Ciŵelu, August 23
Tsiku la Yehova lidzabwela ndendende ngati wakuba usiku.—1 Ates. 5:2.
M’Baibo mawu akuti “tsiku la Yehova” amakamba za nthawi pamene Yehova adzawononga adani ake na kupulumutsa anthu ake. Kalelo, Yehova anaonetsapo zakuda mitundu ina. (Yes. 13:1, 6; Ezek. 13:5; Zef. 1:8) M’masiku athu ano, “tsiku la Yehova” lidzayamba na kuukilidwa kwa Babulo Wamkulu, ndipo lidzatha na nkhondo ya Aramagedo. Kuti tikapulumuke pa ‘tsikulo,’ tiyenela kukonzekela palipano. Yesu anati “khalani okonzeka” kaamba ka “cisautso cacikulu.” Izi zitanthauza kuti tiyenela kukhalabe okonzeka. (Mat. 24:21; Luka 12:40) M’kalata yake yoyamba youzilidwa yopita kwa Atesalonika, mtumwi Paulo anagwilitsa nchito mafanizo angapo pothandiza Akhristu kukhalabe okonzeka tsiku lalikulu la Yehova laciweluzo. Paulo anadziŵa kuti tsiku la Yehova silidzafika panthawi imeneyo. (2 Ates. 2:1-3) Ngakhale n’telo, iye analimbikitsa Akhristu anzake kukonzekela tsikulo ngati kuti lidzabwela maŵa. Nafenso tiyenela kuseŵenzetsa uphungu umenewo. w23.06 8 ¶1-2
Sondo, August 24
Abale anga okondedwa, khalani olimba, ndiponso osasunthika.—1 Akor. 15:58.
Mu 1978, nyumba yaitali ya nsanjika 60 inamangidwa mu mzinda wa Tokyo, ku Japan. Anthu anali kudzifunsa ngati nyumbayo idzapilila zivomezi zimene zinali kucitika pafupi-pafupi mu mzindawo. Kodi cinsinsi cake cinali ciyani? Akatswili anaimanga m’njila yakuti ikhale yolimba, koma panthawi imodzimodzi kuti ikhale yofeŵa kukacitika civomezi. Akhristu ali monga nyumba ya nsanjika imeneyo. Motani? Mkhristu ayenela kukhala wosasunthika. Koma ayenelanso kukhala wofeŵa kapena kuti wokonzeka kusintha. Ayenela kukhala wolimba komanso wosasunthika pa kumvela malamulo na miyeso ya Yehova. Iye ni ‘wokonzeka kumvela’ nthawi zonse. Kumbali ina, ayenela kukhala ‘wololela’ kapena kuti wokonzeka kusintha pakafunika kutelo. (Yak. 3:17) Mkhristu amene amaona zinthu mwa njila imeneyi amapewa kukhwimitsa kwambili zinthu, kapena kukhala wololela mopitilila malile. w23.07 14 ¶1-2
Mande, August 25
Ngakhale kuti Khristuyo simunamuonepo, mumamukonda.—1 Pet. 1:8.
Yesu analimbana na mayeselo osiyanasiyana ocokela kwa Satana, kuphatikizapo ciyeso comuuza mwacindunji kuti aleke kukhala wokhulupilika kwa Mulungu. (Mat. 4:1-11) Satana anali wotsimikiza mtima kucimwitsa Yesu kuti asathe kupeleka dipo. Yesu anakumananso na mayeso ena pocita utumiki wake pa dziko lapansi. Anazunzidwa, ndipo moyo wake unali paciopsezo. (Luka 4:28, 29; 13:31) Anali kupililanso zophophonya za otsatila ake. (Maliko 9:33, 34) Pozengedwa mlandu kuti aphedwe, anazunzidwa na kunyozedwa. Ndipo anaphedwa m’njila yoŵaŵa komanso yonyazitsa kwambili. (Aheb. 12:1-3) Anapilila yekha mavuto othela popanda Yehova kum’teteza. (Mat. 27:46) Kunena zoona, Yesu anavutika zedi kuti apeleke dipo. Ndipo tikaganizila zinthu zimene Yesu anapitamo modzipeleka kaamba ka ife, cikondi cathu pa iye cimakula. w24.01 10-11 ¶7-9