Cisanu, August 1
Mavuto a munthu wolungama ndi ambili, koma Yehova amamupulumutsa ku mavuto onsewo.—Sal. 34:19.
Onani mfundo ziŵili izi zimene zili pa salimo lili pamwambapa: (1) Anthu olungama amakumana na mavuto. (2) Yehova amatipulumutsa ku mavutowo. Kodi amatipulumutsa bwanji? Njila imodzi ni kutithandiza kuona umoyo moyenela m’dzikoli. N’zoona kuti Yehova anatilonjeza kuti tidzakhala acimwemwe pom’tumikila. Koma sanatiuze kuti palipano tidzakhala na umoyo wopanda mavuto. (Yes. 66:14) Iye amatilimbikitsa kuganizila za tsogolo lathu, pamene tidzasangalala na moyo kwamuyaya. (2 Akor. 4:16-18) Koma pakali pano, iye amatithandiza kuti tisaleke kum’tumikila. (Maliro 3:22-24) Tiphunzilapo ciyani pa zitsanzo za alambili a Yehova okhulupilika ochulidwa m’Baibo, komanso amakono? Tingakumane na mavuto mosayembekezela. Koma tikam’dalila Yehova, sadzalephela kutithandiza.—Sal. 55:22. w23.04 14-15 ¶3-4
Ciŵelu, August 2
[Muzimvela] olamulila akulu-akulu.—Aroma 13:1.
Tingatengele citsanzo ca Yosefe na Mariya amene anali okonzeka kumvela olamulila ngakhale pamene cinali covuta kutelo. (Luka 2:1-6) Mariya atatsala pang’ono kubeleka, boma linapeleka lamulo limene likanapangitsa kuti zikhale zovuta kwa iye na Yosefe kulitsatila. Bwanamkubwa waciroma, dzina Augusito, analamula kuti nzika zonse za ufumuwo zipite ku mizinda yakwawo kukalembetsa m’kaundula. Yosefe na Mariya anafunika kupita ku Betelehemu, ulendo wodutsa m’mapili wa makilomita 150. Ulendowu unali wosautsa maka-maka kwa Mariya. N’kutheka kuti iwo analinso kudela nkhawa za umoyo wa Mariya komanso za mwana wosabadwayo. Mwina iwo anadzifunsa kuti, bwanji ngati nthawi yobeleka yakwana pamene tikali paulendowu? Nkhawa yawo inali yomveka cifukwa mwana wobadwayo anali kudzakhala Mesiya wolonjezedwa na Yehova. Kodi zifukwa zimenezi zinawacititsa kuti asamvele lamulo la boma? Yosefe na Mariya sanalole kuti zimenezo ziwalepheletse kutsatila lamulo la boma. Yehova anawadalitsa cifukwa ca kumvela kwawo. Mariya anafika bwino ku Betelehemu, anabeleka mwana wathanzi, ndipo anathandiza kukwanilitsa ulosi wa m’Baibo.—Mika 5:2. w23.10 8 ¶9; 9 ¶11-12
Sondo, August 3
Tiyeni tilimbikitsane.—Aheb. 10:25.
Koma bwanji ngati mumacita mantha kupelekapo ndemanga pa misonkhano? Mungapindule kwambili mukamakonzekela bwino. (Miy. 21:5) Mukaimvetsa bwino nkhani imene mudzaphunzila, cidzakhala cosavuta kukapelekapo ndemanga pamsonkhano. Cina, mayankho anu azikhala aafupi. (Miy. 15:23; 17:27) Yankho lanu likakhala lalifupi simudzadodoma kwambili. Mukapeleka ndemanga yaifupi m’mawu anu-anu, zidzaonetsa kuti munakonzekela bwino, komanso kuti munaimvetsa bwino nkhaniyo. Bwanji ngati mwayesa kutsatila malingalilo amenewa, koma mukucitabe mantha kupelekapo ndemanga kaŵili kapena kuposapo? Dziŵani kuti Yehova amayamikila kwambili kuyesetsa kwanu. (Luka 21:1-4) Iye satipempha kucita zimene sitingakwanitse. (Afil. 4:5) Conco, dziŵani zimene mungathe kucita, dziikileni colinga cocita zimenezo, ndipo pemphelani kuti mukhale wodekha. Colingaco cingakhale kukapeleka ndemanga imodzi yaifupi. w23.04 21 ¶6-8