UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kulalikila na Kuphunzitsa—N’kofunika pa Nchito Yopanga Ophunzila
Yesu analamula otsatila ake kuti apite kukapanga ophunzila. (Mat. 28:19) Izi ziphatikizapo kulalikila na kuphunzitsa. Conco, nthawi zonse timafunika kudzifunsa kuti, ‘Ningacite ciani kuti nizicita bwino pa mbali zimenezi za nchito yopanga ophunzila?’
KULALIKILA
M’malo moyembekezela anthu kubwela kwa ise, tifunika kucita khama kusakila anthu ‘oyenelela.’ (Mat. 10:11) Pamene tilalikila, kodi timakhala chelu kuona mipata yokamba na anthu ‘amene tapeza’? (Mac. 17:17) Lidiya anakhala wophunzila cifukwa ca khama limene mtumwi Paulo anali nalo polalikila.—Mac. 16:13-15.
“Bzala mbeu zako m’maŵa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo.” (Mlal. 11:6)
TAMBANI VIDIYO YAKUTI PITILIZANI KULALIKILA “MWAKHAMA”—ULALIKI WAMWAYI, KUNYUMBA NDI NYUMBA, NDIYENO, YANKHANI MAFUNSO AYA:
M’zocita zake za tsiku na tsiku, kodi Samuel anaonetsa bwanji kuti anali na khama loshanga mbeu za coonadi?
N’cifukwa ciani tifunika kuyesetsa kucita maulaliki osiyana-siyana?
M’zocita zathu za tsiku na tsiku, n’ndani amene mungauzeko uthenga wabwino wa Ufumu?
KUPHUNZITSA
Kuti tipange ophunzila, timafunika kucita zambili osati kungosiila cabe anthu zofalitsa. Timafunika kupanga maulendo obwelelako na kutsogoza maphunzilo a Baibo kuti tiwathandize kukula kuuzimu. (1 Akor. 3:6-9) Nanga bwanji ngati tiyesetsa kuphunzitsa munthu coonadi ca Ufumu koma sapita patsogolo? (Mat. 13:19-22) Tifunika kupitiliza kufufuza anthu amene mitima yawo ili ngati ‘nthaka yabwino.’—Mat. 13:23; Mac. 13:48.
“Ineyo ndinabzala, Apolo anathilila, koma Mulungu ndiye anakulitsa” (1 Akor. 3:6)
TAMBANI VIDIYO YAKUTI PITILIZANI KULALIKILA “MWAKHAMA”—ULALIKI WAPOYELA, KUPANGA OPHUNZILA, NDIYENO, YANKHANI MAFUNSO AYA:
Kodi Solomon na Mary anathilila bwanji mbeu za coonadi mu mtima wa Ezekiel na Abigail?
Kodi tifunika kukhala na colinga canji pocita maulaliki osiyana-siyana, kuphatikizapo ulaliki wapoyela?
Kodi tingacite bwanji kuti tizicita khama pophunzitsa ena coonadi?