LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 7/1 masa. 15-20
  • “Dziŵani Kuti Ine Ndili Pamodzi Ndi Inu masiku Onse”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Dziŵani Kuti Ine Ndili Pamodzi Ndi Inu masiku Onse”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUSAMALIDWA BWINO NDI YESU
  • MTHENGA ‘AKONZA NJILA’
  • ZAKA ZA KUYENDELA NDI KUYELETSA
  • KODI CINACITIKA N’CIANI PAMENE NTHAWI YOKOLOLA INAYAMBA?
  • MAPINDU AMENE TIKUPEZA
  • Fanizo la Tiligu ndi Namsongole
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • “Ufumu Wanu Ubwele”
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 7/1 masa. 15-20

“Dziŵani Kuti Ine Ndili Pamodzi Ndi Inu masiku Onse”

“Dziŵani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.”—MAT. 28:20.

PEZANI MAYANKHO A MAFUNSO AWA:

N’cifukwa ciani tinganene kuti kucokela m’nthawi za atumwi mpaka masiku ano, padziko lapansi nthawi zonse pakhala Akristu odzozedwa?

Kodi ndi kuyendela kotani kumene Yesu anacita kuyambila mu 1914?

Kodi ndi zocitika zotani zimene zili m’fanizo la Yesu la tiligu ndi namsongole zimene zidzacitika mtsogolo?

1. (a) Mwacidule, fotokozani fanizo la tiligu ndi namsongole. (b) Kodi Yesu anafotokoza bwanji tanthauzo lake?

LIMODZI mwa mafanizo a Ufumu a Yesu limafotokoza za mlimi amene anafesa mbeu zabwino za tiligu m’munda wake, ndi za mdani amene anafesa namsongole m’munda wa tiligu umenewo. Namsongole anakula kuposa tiligu, koma mlimiyo analamula akapolo ake kuti, “zilekeni zonse zikulile pamodzi mpaka nthawi yokolola.” Panthawi yokolola, namsongole anaonongedwa ndipo tiligu anasonkhanitsidwa. Yesu mwiniyo anafotokoza tanthauzo la fanizo limeneli. (Ŵelengani Mateyu 13:24-30, 37-43.) Kodi fanizo limeneli limavumbula ciani? (Onani bokosi lakuti “Tiligu ndi Namsongole.”)

2. (a) Kodi zimene zinacitika m’munda wa mlimi zimaimila ciani? (b) Kodi tidzakambilana mbali iti ya fanizo la tiligu ndi namsongole?

2 Zocitika m’munda wa mlimi zimaonetsa mmene Yesu adzasonkhanitsila gulu la anthu amene ali monga tiligu kucokela pakati pa mtundu wa anthu, ndi nthawi imene adzacita zimenezo. Anthu amenewa ndi Akristu odzozedwa amene adzalamulila pamodzi ndi iye mu Ufumu. Kufesa kumeneku kunayamba pa Pentekosite mu 33 C.E. Kusonkhanitsa kudzatha pamene odzozedwa amene adzakhala ndi moyo kumapeto kwa dongosolo lino la zinthu adzalandila cidindo cao comaliza, kenako n’kutengedwa kupita kumwamba. (Mat. 24:31; Chiv. 7:1-4) Munthu akakwela pamwamba pa phili, akhoza kuona mosavuta malo omuzungulila ngakhale amene ali patali. Mofanana ndi zimenezi, fanizoli limatithandiza kudziŵa bwino zinthu zimene zinali kudzacitika zaka 2000 kucokela pamene Yesu ananena fanizoli. Malinga ndi fanizoli, kodi ndi zocitika zotani zokhudza Ufumu zimene tadziŵa? Fanizo limeneli limafotokoza za nthawi yofesa, yakuti zikule ndi yokolola. Nkhani ino idzafotokoza maka-maka za nthawi yokolola.a

KUSAMALIDWA BWINO NDI YESU

3. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene zinacitika kuciyambi kwa zaka za m’ma 100 C.E.? (b) Malinga ndi Mateyu 13:28, kodi ndi funso lotani limene linabuka? Ndipo ndani amene analifunsa? (Onaninso mau akumapeto.)

3 Kuciyambi kwa zaka za m’ma 100 C.E., ‘namsongole anaonekela’ pamene anthu odzicha Akristu anaonekela m’munda wa dziko lapansi. (Mat. 13:26) Pofika m’zaka za m’ma 300 C.E., Akristu amene anali monga namsongole anaculuka kwambili kuposa Akristu odzozedwa. Kumbukilani kuti m’fanizo limenelo, akapolo anapempha mbuye wao kuti awalole kuti azule namsongole.b (Mat. 13:28) Kodi iye anawayankha bwanji?

4. (a) Kodi yankho la Yesu amene ndi Mbuye, limavumbula ciani? (b) Kodi Akristu amene ali monga tiligu anaonekela liti?

4 Ponena za tiligu ndi namsongole, Yesu anati: “Zilekeni zonse zikulile pamodzi mpaka nthawi yokolola.” Mau amenewa amaonetsa kuti kucokela m’nthawi za atumwi mpaka masiku ano, padziko lapansi nthawi zonse pakhala Akristu odzozedwa amene ali monga tiligu. Cimene cionetsa kuti mfundo imeneyo ndi yoona, ndi mau amene Yesu anauza ophunzila ake pambuyo pake akuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Conco, mau amenewa anaonetsa kuti Akristu odzozedwa adzatetezedwa ndi Yesu masiku onse kufikila nthawi yamapeto. Koma popeza Akristu amene anali monga namsongole anaculuka kuposa Akristu odzozedwa, sitidziŵa bwino-bwino amene anali m’gulu la tiligu pa nyengo yaitali imeneyo. Komabe, zaka zambili nthawi yokolola isanafike, gulu la tiligu linaonekela. Kodi zimenezo zinacitika bwanji?

MTHENGA ‘AKONZA NJILA’

5. Kodi ulosi wa Malaki unakwanilitsidwa bwanji m’nthawi ya atumwi?

5 Zaka zambili Yesu asanakambe fanizo la tiligu ndi namsongole, Yehova anauzila mneneli wake Malaki kulosela zocitika zimene zimagwilizana ndi fanizo la Yesu. (Ŵelengani Malaki 3:1-4.) Yohane Mbatizi ndiye anali ‘mthenga amene anakonza njila.’ (Mat. 11:10, 11) Pamene Yohane anabwela mu 29 C.E., nthawi yoweluza mtundu wa Aisiraeli inali itayandikila. Yesu anali mthenga waciŵili. Iye anayeletsa kacisi ku Yerusalemu kaŵili. Nthawi yoyamba ndi pamene anayamba ulaliki wake, ndipo yaciŵili ndi ca kumapeto kwa ulaliki wake. (Mat. 21:12, 13; Yoh. 2:14-17) Conco, nchito ya Yesu yoyeletsa inatenga zaka.

6. (a) Kodi kukwanilitsika kwakukulu kwa ulosi wa Malaki ndi kotani? (b) Kodi Yesu anayendela liti kacisi wa kuuzimu? (Onani mau akumapeto.)

6 Kodi kukwanilitsika kwakukulu kwa ulosi wa Malaki ndi kotani? Kwa zaka zambili 1914 isanafike, M’bale C. T. Russell ndi anzake anagwila nchito yofanana ndi imene Yohane Mbatizi anagwila. Nchito yofunika kwambili imeneyo inali yobwezeletsa coonadi ca m’Baibo. Ophunzila Baibo anaphunzitsa tanthauzo leni-leni la nsembe ya dipo la Kristu, anavumbula kuti ciphunzitso ca moto wa helo ndi conama, ndipo analalikila za kutha kwa Nthawi za Akunja. Komabe, panali magulu ambili azipembedzo amene anali kudzicha kuti ndi otsatila a Kristu. Motelo, funso lofunika kwambili limene linafunika kuyankhidwa ndi lakuti, Kodi ndani anali tiligu pakati pa magulu amenewo? Kuti funso limenelo liyankhidwe, Yesu anayamba kuyendela kacisi wauzimu mu 1914. Nchito yoyendela ndi yoyeletsa imeneyo inatenga zaka, ndipo inayamba mu 1914 mpaka kuciyambi kwa 1919.c

ZAKA ZA KUYENDELA NDI KUYELETSA

7. Kodi Yesu anapeza ciani pamene anayamba kuyendela kwake mu 1914?

7 Pamene Yesu anayamba kuyendela kwake, kodi anapeza ciani? Anapeza kagulu kocepa ka Ophunzila Baibo acangu, amene kwa zaka zoposa 30 anali kugwilitsila nchito mphamvu zao ndi cuma cao kupititsa patsogolo nchito yolalikila.d Mwacionekele, Yesu ndi angelo anakondwela kwambili kupeza anthu ocepa amenewo amene anali monga tiligu okhwima, cifukwa cakuti namsongole wa Satana sanawalepheletse kukula. Ngakhale ndi conco, panali kufunika ‘kuyeletsa ana a Levi,’ amene ndi Akristu odzozedwa. (Mal. 3:2, 3; 1 Pet. 4:17) N’cifukwa ciani panafunika kucita zimenezo?

8. Kodi n’ciani cinacitika pambuyo pa 1914?

8 Kumapeto kwa 1914, Ophunzila Baibo ena anakhumudwa cifukwa cakuti sanapite kumwamba. M’zaka za 1915 ndi 1916, citsutso cocokela kunja kwa gulu cinabweza m’mbuyo nchito yolalikila. Zinthu zinaipa kwambili maka-maka pamene M’bale Russell anamwalila mu October 1916, cifukwa citsutso cinayamba mkati mwa gulu. Atsogoleli anai mwa atsogoleli 7 a Watch Tower Bible and Tract Society, anakana kuti M’bale Rutherford akhale wotsogolela gulu. Iwo anayesa kupangitsa magaŵano pakati pa abale, koma mu August 1917, io anacoka pa Beteli. Kumeneku kunali kuyeletsa ndithu. Ndiponso, Ophunzila Baibo ena anagonja cifukwa coopa anthu. Koma monga gulu, Ophunzila Baibo anacita zinthu mogwilizana ndi nchito yoyeletsa ya Yesu ndipo anapanga masinthidwe ofunikila. Conco, Yesu anaona kuti io anali Akristu oona amene anali monga tiligu, ndipo iye anakana Akristu onse onama kuphatikizapo anthu onse amene anali m’machalichi Acikristu. (Mal. 3:5; 2 Tim. 2:19) Kodi n’ciani cinacitika pambuyo pake? Kuti tipeze yankho, tiyeni tibwelelenso ku fanizo lija la tiligu ndi namsongole.

KODI CINACITIKA N’CIANI PAMENE NTHAWI YOKOLOLA INAYAMBA?

9, 10. (a) Kodi tsopano tidzakambitsilana ciani ponena za nthawi yokolola? (b) Pa nthawi yokolola, kodi n’ciani cinali coyamba kucitika?

9 Yesu anati: “Nthawi yokolola ikuimila mapeto a nthawi ino.” (Mat. 13:39) Nthawi yokolola imeneyo inayamba mu 1914. Tidzakambitsilana zocitika zisanu zimene Yesu ananenelatu zokhudza nthawi imeneyo.

10 Coyamba, kusonkhanitsa namsongole. Yesu anati: “M’nyengo yokolola ndidzauza okololawo kuti, Coyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga m’mitolo.” Pambuyo pa 1914, angelo anayamba ‘kusonkhanitsa’ Akristu amene anali monga namsongole mwa kuwasiyanitsa ndi odzozedwa amene ndi “ana a ufumu.”—Mat. 13:30, 38, 41.

11. Kodi n’ciani cakhala cikusiyanitsa Akristu oona ndi onama kuyambila kale?

11 Pamene nchito yosonkhanitsa inali mkati, kusiyana pakati pa magulu aŵili amenewo kunaonekela kwambili. (Chiv. 18:1, 4) Pofika mu 1919, zinaonekelatu kuti Babulo Wamkulu wagwa. Kodi n’ciani kweni-kweni cimene cinasiyanitsa Akristu oona ndi onama? Cinawasiyanitsa ndi nchito yolalikila. Abale amene anali kutsogolela Ophunzila Baibo anayamba kugogomeza kuti aliyense anafunika kutengako mbali m’nchito yolalikila za Ufumu. Mwacitsanzo, kabuku kakuti To Whom the Work Is Entrusted (Kwa Amene Apatsidwa Nchito) kamene kanafalitsidwa mu 1919, kanalimbikitsa Akristu onse odzozedwa kuti ayenela kulalikila kunyumba ndi nyumba. Kabuku kameneko kanati: “Nchito imeneyi ioneka yovuta, koma ndi ya Ambuye, ndipo mwa mphamvu zake tidzakwanitsa kuigwila. Muli ndi mwai wotengako mbali m’nchito imeneyi.” Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? Nsanja ya Olonda ya mu 1922, inakamba kuti, kucokela nthawi imeneyo Ophunzila Baibo anaonjezela cangu cao pa nchito yolalikila. Pasanapite nthawi yaitali, nchito yolalikila kunyumba ndi nyumba inakhala cizindikilo ca Akristu okhulupilika amenewo, ndipo ndi mmene zilili ngakhale masiku ano.

12. Kodi gulu la tiligu lakhala likusonkhanitsidwa kuyambila liti? Ndipo zimenezi zinayamba kucitika liti?

12 Caciŵili, kusonkhanitsa tiligu. Yesu analamula angelo ake kuti: “Mupite kukasonkhanitsa tiligu ndi kumuika m’nkhokwe yanga.” (Mat. 13:30) Kuyambila mu 1919, odzozedwa akusonkhanitsidwa mu mpingo wacikristu wokonzedwanso. Akristu odzozedwa amene adzakhalabe ndi moyo kumapeto kwa dongosolo lino la zinthu, adzasonkhanitsidwa komaliza pamene io adzalandila mphoto yao ya kumwamba.—Dan. 7:18, 22, 27.

13. Kodi lemba la Chivumbulutso 18:7 limavumbula kuti hule kapena Babulo Wamkulu, kuphatikizapo Machalichi Acikristu ali ndi maganizo otani masiku ano?

13 Cacitatu, kulila ndi kukukuta mano. Kodi n’ciani cinacitika pambuyo pakuti angelo amanga namsongole m’mitolo? Ponena zimene zidzacitikila gulu la anthu amene ali monga namsongole, Yesu anati: “Kumeneko adzalila ndi kukukuta mano.” (Mat. 13:42) Kodi zimenezo zikucitika panthawi ino? Iyai. Masiku ano, Machalichi Acikristu amene ali mbali ya hule, amadzinena kuti: “Ine ndine mfumukazi. Sindine mkazi wamasiye, ndipo sindidzalila ngakhale pang’ono.” (Chiv. 18:7) Inde, Machalichi Acikristu amadzimva kuti ali ndi mphamvu, ndipo amadziona kuti ‘ndi mfumukazi’ imene imayang’anila atsogoleli andale. Ndipo pakali pano, anthu amene amaimila namsongole sakulila koma amadzitukumula. Koma zimenezo zidzasintha posacedwapa.

14. (a) Kodi Akristu onama adzakukuta mano ao liti? Ndipo n’cifukwa ninji? (b) Kodi kamvedwe kathu katsopano ka Mateyu 13:42, kamagwilizana bwanji ndi mfundo ya pa Salimo 112:10? (Onani mau akumapeto.)

14 Panthawi ya cisautso cacikulu, pambuyo pakuti magulu onse a cipembedzo conama aonongedwa, mamembala ake akale adzafuna kuti akabisale, koma sadzapeza malo acitetezo kuti abisaleko. (Luka 23:30; Chiv. 6:15-17) Ndiyeno, pamene adzazindikila kuti alibe kothaŵila, adzalila posoŵa cocita ndipo ‘adzakukuta mano ao’ cifukwa caukali. Monga mmene Yesu ananenela mu ulosi wake wonena za cisautso cacikulu, panthawi ya mavuto imeneyo, io “adzadziguguda pacifuwa cifukwa ca cisoni.”e—Mat. 24:30; Chiv. 1:7.

15. Kodi n’ciani cidzacitikila namsongole? Ndipo zimenezo zidzacitika liti?

15 Cacinai, kuponyedwa m’ng’anjo yamoto. Kodi n’ciani cidzacitikila mitolo ya namsongole? Angelo ‘adzaiponya m’ng’anjo yamoto.’ (Mat. 13:42) Zimenezo zitanthauza cionongeko cothelatu. Conco, mamembala a magulu azipembedzo zonama adzaonongedwa pa Aramagedo, imene ndi mbali yomaliza ya cisautso cacikulu.—Mal. 4:1.

16, 17. (a) Kodi ndi cocitika comaliza citi cimene Yesu anachula m’fanizo lake? (b) N’cifukwa ciani tinganene kuti cocitika cimeneco cidzakwanilitsidwa mtsogolo?

16 Cacisanu, kuwala kwambili. Yesu anamaliza ulosi wake ndi mau awa: “Pa nthawi imeneyo olungama adzawala kwambili ngati dzuŵa mu ufumu wa Atate wao.” (Mat. 13:43) Kodi zimenezo zidzacitika liti, ndipo zidzacitikila kuti? Mau amenewa adzakwanilitsidwa mtsogolo. Yesu anali kunena za zinthu za mtsogolo zimene zidzacitika kumwamba, osati zimene zikucitika padziko lapansi tsopano.f Tiyeni tikambilane zifukwa ziŵili zimene tanenela conco.

17 Coyamba, kodi zimenezo zidzacitika liti? Yesu anati: “Pa nthawi imeneyo olungama adzawala.” Mwacionekele, mau akuti “pa nthawi imeneyo” amakamba za cocitika cimene Yesu anangonena kumene, cimene ndi ‘kuponya namsongole m’ng’anjo yamoto.’ Zimenezo zidzacitika pa mbali yomaliza ya cisautso cacikulu. Motelo, ‘kuwala kwambili’ kwa odzozedwa kuyenela kuti kudzacitika mtsogolo. Caciŵili, kodi zimenezo zidzacitikila kuti? Yesu anakamba kuti olungama ‘adzawala mu ufumu.’ Kodi zimenezo zitanthauza ciani? Zitanthauza kuti Akristu odzozedwa onse okhulupilika amene adzakhala ali padziko lapansi mbali yoyamba ya cisautso cacikulu ikadzatha, adzakhala atalandila kale cidindo cao comaliza. Ndiyeno, monga mmene ulosi wa Yesu wonena za cisautso cacikulu umaonetsela, io adzatengedwa kupita kumwamba. (Mat. 24:31) Kumeneko io adzawala “mu ufumu wa Atate wao,” ndipo mwamsanga pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, io adzasangalala monga mkwatibwi wa Yesu pa “ukwati wa Mwanawankhosa.”—Chiv. 19:6-9.

MAPINDU AMENE TIKUPEZA

18, 19. Kodi kumvetsetsa fanizo la Yesu la tiligu ndi namsongole kumatipindulitsa bwanji?

18 Kodi ifeyo tikupindula bwanji ndi mmene fanizo limeneli lamveketsela bwino zinthu? Tapindula ndi fanizo limeneli m’njila zitatu. Coyamba, latithandiza kumvetsetsa cifukwa cacikulu cimene Yehova walolela kuipa. Iye “analekelela . . . ziwiya za mkwiyo” kuti akonze “ziwiya zacifundo” zimene ndi gulu la tiligu.g (Aroma 9:22-24) Caciŵili, fanizo limeneli limalimbikitsa cikhulupililo cathu. Pamene mapeto ayandikila, adani athu adzamenyana nafe zolimba, “koma sadzapambana” (Ŵelengani Yeremiya 1:19.) Monga mmene Yehova anatetezela gulu la anthu amene anali monga tiligu, Atate wathu wakumwamba kupyolela mwa Yesu ndi angelo adzakhala nafe “masiku onse” mpaka mtsogolo.—Mat. 28:20.

19 Cacitatu, fanizo limeneli limatithandiza kudziŵa gulu la tiligu. N’cifukwa ciani kudziŵa zimenezo n’kofunika kwambili? Kudziŵa Akristu amene ali monga tiligu n’kofunika kuti tipeze yankho la funso limene Yesu anafunsa mu ulosi wake waukulu wonena za masiku otsiliza. Iye anafunsa kuti: “Ndani kweni-kweni amene ali kapolo wokhulupilika ndi wanzelu?” (Mat. 24:45) Nkhani ziŵili zotsatila zidzapeleka yankho lokhutilitsa la funso limenelo.

MAU AKUMAPETO: (Mau awa aŵelengedwe monga mau a munsi poŵelenga ndime zake.)

[Mau apansi]

a Ndime 2: Kuti mumvetsetse tanthauzo la mbali zina za fanizo limeneli, tikulimbitsani kuŵelenga nkhani yakuti, “Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuŵa,” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2010.

b Ndime 3: Popeza atumwi a Yesu anali atafa ndipo odzozedwa amene anali padziko lapansi sanawayelekezele ndi akapolo koma anawayelekezela ndi tiligu, akapolo amenewa amaimila angelo. Cakumapeto kwa fanizo limeneli, Yesu ananena kuti, okolola namsongole ndi angelo.—Mat. 13:39.

c Ndime 6: Kumeneku ndi kusintha kwa kamvedwe kathu. Kale tinali kukhulupilila kuti kuyendela kwa Yesu kunacitika mu 1918.

d Ndime 7: Kucokela mu 1910 mpaka mu 1914, Ophunzila Baibo anafalitsa mabuku pafupi-fupi 4,000,000 ndiponso tumapepala twauthenga ndi tumabuku toposa 200,000,000.

e Ndime 14: Kumeneku ndi kusintha kwa kamvedwe kathu ka lemba la Mateyu 13:42. M’mbuyomu, zofalitsa zathu zinali kufotokoza kuti Akristu onama akhala akulila ndi kukukuta mano kwa zaka zambili cifukwa cakuti, “ana a ufumu” akhala akuwavumbula kuti io ndi “ana a woipayo.” (Mat. 13:38) Komabe, zimene tiyenela kudziŵa ndi zakuti, kukukuta mano kumeneku ndi kogwilizana ndi cionongeko.—Sal. 112:10.

f Ndime 16: Lemba la Danieli 12:3 limakamba kuti “Anthu ozindikila [Akristu odzozedwa] adzawala ngati kuwala kwa kuthambo.” Akali padziko lapansi, io amacita zimenezi mwa kutengako mbali mu nchito yolalikila. Koma Mateyu 13:43 imakamba za nthawi pamene io adzawala kwambili mu Ufumu wakumwamba. Poyamba, tinali kukhulupilila kuti malemba onse aŵili amenewa amanena za nchito yolalikila.

g Ndime 18: Onani buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, patsamba 288-289.

[Chati papeji 16, 17]

TILIGU NDI NAMSONGOLE

33 C.E. KUFESA KUYAMBA

WOFESA: Yesu

KUFESA MBEU ZABWINO: Kudzoza ndi mzimu woyela

MUNDA: Anthu padziko lapansi

‘Munthu anafesa mbeu zabwino m’munda wake’ (Mat. 13:24)

MDANI: Mdyelekezi

ANTHU ANALI M’TULO: Kufa kwa atumwi

‘Pamene anthu anali m’tulo, mdani anafesa namsongole pakati pa tiligu’ (Mat. 13:25)

TILIGU: Akristu Odzozedwa

NAMSONGOLE: Akristu Onama

“Zonse zikulile pamodzi mpaka nthawi yokolola” (Mat. 13:30)

1914 KUKOLOLA KUYAMBA

AKAPOLO/ OKOLOLA: Angelo

Akristu amene ali monga namsongole asiyanitsidwa ndi “ana a ufumu” odzozedwa

Namsongole asonkhanitsidwa ndi kumumanga m’mitolo (Mat. 13:30)

(Onani ndime 10 ndi 11)

1919 KUSONKHANITSA NDI KUIKA M’NKHOKWE: Akristu odzozedwa asonkhanitsidwa mumpingo wokonzedwanso

KUKOLOLA

‘Kusonkhanitsa tiligu ndi kumuika m’nkhokwe’ (Mat. 13:30)

(Onani ndime 12)

ARAMAGEDO

At Armageddon, the weeds are pitched into the fire

KUWALA KWAMBILI

Kukangotsala pang’ono kuti Aramagedo iyambe, Akristu odzozedwa okhulupilika amene adzakhala akali padziko lapansi adzatengedwa kupita kumwamba

Olungama adzawala kwambili mu Ufumu (Mat. 13:43) (Onani ndime 16 ndi 17)

Namsongole aponyedwa m’ng’anjo ya moto (Mat. 13:42) (Onani ndime 15)

[Cithunzi papeji 19]

Mgwilizano wolimba wa Machalichi Acikristu ndi atsogoleli andale udzatha posacedwapa

(Onani ndime 13)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani