LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Citatu, August 20

Sanaticitile mogwilizana ndi macimo athu, kapena kutipatsa cilango cogwilizana ndi zolakwa zathu.​—Sal. 103:10.

Ngakhale kuti Samisoni anapanga colakwa cacikulu, sanafooke. Iye anali kufuna-funa mpata kuti akwanilitse nchito imene Mulungu anamupatsa yogonjetsa Afilisiti. (Ower. 16:28-30) Iye anacondelela Yehova kuti: “Ndiloleni ndiwabwezele Afilisitiwa.” Mulungu woona anayankha pemphelo la Samisoni pobwezeletsa mphamvu zake zapadela. Conco pa tsikulo Samisoni anapha Afilisiti ambili kuposa amene anawapha mu umoyo wake wonse. Ngakhale kuti Samisoni anakumana na mavuto aakulu cifukwa ca colakwa cake, iye sanaleke kuyesetsa kucita cifunilo ca Yehova. Nafenso tikalakwitsa zina zake, kenako n’kudzudzulidwa kapena kucotsedwa paudindo, sitiyenela kuleka kuyesetsa kucita cifunilo ca Yehova. Musaiŵale kuti Yehova ni okonzeka kutikhululukila. (Sal. 103:8, 9) Monga zinalili kwa Samisoni, nafenso Yehova angadzapitilize kutigwilitsa nchito ngakhale titalakwitsa zina zake. w23.09 6 ¶15-16

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cinayi, August 21

Kupilila kumacititsa kuti tikhale ovomelezeka kwa Mulungu ndipo kukhala ovomelezeka kwa Mulungu kumacititsa kuti tikhale ndi ciyembekezo.​—Aroma 5:4.

Kupilila kwanu kungacititse kuti mukhale ovomelezeka kwa Yehova. Izi sizitanthauza kuti Yehova amakondwela mukamakumana na mavuto ayi. M’malo mwake amakondwela kuti mwakwanitsa kupilila mokhulupilika. N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti tikapilila timakondweletsa Yehova! (Sal. 5:12) Kumbukilani kuti Abulahamu anapilila mayeso, ndipo pothela pake anayanjidwa na Mulungu. Anakhala bwenzi la Yehova, ndipo anaonedwa wolungama. (Gen. 15:6; Aroma 4:13, 22) Zingakhalenso cimodzi-modzi kwa ife. Mulungu satiyanja cifukwa ca kuculuka kwa nchito zimene timacita mu utumiki wake, kapena maudindo amene tili nawo. M’malo mwake, amatiyanja cifukwa ca kupilila kwathu mokhulupilika. Tonsefe tingakwanitse kupilila mosasamala kanthu za msinkhu wathu, mikhalidwe yathu, na maluso athu. Kodi mukupilila mokhulupilika mayeso ena ake pali pano? Ngati n’telo, pezani citonthozo podziŵa kuti Mulungu akusangalala nanu. Kudziŵa zimenezi kumalimbikitsa ciyembekezo cathu. w23.12 11 ¶13-14

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cisanu, August 22

Iweyo ucite zinthu mwamphamvu.​—1 Maf. 2:2.

Mwamuna wacikhristu ayenela kuphunzila kukamba bwino na ena. Mwamuna amene amakamba bwino na ena amamvetsela zimene ena akunena ndipo amazindikila mmene akumvela. (Miy. 20:5) Amamvetsa mmene ena akumvela poona mmene akulankhulila, komanso magesica amene akupanga polankhula. Simungakwanitse kucita zimenezi ngati simupatula nthawi yoceza na anthu. Ngati nthawi zambili mumaceza na anthu pa mameseji, simungakulitse luso lanu lokambilana na anthu pamaso-m’pamaso. Conco, muzipeza mipata yokambilana na anthu pamaso-m’pamaso. (2 Yoh. 12) Mkhristu wokhwima ayenela kudzisamalila komanso kusamalila a m’banja lake. (1 Tim. 5:8) M’pofunikila kuphunzila luso lina lake limene lingakuthandizeni kupeza nchito. (Mac. 18:2, 3; 20:34; Aef. 4:28) Muzidziŵika kuti ndinu munthu wakhama pa nchito, amene amayamba nchito na kuimalizitsa. Mukatelo, mudzapeza nchito na kukhalitsa pa nchitoyo. w23.12 27 ¶12-13

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani