Mande, September 29
Wosangalala ndi munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene macimo ake akhululukidwa.—Sal. 32:1.
Ganizilani cifukwa cake munadzipatulila na kubatizika. Munatenga masitepe amenewa pofuna kukhala kumbali ya Yehova. Kumbukilani cimene cinakukhutilitsani kuti mwapeza coonadi. Munaphunzila coonadi ponena za Yehova, ndipo munayamba kukonda Atate wanu wakumwamba, na kum’lemekeza. Cina, munakhala na cikhulupililo ndipo cinakusonkhezelani kulapa. Kenako, munaleka makhalidwe oipa, n’kuyamba kucita zinthu zokondweletsa Mulungu. Mtima wanu unakhala m’malo mutazindikila kuti Mulungu wakukhululukilani. (Sal. 32:2) Kuwonjezela apo, munayamba kupezeka pa misonkhano yacikhristu, na kuuzako ena zinthu zosangalatsa zimene munali kuphunzila. Tsopano monga Mkhristu wobatizika, mukuyenda pa msewu wopita kumoyo, ndipo ndinu wofunitsitsa kuyendabe pa msewuwo. (Mat. 7:13, 14) Khalanibe olimba, pa kudzipeleka kwanu kwa Yehova komanso osasunthika pomvela malamulo ake. w23.07 17 ¶14; 19 ¶19
Ciŵili, September 30
Mulungu ndi wokhulupilika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile, koma pamene mukukumana ndi mayeselowo iye adzapeleka njila yopulumukila kuti muthe kuwapilila.—1 Akor. 10:13.
Kusinkhasinkha pemphelo limene munapeleka podzipatulila kwa Yehova, kudzakuthandizani kugonjetsa mayeselo alionse amene mungakumane nawo. Mwacitsanzo, kodi mungayambe kuceza mokopana na mkazi wa mwini kapena mwamuna wa mwini? M’pang’ono pomwe! Cifukwa munasankhilatu kuti simungacite za mtundu umenewu. Ngati simulola zilakolako zoipa kuzika mizu mwa inu, simudzafunika kulimbana nazo mtsogolo. Ndipo mudzapewa kuyenda “panjila yoipa.” (Miy. 4:14, 15) Kuganizila citsanzo ca Yesu kungakuthandizeni. Iye anali wofunitsitsa kukondweletsa Atate ake. Nanunso muyenela kukana nthawi yomweyo komanso mosasunthika ciliconse cimene cingakhumudwitse Mulungu amene munadzipatulila kwa Iye. (Mat. 4:10; Yoh. 8:29) Kwenikweni, mayeso na mayeselo amakupatsani mpata woonetsa kuti ndinu wofunitsitsa kum’tsatilabe Yesu. Mwa kutelo, dziŵani kuti Yehova adzakuthandizani. w24.03 9-10 ¶8-10
Citatu, October 1
Nzelu yocokela kumwamba . . . ndi yokonzeka kumvela.—Yak. 3:17.
Kodi kukhala womvela kumakuvutani? Davide nayenso, zinali kumuvuta nthawi zina. Ndiye cifukwa cake anapemphela kuti: “Ndipatseni mtima wofunitsitsa kukumvelani.” (Sal. 51:12) Davide anali kukonda Yehova. Ngakhale n’telo, nthawi zina Davide zinali kumuvuta kuonetsa mtima womvela, ndipo ni mmenenso zilili kwa ise. Cifukwa ciyani? Coyamba, cifukwa cakuti tinatengela mzimu wa kusamvela kwa makolo athu. Caciŵili, Satana amayesetsa kutinyengelela kuti tipandukile Yehova mmene iye anacitila. (2 Akor. 11:3) Cacitatu, tikukhala m’dziko mmene khalidwe la kupanduka lili paliponse, ndipo “mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka, tsopano kakugwila nchito mwa ana osamvela.” (Aef. 2:2) Tiyenela kucita zonse zothekha kuti tilimbane na ucimo, Satana, komanso dziko, kuti timvele Yehova komanso aja amene wapatsa ulamulilo. w23.10 6 ¶1