Citatu, August 27
Ndimaona lamulo lina mʼthupi langa likumenyana ndi malamulo amʼmaganizo mwanga nʼkundicititsa kukhala kapolo wa lamulo la ucimo limene lili mʼthupi langa.—Aroma 7:23.
Ngati mungalefuke poona kuti mumakhala na zilakolako zoipa, kuganizila lonjezo limene munapeleka kwa Yehova podzipatulila kudzakuthandizani kutsimikiza mtima kugonjetsa mayeselo. Ndipo zoona zake n’zakuti lumbilo lanu la kudzipatulila lidzakuthandizani kugonjetsa mayeselo. Motani? Mukadzipatulila kwa Yehova mumadzikana nokha. Izi zikutanthauza kunena kuti toto ku zikhumbo zanu, na zolinga zanu zimene sizingakondweletse Yehova. (Mat. 16:24) Conco, mukakumana na mayeso simudzacedwa na kuganizilapo zimene muyenela kucita. Mudzakhala mutadziwilatu zocita, zomwe ni kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Mudzakhalabe wosasunthika pa kukondweletsa Yehova. Mudzakhala ngati Yobu amene ngakhale pambuyo pokumana na mavuto aakulu ananena motsimikiza kuti: “Sindidzasiya kukhala wokhulupilika.”—Yobu 27:5. w24.03 9 ¶6-7
Cinayi, August 28
Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana, onse amene amamuitana mʼcoonadi.—Sal. 145:18.
Yehova, “Mulungu amene ndi wacikondi,” ali nafe! (2 Akor. 13:11) Iye amationetsa cidwi aliyense payekha-payekha. Ndife otsimikiza kuti ndife ‘otetezeka ndi cikondi Cake cokhulupilika.’ (Sal. 32:10) Tikapitiliza kusinkhasinkha za mmene iye waonetsela cikondi cake pa ife, m’pamene iyenso amakhala weniweni kwa ife. Ndipo timamva kuti tikuyandikana naye. Tingamufikile momasuka na kumuuza kufunika kwa cikondi cake kwa ife. Tingamufotokozele nkhawa zathu zonse tili na cidalilo kuti amatimvetsa, komanso kuti ni wofunitsitsa kutithandiza. (Sal. 145:19) Monga mmene timafunila moto kukazizila, tifunikilanso cikondi ca Yehova. Ngakhale kuti cikondi ca Yehova n’camphamvu, cimapelekedwa mokoma mtima. Conco muzikhala wosangalala podziŵa kuti Yehova amakukondani kwambili. Ndipo tonsefe tiyeni tinene mofuula za cikondi cake kuti: “Ndimakonda Yehova”!—Sal. 116:1. w24.01 31 ¶19-20
Cisanu, August 29
Ine ndacititsa kuti iwo adziŵe dzina lanu.—Yoh. 17:26
Yesu anacita zambili kuposa kungouza anthu kuti dzina la Mulungu ni Yehova. Ayuda omwe Yesu anali kuphunzitsa anali kulidziŵa kale dzina la Mulungu. Koma Yesu anakhala patsogolo ‘kuwafotokozela za Mulungu.’ (Yoh. 1:17, 18) Mwa citsanzo, Malemba a Ciheberi amaonetsa kuti Yehova ni wacifundo, komanso wacisomo. (Eks. 34:5-7) Yesu anafotokoza coonadi cimeneci momveka bwino pomwe anakamba za fanizo la mwana woloŵelela. Bambo wa m’fanizoli ataona mwana wake wolapa “ali capatali ndithu,” anathamangila mwanayo, kumukumbatila na kum’khululukila na mtima wonse. Zimenezi zimatithandiza kumvetsa bwino cifundo ca Yehova na cisomo cake. (Luka 15:11-32) Yesu anathandiza ena kumvetsa kuti Yehova ni Tate wotani kwenikweni. w24.02 10 ¶8-9