Cisanu, August 8
Munthu amene amacita zabwino amaopa Yehova.—Miy. 14:2.
Tikamaona makhalidwe oipa m’dzikoli, timamva monga mmene Loti anamvela. Iye “anavutika mtima kwambili ndi kulowelela kwa anthu ophwanya malamulo mu khalidwe lawo lotayilila,” podziŵa kuti Atate wathu wakumwamba amadana na makhalidwe oipa. (2 Pet. 2:7, 8) Kuopa Mulungu komanso kum’konda kunalimbikitsa Loti kupewa makhalidwe oipa a anthu a m’nthawi yake. Nafenso masiku ano, tili pakati pa anthu amene salemekeza malamulo a Yehova. Ngakhale n’telo, n’zotheka kukhalabe oyela ngati timam’konda Mulungu na kumuopa. Yehova amatithandiza kucita zimenezo kupyolela m’buku la Miyambo. Akhristu onse, amuna, akazi, ana, komanso okalamba, angapindule na uphungu wanzelu wa m’bukuli. Kuopa Yehova kumatithandiza kupewa kugwilizana na anthu a makhalidwe oipa. w23.06 20 ¶1-2; 21 ¶5
Ciŵelu, August 9
Ngati munthu akufuna kunditsatila, adzikane yekha ndipo anyamule mtengo wake wozunzikilapo nʼkupitiliza kunditsatila tsiku ndi tsiku.—Luka 9:23.
Mwina acibale anu akukutsutsani, kapena munasiya zolinga zanu za kuthupi kuti muike za Ufumu patsogolo pa umoyo wanu. (Mat. 6:33) Ngati n’telo, dziŵani kuti Yehova amaona nchito za kukhulupilika kwanu. (Aheb. 6:10) Mwacionekele, mwapeza madalitso amene Yesu anachula ponena kuti: “Palibe amene anasiya nyumba, abale, alongo, amayi, abambo, ana kapena minda cifukwa ca ine, ndi cifukwa ca uthenga wabwino, amene panopa sadzapeza zoculuka kuwilikiza maulendo 100 m’nthawi ino. Iye adzapeza nyumba, abale, alongo, amayi, ana na minda, pamodzi na mazunzo, ndipo m’nthawi imene ikubwelayo, adzapeza moyo wosatha.” (Maliko 10:29, 30) Madalitso amene mwapezawo ni oculuka kwambili kuposa zimene munasiya.—Sal. 37:4. w24.03 9 ¶5
Sondo, August 10
Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.—Miy. 17:17.
Pamene Akhristu ku Yudeya anali pa njala yadzaoneni. Abale mu mpingo wa ku Antiokeya “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo kwa abale a ku Yudeya, aliyense mogwilizana ndi zimene akanakwanitsa.” (Mac. 11:27-30) Ngakhale kuti okhudzidwa na njala anali kukhala kutali kwambili na ku Antiyokeya, Akhristu a ku Antiyokeya anapelekabe thandizo kwa abale awo. (1 Yoh. 3:17, 18) Nafenso tingawacitile cifundo alambili anzathu tikamva kuti tsoka lawagwela. Timacitapo kanthu mwamsanga, mwina mwa kufunsa akulu ngati tingadzipeleke kukathandizila. Cina, timapanga zopeleka pa nchito ya padziko lonse, kapena timapemphelela omwe akumana na tsokalo. Abale na alongo athu angadzafunikile thandizo kuti apeze zofunikila pa umoyo. Mfumu yathu Khristu Yesu akadzabwela kudzaweluza anthu, tikufuna adzatipeze tikuonetsa cifundo, na kutiuza kuti “lowani mu Ufumu.”—Mat. 25:34-40. w23.07 4 ¶9-10; 6 ¶12