Ciŵelu, August 9
Ngati munthu akufuna kunditsatila, adzikane yekha ndipo anyamule mtengo wake wozunzikilapo nʼkupitiliza kunditsatila tsiku ndi tsiku.—Luka 9:23.
Mwina acibale anu akukutsutsani, kapena munasiya zolinga zanu za kuthupi kuti muike za Ufumu patsogolo pa umoyo wanu. (Mat. 6:33) Ngati n’telo, dziŵani kuti Yehova amaona nchito za kukhulupilika kwanu. (Aheb. 6:10) Mwacionekele, mwapeza madalitso amene Yesu anachula ponena kuti: “Palibe amene anasiya nyumba, abale, alongo, amayi, abambo, ana kapena minda cifukwa ca ine, ndi cifukwa ca uthenga wabwino, amene panopa sadzapeza zoculuka kuwilikiza maulendo 100 m’nthawi ino. Iye adzapeza nyumba, abale, alongo, amayi, ana na minda, pamodzi na mazunzo, ndipo m’nthawi imene ikubwelayo, adzapeza moyo wosatha.” (Maliko 10:29, 30) Madalitso amene mwapezawo ni oculuka kwambili kuposa zimene munasiya.—Sal. 37:4. w24.03 9 ¶5
Sondo, August 10
Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.—Miy. 17:17.
Pamene Akhristu ku Yudeya anali pa njala yadzaoneni. Abale mu mpingo wa ku Antiokeya “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo kwa abale a ku Yudeya, aliyense mogwilizana ndi zimene akanakwanitsa.” (Mac. 11:27-30) Ngakhale kuti okhudzidwa na njala anali kukhala kutali kwambili na ku Antiyokeya, Akhristu a ku Antiyokeya anapelekabe thandizo kwa abale awo. (1 Yoh. 3:17, 18) Nafenso tingawacitile cifundo alambili anzathu tikamva kuti tsoka lawagwela. Timacitapo kanthu mwamsanga, mwina mwa kufunsa akulu ngati tingadzipeleke kukathandizila. Cina, timapanga zopeleka pa nchito ya padziko lonse, kapena timapemphelela omwe akumana na tsokalo. Abale na alongo athu angadzafunikile thandizo kuti apeze zofunikila pa umoyo. Mfumu yathu Khristu Yesu akadzabwela kudzaweluza anthu, tikufuna adzatipeze tikuonetsa cifundo, na kutiuza kuti “lowani mu Ufumu.”—Mat. 25:34-40. w23.07 4 ¶9-10; 6 ¶12
Mande, August 11
Anthu onse adziŵe kuti ndinu ololela.—Afil. 4:5.
Yesu anatengela citsanzo ca Yehova ca kulolela. Iye anatumidwa padziko lapansi kudzalalikila “kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” Koma anaonetsa kulolela pocita utumiki wakewo. Panthawi ina, mayi wina amene sanali Mwisiraeli anam’condelela kuti acilitse mwana wake wamkazi, amene anali ‘atagwidwa ndi ciwanda mocititsa mantha.’ Mwacifundo, Yesu anacita zimene mayiyo anam’pempha ndipo anam’cilitsa mwanayo. (Mat. 15:21-28) Naci citsanzo cina. Ca kumayambililo kwa utumiki wake, Yesu ananena kuti: “Aliyense amene adzandikane . . . , inenso ndidzamukana.” (Mat. 10:33) Iye anakanidwa katatu na Petulo. Koma kodi Yesu anam’kana Petulo? Ayi. Yesu anaona kulapa na cikhulupililo ca Petulo. Pambuyo poukitsidwa, Yesu anaonekela kwa Petulo. Ndipo mwacionekele, anam’tsimikizila kuti anam’khululukila komanso kuti anali kum’kondabe. (Luka 24:33, 34) Yehova Mulungu na Yesu Khristu ni ololela. Nanga bwanji ife? Yehova amafuna kuti nafenso tikhale ololela. w23.07 21 ¶6-7