NKHANI 9
Kodi Tili mu “Masiku Otsiliza”?
Kodi ndi zinthu ziti zimene Baibo inakambilatu kuti zidzacitika m’masiku athu ano?
Kodi Mau a Mulungu anakambilatu kuti mu “masiku otsiliza” anthu adzakhala otani?
Nanga ndi zinthu zabwino ziti zimene Baibo inakambilatu kuti zidzacitika m’masiku otsiliza?
1. Kodi n’ciani cingatithandize kudziŵa za mtsogolo?
KODI mwamvetselapo nyuzi pa TV kapena pa wailesi ndi kudzifunsa kuti, ‘Kodi dziko ili lipita kuti?’ Zinthu zoopsa ndi zomvetsa cisoni zimacitika mosayembekezeleka cakuti palibe munthu amene angadziŵe zimene zidzacitika maŵa. (Yakobo 4:14) Koma Yehova amadziŵa za mtsogolo. (Yesaya 46:10) Kale kwambili, Mau ake, Baibo, anakambilatu za zinthu zoipa zimene zicitika masiku ano, ndi zinthu zabwino zimene zidzacitika mtsogolo posacedwa.
2, 3. Kodi ophunzila a Yesu anam’funsa funso liti? Ndipo iye analiyankha bwanji?
2 Yesu Kristu anakamba za Ufumu wa Mulungu, umene udzacotsa zoipa zonse ndi kusintha dziko lapansi kukhala paladaiso. (Luka 4:43) Anthu anafuna kudziŵa pamene Ufumu udzabwela. Ndipo ophunzila a Yesu anam’funsa kuti: “Cizindikilo ca kukhalapo kwanu ndi ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciani?” (Mateyu 24:3) Yesu powayankha anawauza kuti, ndi Yehova Mulungu cabe amene amadziŵa nthawi yeni-yeni pamene mapeto a dongosolo lino la zinthu adzafika. (Mateyu 24:36) Yesu sanawauze ophunzila ake nthawi yeni-yeni imene mapeto adzafika. Komabe, anakambilatu zinthu zimene zidzacitika padziko lapansi kutatsala pang’ono kuti Ufumu ubweletse mtendele weni-weni ndi cisungiko kwa anthu. Zimene anakambilatu n’zimene zicitika masiku ano.
3 Tikalibe kuona maumboni oonetsa kuti tili mu “masiku otsiliza,” tiyeni mwacidule tikambitsilane za nkhondo imene palibe munthu amene akanatha kuiona ndi maso. Nkhondo imeneyi inacitikila kumwamba, ndipo zotsatilapo zake zimatikhudza.
NKHONDO YA KUMWAMBA
4, 5. (a) Kodi n’ciani cinacitika kumwamba Yesu atangoikidwa kukhala Mfumu? (b) Malinga ndi lemba la Chivumbulutso 12:12, kodi n’ciani cinatsatilapo pambuyo pa nkhondo yakumwamba?
4 Nkhani yapita m’buku lino inafotokoza kuti Yesu Kristu anakhala Mfumu kumwamba m’caka ca 1914. (Danieli 7:13, 14) Atangopatsidwa mphamvu zolamulila, iye anacitapo kanthu nthawi imeneyo. Baibo imati: “Kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli [dzina lina la Yesu] ndi angelo ake anamenyana ndi cinjoka [Satana Mdyelekezi]. Cinjokaco ndi angelo ake anamenya nkhondo.”a Satana ndi angelo ake oipa, kapena kuti ziŵanda, anagonjetsedwa ndipo anaponyedwa kudziko lapansi kucokela kumwamba. Kwa angelo okhulupilika a Mulungu kunali cisangalalo cacikulu cifukwa cakuti Satana ndi ziŵanda zake anacotsedwa kumwamba. Koma kwa anthu zinthu sizinali bwino. Baibo inakambilatu kuti: “Tsoka dziko lapansi . . . cifukwa Mdyelekezi watsikila kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziŵa kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa.”—Chivumbulutso 12:7, 9, 12.
5 Onani zimene zinatsatilapo pambuyo pa nkhondo yakumwamba imeneyi. Cifukwa ca mkwiyo, Satana anabweletsa mavuto osiyana-siyana padziko lapansi. Monga mmene mudzaonela, tsopano tili m’nthawi ya mavuto imeneyo. Koma idzakhala yaifupi—“kanthawi kocepa” cabe. Ngakhale Satana amadziŵa zimenezi. Nthawi imeneyi ndi imene Baibo imati “masiku otsiliza.” (2 Timoteyo 3:1) Ndife okondwa kwambili kuti posacedwa Mulungu adzacotsa mphamvu ya Mdyelekezi padziko lapansi! Tsopano tiyeni tione zinthu zina zimene zicitika masiku ano zimene Baibo inakambilatu. Zinthu zimenezi zimatsimikizila kuti tili m’masiku otsiliza ndi kuti posacedwapa Ufumu wa Mulungu udzabweletsa madalitso osatha kwa anthu onse amene amakonda Yehova. Coyamba, tiyeni tikambitsilane mbali zinai za cizindikilo cimene Yesu ananena kuti cidzaonetsa kuti tili m’masiku otsiliza.
ZOCITIKA ZAZIKULU ZA M’MASIKU OTSILIZA
6, 7. Kodi mau a Yesu onena za nkhondo ndi njala akukwanilitsika bwanji masiku ano?
6 “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Anthu mamiliyoni ambili aphedwa pankhondo m’zaka 100 zapitazo. Katswili wa mbili yakale wa ku Britain analemba kuti: “M’mbili yonse yolembedwa, anthu anaphedwa kwambili m’zaka zoyambila 1901 mpaka 2000. . . . Pa zaka zonsezi nkhondo zinali kucitika mongotsatizana-tsatizana cakuti ndi nthawi zoŵelengeka ndiponso zazifupi cabe pamene sikunali nkhondo.” Lipoti lolembedwa ndi bungwe lina lake (Worldwatch Institute) linati: “Anthu amene anaphedwa m’zaka za pakati pa 1901 mpaka 2000 anali oculuka kwambili poyelekezela ndi amene anaphedwa pankhondo zimene zinacitika m’zaka 100 zoyambilila m’nthawi ya AD mpaka mu 1899.” Anthu oposa 100 miliyoni afa m’nkhondo kuyambila m’caka ca 1914. Ngakhale kuti timadziŵa mmene zimamvekela ukataikilidwa wokondedwa mmodzi pankhondo, sitingamvetsetse cisoni ndi kupwetekedwa mtima kumene anthu mamiliyoni ambili amene ataikilidwa okondedwa ao mu imfa amakhala nako.
7 “Kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Anthu ofufuza amakamba kuti padziko lapansi pakhala cakudya coculuka kwambili pa zaka 30 zapitazo. Komabe, kusoŵa kwa cakudya kwapitilizabe cifukwa cakuti anthu ambili alibe ndalama zokwanila zogulila cakudya kapena malo olima. M’maiko osauka, anthu oposa 1 biliyoni amangopeza ndalama yokwana 1 dola kapena kucepelapo ya cakudya patsiku. Ambili mwa anthu amenewa amavutika ndi njala yosatha. Bungwe loyang’anila za umoyo wa anthu padziko lonse (World Health Organization) limanena kuti matenda obwela cifukwa ca njala ndi amene amapha ana oposa 5 miliyoni caka ciliconse.
8, 9. Kodi n’ciani cionetsa kuti maulosi a Yesu okamba za zivomezi ndi milili akukwanilitsika?
8 “Kudzacitika zivomezi zamphamvu.” (Luka 21:11) Bungwe lofufuza za nthaka ndi miyala la ku America, linapeza kuti kucokela mu 1990 cabe zivomezi pafupi-fupi 19 zimacitika caka ciliconse. Zivomezi zimenezi ndi zamphamvu kwambili cakuti zimagumula nyumba zikulu-zikulu ndi kung’amba nthaka. Pacitikanso zivomezi zamphamvu kwambili zimene zaonongelatu nyumba zikulu-zikulu. Zolembedwa zimene zilipo zaonetsa kuti zivomezi zapha anthu oposa 2 miliyoni kucokela zaka za mu ma 1900. Nkhani ina ya panyuzi inati: “Kupita patsogolo kwa sayansi kwangocepetsa pang’ono cabe imfa zimenezi.”
9 “Kudzakhala milili.” (Luka 21:11) Ngakhale kuti pakhala kupita patsogolo mu zamankhwala, matenda akale ndi atsopano amavutitsabe mtundu wa anthu. Lipoti lina linakamba kuti matenda okwana 20 odziŵika bwino, ophatikizapo TB, maleliya ndi kolela, afala kwambili m’zaka zaposacedwapa. Ndipo matenda ena akumakhala ovuta kwambili kuti amve mankhwala. Komanso pabwela matenda ena atsopano osacepela 30. Ena mwa matenda amenewa alibe mankhwala ndipo ndi akupha.
ANTHU A M’MASIKU OTSILIZA
10. Kodi ndi makhalidwe ati ochulidwa pa 2 Timoteyo 3:1-5 amene mumaona mwa anthu masiku ano?
10 Kuonjezela pa kunenelatu zocitika za padziko lapansi, Baibo inakambilatunso kuti m’masiku otsiliza makhalidwe a anthu ambili adzasintha. Mtumwi Paulo anafotokoza mmene anthu ambili adzakhalila. Pa lemba la 2 Timoteyo 3:1-5, iye anati: “Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta.” Mwa zina, Paulo anakamba kuti anthu adzakhala
odzikonda
okonda ndalama
osamvela makolo
osakhulupilika
opanda cikondi cacibadwa
osadziletsa
oopsa
okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu
ooneka ngati odzipeleka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudzipelekako iwasinthe
11. Kodi lemba la Salimo 92:7 limafotokoza bwanji zimene zidzacitika kwa anthu oipa?
11 Kodi kumene mumakhala anthu amaonetsa makhalidwe amenewa? N’zosacita kufunsa! Anthu kulikonse ali ndi makhalidwe oipa. Zimenezi zimaonetsa kuti posacedwa Mulungu adzacitapo kanthu, cifukwa Baibo imati: “Anthu oipa akamaphuka ngati msipu, ndipo anthu onse ocita zopweteka anzao akamaphuka ngati maluŵa, amatelo kuti aonongeke kwamuyaya.”—Salimo 92:7.
ZINTHU ZABWINO
12, 13. Kodi “cidziŵitso coona” caculuka bwanji mu “nthawi yamapeto” ino?
12 Ndithudi, masiku otsiliza ali ndi mavuto ambili, monga mmene Baibo inakambilatu. Komabe, ngakhale kuti padziko pali mavuto ambili, pakati pa olambila a Yehova pakucitika zinthu zabwino.
13 Buku la m’Baibo la Danieli linanenelatu kuti: ‘Cidziŵitso coona cidzaculuka.’ Kodi zimenezi zinali kudzacitika liti? Zinali kudzacitika mu “nthawi yamapeto.” (Danieli 12:4) Kuyambila mu 1914 maka-maka, Yehova wathandiza anthu amene moona mtima amafuna kum’tumikila kuti amvetse bwino Baibo. Iwo amvetsa bwino coonadi camtengo wapatali conena za dzina la Mulungu ndi colinga cake, nsembe ya dipo la Yesu Kristu, mmene akufa alili, ndi ciukililo. Ndipo olambila Yehova aphunzila mmene angakhalile ndi moyo umene umawapindulitsa, umene umacititsanso kuti Mulungu atamandidwe. Iwo amvetsanso mbali ya Ufumu wa Mulungu ndi mmene udzakonzela zinthu padziko lapansi. Kodi amacita ciani ndi cidziŵitso cimeneci? Funso limeneli litifikitsa pa ulosi wina umene ukukwanilitsika m’masiku ano otsiliza.
“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Mateyu 24:14
14. Kodi uthenga wabwino wa Ufumu walalikidwa mokulila bwanji masiku ano? Ndipo ndani amene amacita nchito imeneyi?
14 Mu ulosi wake wonena za cimalizilo ca dongosolo lino la zinthu, Yesu anakamba kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyu 24:3, 14) Padziko lonse lapansi, uthenga wabwino wa Ufumu wonena za zimene Ufumu uli, zimene udzacita ndi mmene tingapezele madalitso, ukulalikidwa m’maiko oposa 235, ndi m’zinenelo zoposa 500. Mboni za Yehova mamiliyoni ambili zimalalikila mwacangu uthenga wabwino wa Ufumu. Iwo amacokela mu “fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse.” (Chivumbulutso 7:9) Mboni zimacititsa maphunzilo a Baibo kwaulele kwa anthu mamiliyoni amene amafuna kudziŵa zimene Baibo imanena m’ceni-ceni. Kumeneku ndi kukwanilitsika kocititsa cidwi kwa ulosi, maka-maka cifukwa cakuti Yesu anakambilatu kuti Akristu oona ‘adzadedwa ndi anthu onse.’—Luka 21:17.
KODI INU MUDZACITAPO CIANI?
15. (a) Kodi mumakhulupilila kuti tili m’masiku otsiliza? Ndipo n’cifukwa ciani? (b) Kodi “mapeto” akadzafika n’ciani cidzacitikila anthu amene amatsutsa Yehova? Nanga n’ciani cidzacitika ndi anthu amene amagonjela ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu?
15 Popeza maulosi ambili akukwanilitsika masiku ano, kodi simuvomeleza kuti tili m’masiku otsiliza? Uthenga wabwino ukalalikidwa pamlingo umene Yehova afuna, “mapeto” adzafika. (Mateyu 24:14) “Mapeto” atanthauza nthawi imene Mulungu adzacotsa zoipa zonse padziko lapansi. Poononga anthu onse amene amamutsutsa, Yehova adzagwilitsila nchito Yesu ndi angelo amphamvu. (2 Atesalonika 1:6-9) Satana ndi ziŵanda zake sadzasoceletsanso mitundu ya anthu. Pambuyo pa zimenezi, Ufumu wa Mulungu udzabweletsa madalitso kwa anthu onse amene amagonjela ulamulilo wake wolungama.—Chivumbulutso 20:1-3; 21:3-5.
16. Kodi cinthu canzelu cimene muyenela kucita n’ciani?
16 Popeza mapeto a Satana ali pafupi, tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndiyenela kumacita ciani?’ N’cinthu canzelu kupitiliza kuphunzila zambili za Yehova ndi zimene amafuna kwa ife. (Yohane 17:3) Khalani wophunzila Baibo wakhama. Muzigwilizana nthawi zonse ndi anthu amene amafuna kucita cifunilo ca Yehova. (Aheberi 10:24, 25) Pitilizani kupeza cidziŵitso cimene Yehova Mulungu amapeleka moculuka kwa anthu padziko lonse lapansi, ndipo pangani masinthidwe ofunikila paumoyo wanu kuti mulandilike kwa Mulungu.—Yakobo 4:8.
17. N’cifukwa ciani cionongeko ca anthu oipa cidzafikila anthu ambili modzidzimutsa?
17 Yesu anakambilatu kuti anthu ambili adzanyalanyaza umboni woonetsa kuti tili m’masiku otsiliza. Cionongeko ca anthu oipa cidzacitika mwadzidzidzi ndi mosayembekezeka. Cidzafika pa anthu ambili mwadzidzidzi monga mbala usiku. (1 Atesalonika 5:2) Yesu anacenjeza kuti: “Monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalile. M’masiku amenewo cigumula cisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatila ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikila tsiku limene Nowa analoŵa m’cingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kucitika mpaka cigumula cinafika n’kuwaseselatu onsewo. Zidzatelonso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:37-39.
18. Kodi tiyenela kulabadila cenjezo liti la Yesu?
18 Conco, Yesu anauza omvela ake kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambili, kumwa kwambili, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikileni modzidzimutsa ngati msampha. Pakuti lidzafikila onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi. Cotelo, khalani maso ndipo muzipemphela mopembedzela nthawi zonse, kuti mudzathe kuthaŵa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kucitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:34-36) N’cinthu canzelu kulabadila mau a Yesu. Cifukwa ninji? Cifukwa cakuti anthu amene amalandilika kwa Yehova Mulungu ndi “Mwana wa munthu,” Yesu Kristu, ali ndi ciyembekezo codzapulumuka mapeto a dongosolo la zinthu la Satana, ndi kudzakhala kosatha m’dziko losangalatsa limene layandikila kwambili.—Yohane 3:16; 2 Petulo 3:13.
a Kuti mudziŵe zakuti Mikayeli ndi dzina lina la Yesu Kristu, onani Zakumapeto, mapeji 218 mpaka 219.