LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Cisanu, August 15

Iye . . . anadzipatula, cifukwa ankaopa anthu odulidwawo.​—Agal. 2:12.

Ngakhale pambuyo pokhala Mkhristu wodzozedwa, mtumwi Petulo anali kulimbanabe na zifooko zake. Mu 36 C.E, Petulo anaona kamaso pamene Koneliyo, munthu wosadulidwa, anadzozedwa na mzimu woyela. Uwu unali umboni woonekelatu wakuti “Mulungu alibe tsankho,” komanso kuti anthu amitundu ina angakhale mu mpingo wacikhristu. (Mac. 10:34, 44, 45) Pambuyo pa izi, Petulo anali womasuka kudyela pamodzi na anthu a mitundu ina, zimene kumbuyoku sakanacita. Komabe, Akhristu ena aciyuda anali kuona kuti Ayuda na anthu amitundu ina sayenela kudyela pamodzi. Ayuda ena atafika ku Antiokeya, Petulo analeka kudya na Akhristu a mitundu ina, mwina poopa kukhumudwitsa Akhristu aciyuda. Mtumwi Paulo anaona kuti cimeneco n’cinyengo. Conco, anam’dzudzula pamaso pa anthu. (Agal. 2:13, 14) Ngakhale kuti Petulo anaphonyetsanso, sanabwelele m’mbuyo. w23.09 22 ¶8

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵelu, August 16

Adzakulimbitsani.​—1 Pet. 5:10.

Kudziunika moona mtima kungakuthandizeni kuti muone pamene muyenela kuongolela, koma musalefuke. “Ambuye ndi wokoma mtima,” ndipo adzakuthandizani kuti muongolele. (1 Pet. 2:3) Mtumwi Petulo anatitsimikizila kuti “Mulungu . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani.” Panthawi ina, Petulo anaziona wosayenela kukhala pamodzi na Mwana wa Mulungu. (Luka 5:8) Koma cifukwa ca thandizo la Yehova komanso la Yesu, anakwanitsa kutsatila Khristu mokhulupilika. Zotsatila zake zinali zakuti Yehova ‘anam’tsegulila khomo kuti aloŵe mwaulemelelo mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.’ (2 Pet. 1:11) Mphoto yosangalatsa zedi! Ngati mwaikilapo mtima mmene Petulo anacitila komanso kulola Yehova kuti akuphunzitseni, inunso mudzalandila mphoto ya moyo wosatha. Ndipo “cikhulupililo canu cidzacititsa kuti miyoyo yanu ipulumuke.”​—1 Pet. 1:9. w23.09 31 ¶16-17

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Sondo, August 17

Lambilani Iye amene anapanga kumwamba, [ndi] dziko lapansi.​—Chiv. 14:7.

Cihema cinali na bwalo lomwe linali locingidwa na mpanda mmene ansembe anali kucitila utumiki wawo. Guwa lansembe lamkuwa lofukizilapo nsembe linali m’bwalo limeneli pamodzi na beseni lamkuwa lomwe ansembe anali kuseŵenzetsa podziyeletsa asanayambe kugwila nchito yawo yopatulika. (Eks. 30:17-20; 40:6-8) Masiku ano, otsalila odzodzedwa a Khristu amatumikila mokhulupilika padziko lapansi m’bwalo lamkati la kacisi wauzimu asanapite kukatumikila monga ansembe na Yesu kumwamba. Beseni la madzi lomwe linali pacihema limakumbutsa odzodzedwa komanso Akhristu onse kuti ayenela kukhala oyela m’makhalidwe komanso mwauzimu. Koma kodi “a khamu lalikulu”, amalambilila kuti? Mtumwi Yohane anawaona “ataimilila pamaso pa mpando wacifumu,” limene ni bwalo lakunja la kacisi wa Yehova, komwe “akumucitila utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kacisi wake.” (Chiv. 7:9, 13-15) Ndife oyamikila ngako kuti tili na malo m’makozedwa a Yehova akulambila koyela! w23.10 28 ¶15-16

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani