LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Cinayi, July 31

Nthawi zonse muzitsimikizila kuti covomelezeka kwa Ambuye nʼciti.​—Aef. 5:10.

Tikafunika kupanga cisankho cofunika kwambili, tiyenela “kuzindikila cifunilo ca Yehova,” na kucita zinthu mogwilizana na cifuniloco. (Aef. 5:17) Tikamafufuza na kupeza mfundo za m’Baibo zothandiza pa cisankho cimene tifuna kupanga, kwenikweni timakhala tikufunafuna maganizo a Mulungu pa nkhaniyo. Ndipo tikagwilitsa nchito mfundo zake, timapanga zisankho zabwino. Mdani wathu Satana, “Woipayo,” amafuna kuticenjeneka na kufuna-funa zinthu za m’dzikoli n’colinga cakuti tizisoŵelatu nthawi yotumikila Mulungu. (1 Yoh. 5:19) Cingakhale capafupi kwa Mkhristu kutsogoza zakuthupi, maphunzilo, kapena nchito m’malo moseŵenzetsa mipata imene ilipo yotumikila Yehova. Zotelezi zikacitika, zingaonetse kuti munthu wayamba kuyendela maganizo a m’dzikoli. N’zoona kuti zinthu zimenezi si zoipa kwenikweni. Koma si ndiye zomwe tiyenela kutsogoza pa umoyo wathu. w24.03 24 ¶16-17

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cisanu, August 1

Mavuto a munthu wolungama ndi ambili, koma Yehova amamupulumutsa ku mavuto onsewo.​—Sal. 34:19.

Onani mfundo ziŵili izi zimene zili pa salimo lili pamwambapa: (1) Anthu olungama amakumana na mavuto. (2) Yehova amatipulumutsa ku mavutowo. Kodi amatipulumutsa bwanji? Njila imodzi ni kutithandiza kuona umoyo moyenela m’dzikoli. N’zoona kuti Yehova anatilonjeza kuti tidzakhala acimwemwe pom’tumikila. Koma sanatiuze kuti palipano tidzakhala na umoyo wopanda mavuto. (Yes. 66:14) Iye amatilimbikitsa kuganizila za tsogolo lathu, pamene tidzasangalala na moyo kwamuyaya. (2 Akor. 4:16-18) Koma pakali pano, iye amatithandiza kuti tisaleke kum’tumikila. (Maliro 3:22-24) Tiphunzilapo ciyani pa zitsanzo za alambili a Yehova okhulupilika ochulidwa m’Baibo, komanso amakono? Tingakumane na mavuto mosayembekezela. Koma tikam’dalila Yehova, sadzalephela kutithandiza.​—Sal. 55:22. w23.04 14-15 ¶3-4

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵelu, August 2

[Muzimvela] olamulila akulu-akulu.​—Aroma 13:1.

Tingatengele citsanzo ca Yosefe na Mariya amene anali okonzeka kumvela olamulila ngakhale pamene cinali covuta kutelo. (Luka 2:1-6) Mariya atatsala pang’ono kubeleka, boma linapeleka lamulo limene likanapangitsa kuti zikhale zovuta kwa iye na Yosefe kulitsatila. Bwanamkubwa waciroma, dzina Augusito, analamula kuti nzika zonse za ufumuwo zipite ku mizinda yakwawo kukalembetsa m’kaundula. Yosefe na Mariya anafunika kupita ku Betelehemu, ulendo wodutsa m’mapili wa makilomita 150. Ulendowu unali wosautsa maka-maka kwa Mariya. N’kutheka kuti iwo analinso kudela nkhawa za umoyo wa Mariya komanso za mwana wosabadwayo. Mwina iwo anadzifunsa kuti, bwanji ngati nthawi yobeleka yakwana pamene tikali paulendowu? Nkhawa yawo inali yomveka cifukwa mwana wobadwayo anali kudzakhala Mesiya wolonjezedwa na Yehova. Kodi zifukwa zimenezi zinawacititsa kuti asamvele lamulo la boma? Yosefe na Mariya sanalole kuti zimenezo ziwalepheletse kutsatila lamulo la boma. Yehova anawadalitsa cifukwa ca kumvela kwawo. Mariya anafika bwino ku Betelehemu, anabeleka mwana wathanzi, ndipo anathandiza kukwanilitsa ulosi wa m’Baibo.​—Mika 5:2. w23.10 8 ¶9; 9 ¶11-12

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani