Mande, September 22
Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza mʼdzina la Atate, ndi la Mwana.—Mat. 28:19.
Mosakayikila, Yesu anafuna kuti ena aziseŵenzetsa dzina lenileni la Atate wake. Atsogoleli ena a cipembedzo a m’nthawi imeneyo anali kunena kuti dzina la Mulungu ni lolemekezeka kwambili moti siliyenela kuchulidwa. Koma Yesu sanalole kuti miyambo yosazikika m’Malemba imeneyo imulepheletse kulemekeza dzina la Atate wake. Ganizilani zimene zinacitika atacilitsa munthu wogwidwa na ziŵanda m’cigawo ca Agerasa. Anthu anacita mantha kwambili, ndipo anacondelela Yesu kuti acoke. Conco, iye sanakhalitse m’cigawo cimeneco. (Maliko 5:16, 17) Ngakhale n’telo, iye anafunabe kuti anthu adziŵe dzina la Yehova m’cigawo cimeneci. Conco, anauza wocilitsidwayo kuti aziuza anthu zimene Yehova anam’citila, osati zimene Yesu anacita. (Maliko 5:19) N’zimenenso amafuna masiku ano—kuti tidziŵikitse dzina la Atate ake pa dziko lonse lapansi! (Mat. 24:14; 28:20) Tikacita zimenezi, timakondweletsa Mfumu yathu, Yesu. w24.02 10 ¶10
Ciŵili, September 23
Walimbana ndi mavuto osiyanasiyana cifukwa ca dzina langa.—Chiv. 2:3.
Ndife odalitsika cotani nanga kukhala m’gulu la Yehova pa nthawi ino yovuta ya masiku otsiliza! Pomwe mavuto a m’dzikoli akuwonjezeleka, Yehova watipatsa banja lauzimu la abale na alongo ogwilizana. (Sal. 133:1) Amatithandiza kukhala na mabanja ogwilizana. (Aef. 5:33–6:1) Amatipatsanso nzelu na kuzindikila kuti tikhale na mtendele wa mumtima. Komabe, tiyenela kulimbikila kuti tipitilize kutumikila Yehova mokhulupilika. Cifukwa ciyani? Cifukwa nthawi zina tingakhumudwe na zophophonya za ena. Cina, tingakhumudwe na zophophonya zathu, maka-maka ngati talakwitsa cina cake mobweleza-bweleza. Komabe, tiyenela kulimbikilabe kutumikila Yehova (1) ngati Mkhristu mnzathu watikhumudwitsa, (2) ngati tagwilitsidwa mwala mu ukwati wathu, komanso (3) ngati takhumudwa na zophophonya zathu. w24.03 14 ¶1-2
Citatu, September 24
Mulimonse mmene tapitila patsogolo, tiyeni tipitilize kupita patsogolo pocita zomwe tikucitazo.—Afil. 3:16.
Nthawi na nthawi, mumamva zocitika za abale na alongo amene adzipeleka kuti awonjezele utumiki wawo wopatulika. Mwina analoŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu, kapena anasamukila ku malo osoŵa. Ngati mungathe kudziikila zolinga ngati zimenezi, teloni. Anthu a Yehova ni ofunitsitsa kuwonjezela utumiki wawo. (Mac. 16:9) Nanga bwanji ngati pali pano simungakwanitse kucita zimenezi? Musamadzione kuti ndinu wolephela podziyelekezela na amene angakwanitse. Cofunika kwambili kwa Akhristu ni kupitilizabe kutumikila mokhulupilika. (Mat. 10:22) Musaiŵale kuti Yehova amakondwela ngako ngati mum’patsa zonse zimene mungathe malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wanu. Iyi ndiyo njila yabwino kwambili imene mungapitilizile kutsatila Yesu pambuyo pa ubatizo wanu.—Sal. 26:1. w24.03 10 ¶11