Cisanu, August 22
Iweyo ucite zinthu mwamphamvu.—1 Maf. 2:2.
Mwamuna wacikhristu ayenela kuphunzila kukamba bwino na ena. Mwamuna amene amakamba bwino na ena amamvetsela zimene ena akunena ndipo amazindikila mmene akumvela. (Miy. 20:5) Amamvetsa mmene ena akumvela poona mmene akulankhulila, komanso magesica amene akupanga polankhula. Simungakwanitse kucita zimenezi ngati simupatula nthawi yoceza na anthu. Ngati nthawi zambili mumaceza na anthu pa mameseji, simungakulitse luso lanu lokambilana na anthu pamaso-m’pamaso. Conco, muzipeza mipata yokambilana na anthu pamaso-m’pamaso. (2 Yoh. 12) Mkhristu wokhwima ayenela kudzisamalila komanso kusamalila a m’banja lake. (1 Tim. 5:8) M’pofunikila kuphunzila luso lina lake limene lingakuthandizeni kupeza nchito. (Mac. 18:2, 3; 20:34; Aef. 4:28) Muzidziŵika kuti ndinu munthu wakhama pa nchito, amene amayamba nchito na kuimalizitsa. Mukatelo, mudzapeza nchito na kukhalitsa pa nchitoyo. w23.12 27 ¶12-13
Ciŵelu, August 23
Tsiku la Yehova lidzabwela ndendende ngati wakuba usiku.—1 Ates. 5:2.
M’Baibo mawu akuti “tsiku la Yehova” amakamba za nthawi pamene Yehova adzawononga adani ake na kupulumutsa anthu ake. Kalelo, Yehova anaonetsapo zakuda mitundu ina. (Yes. 13:1, 6; Ezek. 13:5; Zef. 1:8) M’masiku athu ano, “tsiku la Yehova” lidzayamba na kuukilidwa kwa Babulo Wamkulu, ndipo lidzatha na nkhondo ya Aramagedo. Kuti tikapulumuke pa ‘tsikulo,’ tiyenela kukonzekela palipano. Yesu anati “khalani okonzeka” kaamba ka “cisautso cacikulu.” Izi zitanthauza kuti tiyenela kukhalabe okonzeka. (Mat. 24:21; Luka 12:40) M’kalata yake yoyamba youzilidwa yopita kwa Atesalonika, mtumwi Paulo anagwilitsa nchito mafanizo angapo pothandiza Akhristu kukhalabe okonzeka tsiku lalikulu la Yehova laciweluzo. Paulo anadziŵa kuti tsiku la Yehova silidzafika panthawi imeneyo. (2 Ates. 2:1-3) Ngakhale n’telo, iye analimbikitsa Akhristu anzake kukonzekela tsikulo ngati kuti lidzabwela maŵa. Nafenso tiyenela kuseŵenzetsa uphungu umenewo. w23.06 8 ¶1-2
Sondo, August 24
Abale anga okondedwa, khalani olimba, ndiponso osasunthika.—1 Akor. 15:58.
Mu 1978, nyumba yaitali ya nsanjika 60 inamangidwa mu mzinda wa Tokyo, ku Japan. Anthu anali kudzifunsa ngati nyumbayo idzapilila zivomezi zimene zinali kucitika pafupi-pafupi mu mzindawo. Kodi cinsinsi cake cinali ciyani? Akatswili anaimanga m’njila yakuti ikhale yolimba, koma panthawi imodzimodzi kuti ikhale yofeŵa kukacitika civomezi. Akhristu ali monga nyumba ya nsanjika imeneyo. Motani? Mkhristu ayenela kukhala wosasunthika. Koma ayenelanso kukhala wofeŵa kapena kuti wokonzeka kusintha. Ayenela kukhala wolimba komanso wosasunthika pa kumvela malamulo na miyeso ya Yehova. Iye ni ‘wokonzeka kumvela’ nthawi zonse. Kumbali ina, ayenela kukhala ‘wololela’ kapena kuti wokonzeka kusintha pakafunika kutelo. (Yak. 3:17) Mkhristu amene amaona zinthu mwa njila imeneyi amapewa kukhwimitsa kwambili zinthu, kapena kukhala wololela mopitilila malile. w23.07 14 ¶1-2