LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 12/1 masa. 23-27
  • ‘Citani Zimenezi Pondikumbukila’

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • ‘Citani Zimenezi Pondikumbukila’
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIZINDIKILO ZA PA CIKUMBUTSO
  • KODI ZIZINDIKILOZI ZIMAIMILA CIANI?
  • KUCITA CIKUMBUTSO CA IMFA YA KRISTU
  • Cifukwa Cake Timacita Mgonelo wa Ambuye
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Mgonelo wa Ambuye—Mwambo Umene Umalemekeza Mulungu
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 12/1 masa. 23-27

‘Citani Zimenezi Pondikumbukila’

“Atayamika, anaunyema-nyema n’kunena kuti: ‘Mkate uwu ukuimila thupi langa limene likupelekedwa cifukwa ca inu. Muzicita zimenezi pondikumbukila.’”—1 AKOR. 11:24.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi tsiku la Cikumbutso limadziŵika bwanji caka ciliconse?

Kodi mkate ndi vinyo zimaimila ciani pa Mgonelo wa Ambuye?

N’cifukwa ciani tifunika kupezeka pa Cikumbutso mosasamala kanthu za ciyembekezo cathu?

1, 2. Kodi atumwi ayenela kuti anali kuganiza ciani Yesu asanapite ku Yerusalemu komaliza?

ALONDA ku Yerusalemu anaona kuti mwezi wakhala. Pamene akulu-akulu a Sanihedirini anauzidwa zimenezi, analengeza kuti mwezi watsopano wa Nisani wayamba. Ndiyeno, amithenga analengeza zimenezi. Atumwi anadziŵa kuti nthawi ya Pasika yayandikila. Mosakaikila, io anazindikila kuti Yesu anali kufuna kupita ku Yerusalemu mwamsanga kuti akafike Pasika asanayambe.

2 Panthawi imeneyo, Yesu ndi atumwi ake anali ku Pereya (ku tsidya la Yorodano) paulendo wake womaliza wopita ku Yerusalemu. (Mat. 19:1; 20:17, 29; Maliko 10:1, 32, 46) Ayuda akadziŵa tsiku la Nisani 1, kunali kusavuta kuti io adziŵe tsiku la Pasika imene inali kucitika pambuyo pa masiku 13, pa Nisani 14, dzuŵa likalowa.

3. N’cifukwa ciani Akristu amafuna kudziŵa tsiku la Pasika?

3 Mwambo wa Mgonelo wa Ambuye, umene umacitika patsiku lofanana ndi la Pasika, udzakhala pa April 14, 2014, dzuŵa litalowa. Tsiku limeneli lidzakhala tsiku lapadela kwa Akristu oona onse ndi anthu acidwi. N’cifukwa ciani tikutelo? Tikutelo cifukwa ca mau opezeka pa 1 Akorinto 11:23-25 amene amati: “Yesu, usiku umene anali kukapelekedwa anatenga mkate. Ndipo atayamika, anaunyema-nyema n’kunena kuti: ‘Mkate uwu ukuimila thupi langa limene likupelekedwa cifukwa ca inu. Muzicita zimenezi pondikumbukila.’ Anacitanso cimodzi-modzi ndi kapu.”

4. (a) Kodi ndi mafunso ati okhudza Pasika amene mungafunse? (b) Kodi timadziŵa bwanji tsiku limene kudzakhala Cikumbutso? (Onani bokosi lakuti “Cikumbutso ca 2014.”)

4 Mosakaikila inu mudzakhalapo pa mwambo umene Yesu anauza otsatila ake kuti azicita caka ciliconse. Mwambowu usanafike, muyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndiyenela kuukonzekela bwanji mwambowu? Kodi adzagwilitsila nchito zinthu zotani pamwambowo? N’ciani cidzacitikakumeneko? Kodi mwambo umenewo ndiponso zizindikilo zimene zimagwilitsidwa nchito n’zofunika bwanji kwa ine?’

ZIZINDIKILO ZA PA CIKUMBUTSO

5. Kodi Yesu anauza atumwi ake kucita ciani pokonzekela Pasika?

5 Pamene Yesu anauza atumwi ake kukakonza cipinda codyelamo Pasika, iye sanawauze kuti akakongoletse kwambili cipindaco. Koma anali kungofuna nyumba yoyenelela, yaukhondo ndi yaikulu imene ikanakwana anthu onse opezekapo. (Ŵelengani Maliko 14:12-16.) Iwo anayenela kutenga zinthu zofunika pa Pasika, kuphatikizapo mkate wopanda cofufumitsa ndi vinyo wofiila. Atamaliza Pasika, Yesu anakamba za mkate ndi vinyo. Mkate ndi vinyo ndi zizindikilo ziŵili zimene zimagwilitsilidwa nchito pa Cikumbutso.

6. (a) Kodi Yesu anakamba ciani za mkate atamaliza kudya Pasika? (b) Kodi ndi mkate wotani umene umagwilitsidwa nchito pa Cikumbutso?

6 Mtumwi Mateyu analipo panthawiyo ndipo analemba kuti: “Yesu anatenga mkate, ndipo atapempha dalitso, anaunyema-nyema n’kuupeleka kwa ophunzila ake. Iye anati: ‘Eni, idyani.’” (Mat. 26:26) “Mkate” umenewo unali wopanda cotupitsa ngati mkate umene anali kugwilitsila nchito pa Pasika. (Eks. 12:8; Deut. 16:3) Mkatewo unapangidwa ndi ufa wa tiligu ndi madzi popanda kuikako yisiti kapena zinthu zina zokometsela monga mcele. Mkatewo sunafufume cifukwa cakuti unali wopanda yisiti. Unali mkate wamba, wouma, wopyapyala wosavuta kunyema, kapena wokhala ngati bisiketi. Masiku ano, akulu mumpingo angapemphe munthu wina kuti apange mkate wotelo nthawi ya Cikumbutso isanakwane. Iye angapangile mkatewo pa pani yopakidwa mafuta pang’ono. (Ngati ufa wa tiligu kulibe, angagwilitsile nchito ufa wa mpunga, mapila, cimanga, kapena zakudya zina zofanana ndi zimenezi.) Mkate wozoloweleka wa Ayuda wochedwa matzoth wosaika mazila kapena anyenzi ungagwilitsilidwe nchito.

7. Kodi Yesu anali kukamba za vinyo wotani? Nanga ndi vinyo wotani umene tiyenela kugwilitsila nchito pa Cikumbutso masiku ano?

7 Mateyu anapitiliza kunena kuti: “[Yesu] anatenga kapu ndipo atayamika, anaipeleka kwa io n’kunena kuti: ‘Imwani nonsenu.’” (Mat. 26:27, 28) Panthawiyo, Yesu anatenga kapu ya vinyo wofiila. (Umenewo unali vinyo wowila osati cakumwa cosawila ca mphesa cifukwa cakuti nyengo yokolola mphesa inali itatha kale.) Aisiraeli sanagwilitsile nchito vinyo pa mwambo woyamba wa Pasika umene anacita ku Iguputo. Koma Yesu sananene kuti kumwa vinyo pa Pasika n’kulakwa. Ndipo iye anagwilitsila nchito vinyo pocita Mgonelo wa Ambuye. Conco, Akristu amagwilitsila nchito vinyo pa Cikumbutso. Popeza kuti magazi a Yesu anali kale ndi mphamvu yokwanila pa io okha, vinyo umene umagwilitsilidwa nchito pa Cikumbutso umakhala vinyo wamba, wopanda zinthu zowonjezela mphamvu kapena zokometsela. Vinyo wofiila umene umagulitsidwa monga ngati Chianti, Burgundy, Beaujolais, kapena vinyo wamba wofiila wodzipangila, ndi umene tiyenela kugwilitsila nchito pa Cikumbutso.

KODI ZIZINDIKILOZI ZIMAIMILA CIANI?

8. N’cifukwa ciani Akristu amafuna kudziŵa tanthauzo la mkate ndi vinyo?

8 Mtumwi Paulo anaonetsa kuti atumwi kuphatikizapo Akristu onse anafunikila kucita Mgonelo wa Ambuye. Iye analembela Akristu anzake a ku Korinto kuti: “Zimene ndinalandila kwa Ambuye n’zimene inenso ndinakupatsilani, zakuti Ambuye Yesu . . . anatenga mkate, atayamika, anaunyema-nyema n’kunena kuti: ‘Mkate uwu ukuimila thupi langa limene likupelekedwa cifukwa ca inu. Muzicita zimenezi pondikumbukila.’” (1 Akor. 11:23, 24) N’cifukwa cake Akristu masiku ano amacita mwambo umenewu kamodzi pa caka ndipo amafuna kudziŵa tanthauzo la mkate ndi vinyo.

9. Kodi anthu ena ali ndi maganizo olakwika otani ponena za mkate umene Yesu anagwilitsila nchito?

9 Anthu ena amene amapita ku chalichi amakamba kuti Yesu ananena kuti: ‘Mkate uwu ndi thupi langa.’ Iwo amakhulupilila kuti mkatewo unakhaladi thupi lake leni-leni. Koma zimenezo si zoona.a Yesu weni-weniyo anali ndi atumwi ake okhulupilika panthawiyo ndipo mkate wopanda cofufumitsa umene anafunikila kudya unaliponso. Mwacionekele, iye anali kukamba mophiphilitsa monga mmene anali kucitila nthawi zambili.—Yoh. 2:19-21; 4:13, 14; 10:7; 15:1.

10. Kodi mkate umene umagwilitsidwa nchito pa Mgonelo wa Ambuye umaimila ciani?

10 Mkate umene atumwi anali kuona ndiponso umene anafunikila kudya unali kuimila thupi la Yesu. Thupi lake liti? Pa nthawi ina, atumiki a Mulungu anali kukhulupilila kuti mkate unali kuimila “thupi la Kristu” limene ndi mpingo wa odzodzedwa cifukwa cakuti Yesu ananyema-nyema mkate koma mafupa ake sanathyoledwe. (Aef. 4:12; Aroma 12:4, 5; 1 Akor. 10:16, 17; 12:27) Koma m’kupita kwa nthawi, io anazindikila kuti Malemba amaonetsa kuti mkate umaimila thupi laumunthu la Yesu limene Mulungu anamukonzela. Yesu “anavutika m’thupi” mpaka anapacikidwa pa mtengo. Cotelo, pa Mgonelo wa Ambuye, mkate umaimila thupi laumunthu limene Yesu ‘ananyamulila macimo athu.’—1 Pet. 2:21-24; 4:1; Yoh. 19:33-36; Aheb. 10:5-7.

11, 12. (a) Kodi Yesu anakamba ciani ponena za vinyo? (b) Kodi vinyo umene umagwilitsidwa nchito pa Mgonelo wa Ambuye umaimila ciani?

11 Zimenezi zimatithandiza kumvetsetsa zimene Yesu anakamba ponena za vinyo. Timaŵelenga kuti: “Anacitanso cimodzi-modzi ndi kapu atadya cakudya camadzulo, ndipo anati: ‘Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga.’” (1 Akor. 11:25) Ma Baibo ambili amagwilitsila nchito mau ofanana ndi a m’Baibo yotembenuzidwa ndi Robert Young, imene imati: ‘Kapu iyi ndi pangano latsopano mwa magazi anga.’ Kodi kapu yeni-yeni imene Yesu ananyamula ndi imene inali pangano latsopano? Iyai. Liu lakuti “kapu” linatanthuza vinyo umene unali m’kapumo. Nanga vinyo unaimila ciani? Yesu ananena kuti unaimila magazi ake okhetsedwa.

12 Mu uthenga wabwino wa Maliko, timapeza mau a Yesu akuti: “Vinyoyu akuimila ‘magazi anga a pangano,’ amene adzakhetsedwa cifukwa ca anthu ambili.” (Maliko 14:24) Zoonadi, magazi a Yesu ‘anakhetsedwa cifukwa ca anthu ambili kuti macimo akhululukidwe.’ (Mat. 26:28) Conco, vinyo wofiila umaimiladi magazi eni-eni a Yesu. Kudzela m’dipo la magazi ake, “tingakhululukidwe macimo athu.”—Ŵelengani Aefeso 1:7.

KUCITA CIKUMBUTSO CA IMFA YA KRISTU

13. Kodi mwambo wa pa caka wa Cikumbutso ca imfa ya Kristu umacitika bwanji?

13 Ngati mudzasonkhana pa Cikumbutso ndi Mboni za Yehova kwa nthawi yoyamba, kodi muganiza kuti kudzakhala zotani? Msonkhanowo udzacitikila pa malo ooneka bwino ndi aukhondo pamene onse opezekapo angasangalale ndi mwambowo. Pangakhalenso maluwa, koma sipadzakhala zinthu zambili zokongoletsa ngati mmene zimakhalila pa cikondwelelo. Mkulu woyenelela adzakamba nkhani yomveka bwino yofotokoza zimene Baibo imanena zokhudza mwambo umenewo. Adzatithandiza kuona cifukwa cake tiyenela kuyamikila zimene Yesu anaticitila. Iye anatifela monga dipo kuti tidzakhale ndi moyo wosatha.—Ŵelengani Aroma 5:8-10.

14. Kodi nkhani ya Cikumbutso imafotokoza ziyembekezo ziŵili ziti?

14 Mkambi adzafotokozanso kuti Baibo imanena kuti Akristu ali ndi ziyembekezo zosiyana. Otsatila a Kristu ocepa ali ndi ciyembekezo cokalamulila ndi Kristu kumwamba ndipo atumwi ake okhulupilika ndi ena mwa anthu amene ali ndi ciyembekezo cimeneci. (Luka 12:32; 22:19, 20; Chiv. 14:1) Koma Akristu ambili amene akutumikila Mulungu mokhulupilika masiku ano, ali ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha m’paladaiso padziko lapansi. Ndipo cifunilo ca Mulungu cidzacitika padziko lapansi monga kumwamba. Izi n’zimene Akristu akhala akupemphelela kwa nthawi yaitali. (Matt. 6:10) Malemba amaonetsa mmene anthu adzasangalalila ndi moyo kosatha padziko lapansi.—Yes. 11:6-9; 35:5, 6; 65:21-23.

15, 16. Kodi mkate wa pa Mgonelo wa Ambuye amacita nao ciani?

15 Cakumapeto kwa nkhani ya Cikumbutso, mkambi adzanena kuti nthawi yafika yocita zimene Yesu anauza atumwi ake kucita. Monga takambila kale, padzakhala zizindikilo ziŵili zimene ndi mkate wopanda cofufumitsa ndi vinyo wofiila. Zizindikilo izi zingaikidwe pathebulo pafupi ndi mkambi. Mkambi adzafokoza zimene Yesu ananena ndi kucita pamene anayambitsa mwambo umenewu. Mwacitsanzo, Mateyu anati: “Yesu anatenga mkate, ndipo atapempha dalitso, anaunyema-nyema n’kuupeleka kwa ophunzila ake. Iye anati: ‘Eni, idyani. Mkate uwu ukuimila thupi langa.’” (Matt. 26:26) Yesu ananyema mkate wopanda cofufumitsa ndi kugawila atumwi ake. Pa Cikumbutso ca pa April 14, mudzaona mkate wopanda cofufumitsa wonyema-nyema umene adzaika m’mbale.

16 Pemphelo lacidule lidzapelekedwa ndiyeno mbale za mkate adzazipititsamo mwadongosolo, mogwilizana ndi mikhalidwe yakumaloko. Padzakhala mbale zokwanila n’colinga cakuti pasadzapite nthawi yaitali kupititsa mkate kwa onse opezeka pacikumbutso. Sipadzakhala mwambo uliwonse wapadela pocita zimenezi. Padzakhala anthu ocepa cabe (mwina sipadzakhala aliyense) amene adzadya mkate monga mmene zinalili pacikumbutso ca caka catha ca 2013.

17. Kodi malangizo a Yesu ponena za vinyo amatsatilidwa bwanji pa Cikumbutso?

17 Pambuyo pake, mkambi adzafotokoza zimene Mateyu analemba kuti: “[Yesu] anatenga kapu ndipo atayamika, anaipeleka kwa iwo n’kunena kuti: ‘Imwani nonsenu. Vinyoyu akuimila ‘magazi anga a pangano,’ amene adzakhetsedwa cifukwa ca anthu ambili kuti macimo akhululukidwe.’” (Mat. 26:27, 28) Motsatila citsanzo cimeneci, padzapelekedwa pemphelo lina ndiyeno adzapititsa makapu a vinyo wofiila m’gulu.

18. Ngakhale kuti ndi anthu ocepa cabe amene angadye zizindikilo ndipo mwina sipangale aliyense wakudya, n’cifukwa ciani tiyenela kupezeka pa Cikumbutso?

18 Pamene zizindikilo zimenezi zikupititsidwa, anthu ambili amene amafika pa mwambowu samadya zizindikilo zimenezi. Zili conco cifukwa cakuti Yesu anakamba kuti ndi okhawo amene adzalamulila naye mu Ufumu wakumwamba amene ayenela kuzidya. (Ŵelengani Luka 22: 28-30; 2 Tim. 4:18) Anthu ena onse amene amapezeka pa Cikumbutso amangoonelela mwaulemu. Komabe, kupezeka pa Mgonelo wa Ambuye n’kofunika, cifukwa cakuti kupezekapo kwathu pa mwambowu kumasonyeza kuti timayamikila kwambili kufunika kwa nsembe ya Yesu. Pa Cikumbutso, timaganizila kwambili za madalitso amene tili nao cifukwa ca nsembe ya dipo imeneyi. Tili ndi ciyembekezo cokhala pakati pa “khamu lalikulu” la anthu amene adzapulumuka “citsautso cacikulu.” Olambila Mulungu amenewa adzakhala ‘atacapa mikanjo yao ndi kuiyeletsa m’magazi a Mwanawankhosa.’—Chibv. 7:9, 14-17.

19. Kodi muyenela kucita ciani kuti mukonzekele bwino ndi kuti mukapindule ndi Mgonelo wa Ambuye?

19 Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zimakonzekela kucita mwambo wapadela umenewu. Kukadzatsala milungu yocepa kuti ticite Cikumbutso, tidzaitanila anthu ambili kuti akapezeke pa mwambo umenewu. Ndiponso, kukadzatsala masiku ocepa kuti cikumbutso cicitike, tidzaŵelenga zimene Yesu anacita ndi zimene zinacitika pa madeti ofafanana ndi a mu 33 C.E. Tikonzeletu zinthu zina ndi zina paumoyo wathu kuti tisadzaphonye cikumbutso cimeneci. Tifunika kufika pa mwambowu nyimbo yoyamba ndi pemphelo loyamba zisanacitike n’colinga cakuti tikalandile alendo ndiponso kupindula ndi pulogalamu yonse. Pamene mkambi apeleka nkhani ya Cikumbutso, tonse opezekapo kuphatikizapo alendo, tidzafunika kutsatila m’ma Baibo athu pamene mkambi aŵelenga malemba ndi kuwafotokoza. Koposa zonse, kupezeka kwathu pa Cikumbutso kudzasonyeza kuti timayamikila kwambili nsembe ya Yesu ndi kuti timamvela lamulo lake lakuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.”—1 Akor. 11:24.

[Mau apansi]

a Katswili wina wa ku German wochedwa Heinrich Meyer anati: “Poona . . . kuti thupi la Yesu linali lathunthu (kutanthauza kuti anali wamoyo), ndipo magazi ake anali asanakhetsedwe, palibe aliyense [atumwi] amene akananena . . . kuti akudyadi thupi leni-leni kapena kumwa magazi eni-eni a Ambuye. Ndipo Yesu sakanafuna kuti mau akewo amvedwe mwa njila yolakwika imeneyo cifukwa anali kudziwa kuti ophunzila ake sakanavomeleza zimenezo.”

CIKUMBUTSO CA 2014

Mwezi umazungulila dziko kamodzi pamwezi. Pa nthawi ina mwezi ukamazungulila dziko, umadzafika pena pamene umakhala pakati pa dziko ndi dzuŵa. Panthawi imeneyi, mwezi sumaonekela mpaka pambuyo pa maola 18 kufika 30. Zikakhala conco m’pamene timati “mwezi wakhala.”

Mu 2014, mwezi wina watsopano udzaonekela pa March 30, ndi nthawi ya 8:45 p.m. (20:45), mogwilizana ndi nthawi ya ku Yerusalemu. Limeneli lidzakhala deti loyandikana kwambili ndi March 20 kapena 21 pamene tsiku limakhala ndi maola 12 m’masana ndi 12 usiku. Tsiku lotsatila (March 31), ku Yerusalemu dzuŵa lidzaloŵa pambuyo pa maola 21. Koma tsiku la Nisani 1 silidzayamba patsikulo. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti panthawiyo mwezi sudzaonekela ku Yerusalemu. Komabe mwezi udzaonekela pa April 1 dzuŵa likadzaloŵa. Conco, tikaŵelengetsa masiku monga mmene Ayuda anali kucitila, tikhoza kunena kuti tsiku la Nisani 1 lidzayamba pa April 1 dzuŵa likadzaloŵa.

Motelo, Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zikudziŵa kuti tsiku la Nisani 14 lidzayamba dzuŵa likadzaloŵa pa Mande April 14, 2014. Panthawiyo, mwezi udzakhala wathunthu.—Kuti mumve zambili za mmene timadziŵila deti la Cikumbutso, onani Nsanja ya Olonda yacingelezi ya June 15, 1977, tsamba 383 mpaka 384.

[Cithunzi papeji 25]

Atumwi anamwa vinyo amene anali kuimila magazi a Yesu a pangono (Onani ndime 11 ndi 12)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani