LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso citundu cina: Shan
  • Lelo

Cinayi, August 28

Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana, onse amene amamuitana mʼcoonadi.​—Sal. 145:18.

Yehova, “Mulungu amene ndi wacikondi,” ali nafe! (2 Akor. 13:11) Iye amationetsa cidwi aliyense payekha-payekha. Ndife otsimikiza kuti ndife ‘otetezeka ndi cikondi Cake cokhulupilika.’ (Sal. 32:10) Tikapitiliza kusinkhasinkha za mmene iye waonetsela cikondi cake pa ife, m’pamene iyenso amakhala weniweni kwa ife. Ndipo timamva kuti tikuyandikana naye. Tingamufikile momasuka na kumuuza kufunika kwa cikondi cake kwa ife. Tingamufotokozele nkhawa zathu zonse tili na cidalilo kuti amatimvetsa, komanso kuti ni wofunitsitsa kutithandiza. (Sal. 145:19) Monga mmene timafunila moto kukazizila, tifunikilanso cikondi ca Yehova. Ngakhale kuti cikondi ca Yehova n’camphamvu, cimapelekedwa mokoma mtima. Conco muzikhala wosangalala podziŵa kuti Yehova amakukondani kwambili. Ndipo tonsefe tiyeni tinene mofuula za cikondi cake kuti: “Ndimakonda Yehova”!​—Sal. 116:1. w24.01 31 ¶19-20

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cisanu, August 29

Ine ndacititsa kuti iwo adziŵe dzina lanu.​—Yoh. 17:26

Yesu anacita zambili kuposa kungouza anthu kuti dzina la Mulungu ni Yehova. Ayuda omwe Yesu anali kuphunzitsa anali kulidziŵa kale dzina la Mulungu. Koma Yesu anakhala patsogolo ‘kuwafotokozela za Mulungu.’ (Yoh. 1:17, 18) Mwa citsanzo, Malemba a Ciheberi amaonetsa kuti Yehova ni wacifundo, komanso wacisomo. (Eks. 34:5-7) Yesu anafotokoza coonadi cimeneci momveka bwino pomwe anakamba za fanizo la mwana woloŵelela. Bambo wa m’fanizoli ataona mwana wake wolapa “ali capatali ndithu,” anathamangila mwanayo, kumukumbatila na kum’khululukila na mtima wonse. Zimenezi zimatithandiza kumvetsa bwino cifundo ca Yehova na cisomo cake. (Luka 15:11-32) Yesu anathandiza ena kumvetsa kuti Yehova ni Tate wotani kwenikweni. w24.02 10 ¶8-9

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵelu, August 30

[Tonthozani ena] . . . cifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.​—2 Akor. 1:4.

Yehova amatsitsimula komanso kutonthoza opsinjika maganizo. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova ca kumvela ena cifundo komanso kuwatonthoza? Njila imodzi imene tingacitile zimenezi ni kukulitsa makhalidwe abwino mu mtima mwathu amene angatithandize kutonthoza ena. Kodi ena mwa makhalidwe amenewa ni ati? N’ciyani cingatithandize kukhalabe na cikondi kuti “tipitilize kutonthozana” tsiku na tsiku? (1 Ates. 4:18)Tiyenela kukhala na makhalidwe monga kumvela ena cisoni, kukonda abale, komanso kukhala okoma mtima. (Akol. 3:12; 1 Pet. 3:8) Kodi makhalidwewa adzatithandiza bwanji? Ngati tipanga cifundo na makhalidwe ena otelo kukhala mbali ya umunthu wathu, sicidzakhala covuta kutonthoza amene akuvutika. Yesu anakamba kuti, “pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’cuma cake cabwino.” (Mat. 12:34, 35) Kutonthoza abale na alongo amene akukumana na zovuta ni njila yaikulu imene timaonetsela kuti timawakonda. w23.11 10 ¶10-11

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani