Ciŵili, August 19
Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu. Yehova adzadalitsa anthu ake powapatsa mtendele.—Sal. 29:11.
Mukamapemphela, muyenela kuganizila ngati ni nthawi yoyenela kuti Yehova ayankhe pemphelo lanu. Nthawi zina tingaone kuti tifunikila yankho lam’mangu-m’mangu pa pemphelo lathu. Koma Yehova ndiye amadziŵa bwino nthawi yoyenela kutiyankha. (Aheb. 4:16) Ngati nthawi yomweyo sitinalandile zimene tapempha, tingaganize kuti yankho la Yehova n’lakuti ‘Iyai.’ Koma yankho lake m’ceni-ceni lingakhale lakuti ‘Osati pali pano.’ Mwacitsanzo, m’bale wacinyamata wina anapempha kuti acilitsidwe matenda ake. Koma sanacile. Ngati Yehova mozizwitsa akanam’cilitsa m’baleyo, Satana akanati m’baleyo anapitiliza kutumikila Yehova cifukwa cakuti anam’cilitsa. (Yobu 1:9-11; 2:4) Kuwonjezela apo, Yehova anaikilatu kale nthawi pamene adzacotselatu matenda onse. (Yes. 33:24; Chiv. 21:3, 4) Koma pakali pano, tisayembekezele kucilitsidwa mozizwitsa. Conco m’baleyo angapemphe Yehova kuti am’patse mphamvu komanso mtendele wa mumtima, kuti apilile matendawo na kupitiliza kumutumikila mokhulupilika. w23.11 24 ¶13
Citatu, August 20
Sanaticitile mogwilizana ndi macimo athu, kapena kutipatsa cilango cogwilizana ndi zolakwa zathu.—Sal. 103:10.
Ngakhale kuti Samisoni anapanga colakwa cacikulu, sanafooke. Iye anali kufuna-funa mpata kuti akwanilitse nchito imene Mulungu anamupatsa yogonjetsa Afilisiti. (Ower. 16:28-30) Iye anacondelela Yehova kuti: “Ndiloleni ndiwabwezele Afilisitiwa.” Mulungu woona anayankha pemphelo la Samisoni pobwezeletsa mphamvu zake zapadela. Conco pa tsikulo Samisoni anapha Afilisiti ambili kuposa amene anawapha mu umoyo wake wonse. Ngakhale kuti Samisoni anakumana na mavuto aakulu cifukwa ca colakwa cake, iye sanaleke kuyesetsa kucita cifunilo ca Yehova. Nafenso tikalakwitsa zina zake, kenako n’kudzudzulidwa kapena kucotsedwa paudindo, sitiyenela kuleka kuyesetsa kucita cifunilo ca Yehova. Musaiŵale kuti Yehova ni okonzeka kutikhululukila. (Sal. 103:8, 9) Monga zinalili kwa Samisoni, nafenso Yehova angadzapitilize kutigwilitsa nchito ngakhale titalakwitsa zina zake. w23.09 6 ¶15-16
Cinayi, August 21
Kupilila kumacititsa kuti tikhale ovomelezeka kwa Mulungu ndipo kukhala ovomelezeka kwa Mulungu kumacititsa kuti tikhale ndi ciyembekezo.—Aroma 5:4.
Kupilila kwanu kungacititse kuti mukhale ovomelezeka kwa Yehova. Izi sizitanthauza kuti Yehova amakondwela mukamakumana na mavuto ayi. M’malo mwake amakondwela kuti mwakwanitsa kupilila mokhulupilika. N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti tikapilila timakondweletsa Yehova! (Sal. 5:12) Kumbukilani kuti Abulahamu anapilila mayeso, ndipo pothela pake anayanjidwa na Mulungu. Anakhala bwenzi la Yehova, ndipo anaonedwa wolungama. (Gen. 15:6; Aroma 4:13, 22) Zingakhalenso cimodzi-modzi kwa ife. Mulungu satiyanja cifukwa ca kuculuka kwa nchito zimene timacita mu utumiki wake, kapena maudindo amene tili nawo. M’malo mwake, amatiyanja cifukwa ca kupilila kwathu mokhulupilika. Tonsefe tingakwanitse kupilila mosasamala kanthu za msinkhu wathu, mikhalidwe yathu, na maluso athu. Kodi mukupilila mokhulupilika mayeso ena ake pali pano? Ngati n’telo, pezani citonthozo podziŵa kuti Mulungu akusangalala nanu. Kudziŵa zimenezi kumalimbikitsa ciyembekezo cathu. w23.12 11 ¶13-14