsedwa pansi.’ Ndipo moyo wake weniweniwo unali paciopsezo. (2 Akor. 4:8-10) Paulo anapeza mphamvu zopilila mwakuika maganizo pa ciyembekezo cake. (2 Akor. 4:16-18) Iye anaika maganizo ake pa ciyembekezo ca moyo wosafa kumwamba. Paulo anali kusinkhasinkha za ciyembekezo cimeneco. Conco anayamba kudziona kuti “akucititsidwa kukhala watsopano tsiku ndi tsiku.” w23.10 15-16 ¶14-17

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani