Sondo, September 21
Nawonso akazi akhale . . . ocita zinthu mosapitilila malile, okhulupilika m’zinthu zonse.—1 Tim. 3:11.
Timacita cidwi kuona mmene mwana amakulila mwamsanga kukhala wamkulu. Kukula kumeneku kumacitika pakokha. Komabe, kukhala Mkhristu wokhwima sikucitika pakokha. (1 Akor. 13:11; Aheb. 6:1) Kuti tikwanilitse colinga cimeneci, tiyenela kukhala paubwenzi wa thithithi na Yehova. Tifunikilanso mzimu wake woyela pokulitsa makhalidwe aumulungu, kukulitsa maluso othandiza komanso kukonzekela maudindo a m’tsogolo. (Miy. 1:5) Yehova ndiye analenga amuna na akazi. (Gen. 1:27) N’zoonekelatu kuti amuna na akazi amasiyana m’maonekedwe. Ndipo amasiyananso m’njila zina. Mwacitsanzo, Yehova analenga amuna na akazi kuti azigwila nchito zosiyana. Conco, onse ayenela kukhala na makhalidwe komanso maluso amene angawathandize kukwanilitsa maudindo awo.—Gen. 2:18. w23.12 18 ¶1-2
Mande, September 22
Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza mʼdzina la Atate, ndi la Mwana.—Mat. 28:19.
Mosakayikila, Yesu anafuna kuti ena aziseŵenzetsa dzina lenileni la Atate wake. Atsogoleli ena a cipembedzo a m’nthawi imeneyo anali kunena kuti dzina la Mulungu ni lolemekezeka kwambili moti siliyenela kuchulidwa. Koma Yesu sanalole kuti miyambo yosazikika m’Malemba imeneyo imulepheletse kulemekeza dzina la Atate wake. Ganizilani zimene zinacitika atacilitsa munthu wogwidwa na ziŵanda m’cigawo ca Agerasa. Anthu anacita mantha kwambili, ndipo anacondelela Yesu kuti acoke. Conco, iye sanakhalitse m’cigawo cimeneco. (Maliko 5:16, 17) Ngakhale n’telo, iye anafunabe kuti anthu adziŵe dzina la Yehova m’cigawo cimeneci. Conco, anauza wocilitsidwayo kuti aziuza anthu zimene Yehova anam’citila, osati zimene Yesu anacita. (Maliko 5:19) N’zimenenso amafuna masiku ano—kuti tidziŵikitse dzina la Atate ake pa dziko lonse lapansi! (Mat. 24:14; 28:20) Tikacita zimenezi, timakondweletsa Mfumu yathu, Yesu. w24.02 10 ¶10
Ciŵili, September 23
Walimbana ndi mavuto osiyanasiyana cifukwa ca dzina langa.—Chiv. 2:3.
Ndife odalitsika cotani nanga kukhala m’gulu la Yehova pa nthawi ino yovuta ya masiku otsiliza! Pomwe mavuto a m’dzikoli akuwonjezeleka, Yehova watipatsa banja lauzimu la abale na alongo ogwilizana. (Sal. 133:1) Amatithandiza kukhala na mabanja ogwilizana. (Aef. 5:33–6:1) Amatipatsanso nzelu na kuzindikila kuti tikhale na mtendele wa mumtima. Komabe, tiyenela kulimbikila kuti tipitilize kutumikila Yehova mokhulupilika. Cifukwa ciyani? Cifukwa nthawi zina tingakhumudwe na zophophonya za ena. Cina, tingakhumudwe na zophophonya zathu, maka-maka ngati talakwitsa cina cake mobweleza-bweleza. Komabe, tiyenela kulimbikilabe kutumikila Yehova (1) ngati Mkhristu mnzathu watikhumudwitsa, (2) ngati tagwilitsidwa mwala mu ukwati wathu, komanso (3) ngati takhumudwa na zophophonya zathu. w24.03 14 ¶1-2