LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 11/1 masa. 7-11
  • “Khalani Maso Kuti Musanyalanyaze Kupemphela”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Khalani Maso Kuti Musanyalanyaze Kupemphela”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUZIPEMPHELA MWA MTUNDU ULIWONSE WA PEMPHELO
  • “PEMPHELANI KOSALEKEZA”
  • YEHOVA ANAYANKHA MAPEMPHELO A NEHEMIYA
  • MUZIPEMPHELELA ENA
  • “CIPULUMUTSO CATHU CILI PAFUPI”
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 11/1 masa. 7-11

“Khalani Maso Kuti Musanyalanyaze Kupemphela”

“Khalani oganiza bwino, ndipo khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphela.”—1 PET. 4:7.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi ndi mapemphelo a mtundu uti amene inu panokha mufunika kupeleka kaŵili-kaŵili?

N’cifukwa ciani Akristu oona ayenela kupemphela kosalekeza?

Ndani amene amapindula pamene inuyo mupemphelela ena?

1, 2. (a) N’cifukwa ciani tifunika ‘kukhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphela’? (b) Kodi ndi mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa ponena za pemphelo?

MUNTHU wina amene anali kugwila nchito ya ulonda anati: “Kukhala maso kumavuta kwambili pa nthawi imene kunja kuli pafupi kuca.” Ndithudi, anthu ena amene anagwilako nchito imeneyi angavomeleze mfundo imeneyi. Tingayelekezele zimenezi ndi nthawi imene tikukhalamo. Dziko la Satana lili pafupi kutha, ndipo anthu ambili ali m’tulo tofa nato mwa kuuzimu. N’cifukwa cake Akristu afunikila kucita khama kuti akhalebe maso. (Aroma 13:12) Kugona mwakuuzimu nthawi ino yamapeto ndi koopsa kwambili. Motelo, tifunika ‘kukhala oganiza bwino’ ndi kumvela malangizo a m’Malemba akuti: “Khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphela.”—1 Pet. 4:7.

2 Popeza kuti tikukhala m’masiku otsiliza, tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakonda kupemphela? Kodi ndimapemphela nthawi zonse ndiponso mwa mtundu uliwonse wa pemphelo? Kodi ndimakonda kupemphelela ena, kapena ndimakonda kupempha zofuna zanga zokha? Kodi pemphelo ndi lofunika motani kuti ndikapulumuke?’

MUZIPEMPHELA MWA MTUNDU ULIWONSE WA PEMPHELO

3. Kodi mitundu ina ya mapemphelo ndi iti?

3 Polembela Akristu a ku Aefeso, mtumwi Paulo analemba kuti: “Muzipemphela . . . mwa mtundu uliwonse wa pemphelo.” (Aef. 6:18) Nthawi zambili timapempha Yehova kuti atithandize kupeza zinthu zofunika pa umoyo ndi kulimbana ndi mavuto. Pokhala ndi “Wakumva pemphelo,” iye amamvetsela mwacikondi pamene tipempha thandizo. (Sal. 65:2) Komabe, tiyenela kuyesetsa kupeleka mapemphelo a mitundu ina monga mapemphelo a citamando, a ciyamiko ndi opembedzela.

4. N’cifukwa ciani tiyenela kutamanda Yehova nthawi zonse m’mapemphelo athu?

4 Pali zifukwa zambili zimene tifunika kupelekela mapemphelo a citamando kwa Yehova. Mwacitsanzo, timamutamanda tikaganizila “nchito zake zamphamvu” ndi “ukulu wake wosaneneka.” (Ŵelengani Salimo 150:1-6.) M’mavesi 6 a Salimo 150, timapezamo mau 13 otilimbikitsa kutamanda Yehova. Wamasalimo wina anaonetsa kuti anali kukonda kwambili Mulungu mwa kuimba kuti: “Ndimakutamandani maulendo 7 pa tsiku cifukwa ca zigamulo zanu zolungama.” (Sal. 119:164) Ndithudi, Yehova ndi woyenela kutamandidwa. Conco, tiyenela kum’tamanda m’mapemphelo athu “maulendo 7 pa tsiku,” kutanthauza nthawi zambili.

5. Kodi kuyamikila Mulungu popemphela kuli ndi phindu lotani?

5 Mtundu wina wa pemphelo umene ndi wofunika kwambili ndi pemphelo la ciyamiko. Paulo analangiza Akristu a ku Filipi kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” (Afil. 4:6) Tikukhala m’masiku otsiliza a dziko lino la Satana ndipo anthu ambili ndi “osayamika.” Conco, kuti tisakhale ngati anthu a m’dzikoli, tifunika kuyamikila Yehova kucokela pansi pa mtima pa zabwino zonse zimene amaticitila. (2 Tim. 3:1, 2) Dzikoli ladzala ndi mzimu wosayamika. Cotelo tifunikila kukhala osamala kuti tisakhale ndi mzimu umenewu. Kuyamikila Mulungu m’pemphelo kumatithandiza kukhala osangalala ndiponso kupewa ‘kung’ung’udza ndi kudandaula za umoyo wathu.’ (Yuda 16) Komanso pamene mutu wa banja amayamikila Mulungu popemphela ndi banja lake, amalimbikitsa mkazi wake ndi ana ake kukhala oyamikila.

6, 7. Kodi pembedzelo n’ciani? Ndipo tingapembedzele Yehova pa nkhani ziti?

6 Pembedzelo ndi pemphelo locokela pansi pa mtima ndiponso lopelekedwa mokhudzika mtima kwambili. Kodi tingapembedzele Yehova pa nkhani ziti? Tingacite zimenezi pamene tikuzunzidwa kapena pamene tikudwala matenda a kaya-kaya. Pa nthawi zotelo, timapembedzela Mulungu kuti atithandize. Koma kodi tiyenela kucita zimenezi kokha pamene tikuzunzidwa kapena kudwala?

7 Ganizilani zimene Yesu anakamba m’pemphelo lacitsanzo zokhudza dzina la Mulungu, Ufumu Wake ndi cifunilo Cake. (Ŵelengani Mateyu 6:9, 10.) Anthu ambili m’dzikoli ali ndi makhalidwe oipa, ndipo maboma a anthu alephela kupatsa nzika zao zinthu zofunika paumoyo. Motelo, tifunikila kupemphela kuti dzina la Atate wathu wa kumwamba liyeletsedwe ndi kuti Ufumu wake uthetse ulamulilo wa Satana padzikoli. Ino ndi nthawi yofunika kupembedzela Yehova kuti akwanilitse cifunilo cake padziko lapansi monga kumwamba. Inde, tiyeni tikhale maso ndi kupemphela mwa mtundu uliwonse wa pemphelo.

“PEMPHELANI KOSALEKEZA”

8, 9. N’cifukwa ciani sitifunikila kuimba mlandu Petulo ndi atumwi ena kaamba kakuti anagona m’munda wa Getsemane?

8 Mtumwi Petulo analangiza Akristu kuti ‘akhale maso kuti asanyalanyaze kupemphela.’ Koma iye nthawi ina analephela kucita zimenezi. Iye ndi ophunzila ena anagona pamene Yesu anali kupemphela m’munda wa Getsemane. Ngakhale pamene Yesu anawauza kuti “khalani maso ndipo pemphelani kosalekeza,” io sanacite zimenezo.—Ŵelengani Mateyu 26:40-45.

9 Komabe, sitiyenela kumuimba mlandu Petulo ndi atumwi enawo cifukwa colephela kukhala maso. Tikutelo cifukwa cakuti tsiku limenelo io anali otopa kwambili. Madzulo a tsiku limenelo, iwo anakonza malo ocitila mwambo wa Pasika, ndi kucita mwambo umenewo. Kenako Yesu anayambitsa mwambo wa M’gonelo wa Ambuye, monga citsanzo ca zimene ophunzila ake ayenela kucita pokumbukila imfa yake. (1 Akor. 11:23-25) Baibo imati, “Atatha kuimba nyimbo zotamanda Mulungu, anatuluka n’kupita ku Phili la Maolivi,” ndipo anayenda mtunda wautali ndithu kudutsa ku Yerusalemu. (Mat. 26:30, 36) Mwacionekele, nthawi inali itadutsa kale pakati pa usiku. Tikanakhala m’munda wa Getsemane usiku umenewo, mwina ifenso tikanagona. Yesu sanadzudzule atumwiwo, koma anazindikila kufooka kwao ndipo anati: “Mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”

10, 11. (a) Kodi ndi phunzilo lotani limene Petulo anaphunzila m’munda wa Getsemane? (b) Kodi mwaphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila Petulo?

10 Petulo anaphunzila phunzilo losaiwalika pamene analephela kukhala maso m’munda wa Getsemane. Kumbukilani kuti madzulo a tsiku limeneli, Yesu anati: “Nonsenu muthawa ndi kundisiya ndekha usiku uno.” Atamva zimenezi, Petulo anati: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, ine ndekha sindingathawe!” Yesu anauza Petulo kuti: “Usiku womwe uno tambala asanalile, undikana katatu.” Modzidalila, Petulo anati: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” (Mat. 26:31-35) Koma Petulo anakana Yesu katatu monga mmene Yesu anakambila. Petulo anadzimvela cisoni cifukwa cokana Yesu, ndipo ‘analila mopwetekedwa mtima kwambili.’—Luka 22:60-62.

11 Petulo anatengapo phunzilo pa zimene zinam’citikila ndipo anathetsa cizolowezi cake cocita zinthu modzidalila. N’zoonekelatu kuti pemphelo ndi limene linathandiza Petulo kuthetsa vuto limeneli. Kodi tidziŵa bwanji zimenezi? Timadziŵa zimenezi cifukwa cakuti Petulo ndi amene analemba malangizo akuti “khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphela.” Kodi timatsatila malangizo amenewa ndi ‘kupemphela kosalekeza’? Kucita zimenezi kumaonetsa kuti timadalila Yehova. (Sal. 85:8) Tiyenelanso kukumbukila malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Amene akuyesa kuti ali cilili asamale kuti asagwe.”—1 Akor. 10:12.

YEHOVA ANAYANKHA MAPEMPHELO A NEHEMIYA

12. N’cifukwa ciani Nehemiya ndi citsanzo cabwino kwa ife?

12 Ganizilani Nehemiya amene anali wopelekela cikho kwa Mfumu Aritasasita ya Perisiya m’zaka za m’ma 400 B.C.E. Nehemiya ndi citsanzo cabwino pa nkhani yopemphela mocokela pansi pa mtima. Kwa masiku angapo, iye anali “kusala kudya ndi kupemphela pamaso pa Mulungu.” Iye anali kupemphelela Ayuda amene anali kuvutika ku Yerusalemu. (Neh. 1:4) Pamene Aritasasita anamufunsa cifukwa cake nkhope yake inali yacisoni ndiponso cimene anali kufuna kuti mfumuyo imucitile, ‘nthawi yomweyo [Nehemiya] anapemphela kwa Mulungu wakumwamba.’ (Neh. 2:2-4) Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? Yehova anayankha mapemphelo ake ndipo anathandiza anthu ake. (Neh. 2:5, 6) N’zosakaikitsa kuti zimenezi zinalimbitsa kwambili cikhulupililo ca Nehemiya.

13, 14. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tilimbitse cikhulupililo cathu ndi kugonjetsa ziyeso za Satana?

13 Kupemphela nthawi zonse monga mmene Nehemiya anacitila kumalimbitsa cikhulupililo cathu. Satana ndi wopanda cifundo ndipo nthawi zambili amatiyesa tikalefuka. Mwacitsanzo, pamene tikudwala kapena kuvutika maganizo, tingaone ngati sitikucita zambili potumikila Mulungu. Ena amavutika maganizo cifukwa ca zinthu zimene zinawacitikila m’mbuyomu. Satana amafuna kuti tizidziona monga osanunkha kanthu. Iye amacita zimenezi kuti afooketse cikhulupililo cathu. Koma ngati ‘timakhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphela,’ cikhulupililo cathu cimalimba. Zoonadi, ‘cishango cacikulu cacikhulupililo cidzatithandiza kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’—Aef. 6:16.

14 Ngati ‘tikhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphela,’ sitidzagonja pamene takumana ndi ciyeso. Tikakumana ndi mavuto kapena ciyeso, tiyenela kupemphela mwamsanga kwa Mulungu monga mmene Nehemiya anacitila. Tingagonjetse ziyeso kokha mwa thandizo la Yehova.

MUZIPEMPHELELA ENA

15. Kodi ndi mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa pa nkhani yopemphelela ena?

15 Yesu anapemphelela mtumwi Petulo kuti cikhulupililo cake cisathe. (Luka 22:32) Mkristu wina wa m’nthawi ya atumwi wochedwa Epafura, anatengela citsanzo ca Yesu mwa kupemphelela abale ake a ku Kolose mwakhama. Paulo analembela Akristu amenewo kuti: “Iye [Epafura] amakupemphelelani mwakhama nthawi zonse, kuti pomalizila pake mukhale okhwima mwauzimu ndi osakayika ngakhale pang’ono za cifunilo conse ca Mulungu.” (Akol. 4:12) Conco, tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimapemphelela abale ndi alongo anga mwakhama? Kodi ndimakonda kupemphelela Akristu ena amene akuvutika cifukwa ca ngozi zacilengedwe? Kodi ndili ndi cizolowezi copemphelela abale amene ali pa maudindo m’gulu la Yehova? Kodi pali wina amene akukumana ndi mavuto mumpingo amene ndingapemphelele?’

16. Kodi kupemphelela ena n’kofunika bwanji?

16 Abale athu amapindula kwambili ngati tiwapemphelela kwa Yehova Mulungu. (Ŵelengani 2 Akorinto 1:11.) Yehova samangoyankha mapemphelo cifukwa cakuti atumiki ake oculuka apempha cinacake mobweleza-bweleza. Koma iye amasangalala kuyankha mapemphelo a atumiki ake amene amapemphelela ena, poonetsa kuti amadela nkhawa anzao. Conco, tisanyalanyaze udindo ndi mwai wathu wopemphelela ena. Mofanana ndi Epafura, tikamapemphelela abale ndi alongo athu mwakhama timasonyeza kuti timawakonda ndi kuwadela nkhawa. Ngati ticita zimenezi, tidzakhala ndi cimwemwe coculuka cifukwa cakuti “kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—Mac. 20:35.

“CIPULUMUTSO CATHU CILI PAFUPI”

17, 18. Kodi ‘kukhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphela’ kungatithandize bwanji?

17 Paulo ananena kuti “usiku uli pafupi kutha, usana wayandikila.” Asananene izi, iye analemba kuti: “Nyengo ino mukuidziŵa, kuti tili kale mu ola lakuti mudzuke ku tulo, pakuti cipulumutso cathu cili pafupi kwambili tsopano kusiyana ndi nthawi imene tinakhala okhulupilila.” (Aroma 13:11, 12) Dziko latsopano limene Mulungu walonjeza lili pafupi, ndipo cipulumutso cathu cayandikila kwambili. Sitiyenela kugona mwakuuzimu ndi kulola zinthu za m’dzikoli kutidyela nthawi yopemphela kwa Yehova patokha. M’malo mwake, tifunika “kukhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphela.” Kucita zimenezi kudzatithandiza kuti ‘tizicita nchito zosonyeza kuti ndife odzipeleka kwa Mulungu’ pamene tikuyembekezela tsiku la Yehova. (2 Pet. 3:11, 12) Zocita zathu zingaonetse kuti tili maso mwakuuzimu ndi kuti timakhulupililadi kuti mapeto a dziko loipali ali pafupi. Conco, “muzipemphela mosalekeza.” (1 Ates. 5:17) Ndiponso tiyenela kupeza nthawi yopemphela patokha monga mmene Yesu anali kucitila. Ngati timatenga nthawi yaitali popemphela kwa Yehova patokha, tidzalimbitsa ubwenzi wathu ndi iye. (Yak. 4:7, 8) Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndi cinthu camtengo wapatali kwambili.

18 Malemba amati: “Pamene anali munthu, Kristu anapeleka mapemphelo opembedzela ndi opempha, kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa ku imfa. Anapeleka mapemphelowa mofuula komanso akugwetsa misozi, ndipo anamumvela cifukwa cakuti anali kuopa Mulungu.” (Aheb. 5:7) Yesu anapeleka mapemphelo opembedzela ndi opempha kwa Mulungu, ndipo anakhala wokhulupilika mpaka mapeto a moyo wake padziko lapansi. Pa cifukwa cimeneci, Yehova anapulumutsa Mwana wake wokondedwa ku imfa ndi kumupatsa mphoto ya moyo wosafa kumwamba. Ifenso tingathe kukhalabe okhulupilika kwa Atate wathu wakumwamba ngakhale titakumana ndi ziyeso kapena mavuto ena. Ndithudi, tidzapeza moyo wosatha ngati ‘tikhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphela.’

[Cithunzi papeji 9]

Ngakhale kuti Petulo anakana Yesu, iye anaphunzila ‘kukhala maso kuti asanyalanyaze kupemphela’ (Onani ndime 10 ndi 11)

[Zithunzi papeji 10]

‘Kukhala maso kuti tisanyalanyaze kupemphela’ kumatithandiza kulimbana ndi mavuto ndi ziyeso (Onani ndime 13 ndi 14)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani