LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp21 na. 1 masa. 8-9
  • N’cifukwa Ciani Mulungu Sayankha Mapemphelo Onse?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Mulungu Sayankha Mapemphelo Onse?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Gao 11
    Mvetselani kwa Mulungu
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
wp21 na. 1 masa. 8-9

N’cifukwa Ciani Mulungu Sayankha Mapemphelo Onse?

Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu, ni wokonzeka kumva mapemphelo athu ocokela pansi pa mtima ndipo amakondwela kutelo. Koma pali zinthu zina zimene zingapangitse kuti iye asamvetsele mapemphelo athu. Kodi zinthu zimenezo ni ziti? Nanga tiyenela kukumbukila ciani pamene tipemphela? Onani malangizo ena awa a m’Baibo.

Gulu la anthu m’chechi likupemphela mokweza mwa kuŵelenga pemphelolo m’buku la mapemphelo.

“Iwe popemphela, usanene zinthu mobwelezabweleza.”—Mateyu 6:7.

Yehova safuna kuti tizipeleka mapemphelo oloŵeza pamtima kapena ocita kuwaŵelenga m’buku. Koma amafuna kuti tizikamba naye kucokela mumtima. Kodi mungamvele bwanji ngati mnzanu amabwela na kukuuzani mawu amodzi-modzi tsiku lililonse? Simungamvele bwino. Mabwenzi abwino amakambilana momasuka komanso moona mtima. Ngati tikamba mawu athu-athu popemphela kwa Atate wathu wakumwamba, zimaonetsa kuti timamuona kuti ni bwenzi lathu.

Mwamuna akuyang’ana kumwamba pamene akupala khadi ya njuga.

“Mumapempha koma simulandila, cifukwa mukupempha ndi colinga coipa.”—Yakobo 4:3.

Tidziŵa kuti Mulungu sangayankhe mapemphelo athu ngati tipempha zinthu zimene amaletsa. Mwacitsanzo, kodi Yehova angayankhe pemphelo la munthu wanjuga lopempha kuti awine njugayo pamene iye amaletselatu kucita zinthu mwadyela komanso kukhulupilila mulungu wamwayi? (Yesaya 65:11; Luka 12:15) Ndithudi, Yehova sangayankhe mapemphelo otelo! Conco, kuti Mulungu ayankhe mapemphelo athu, tifunika kuonetsetsa kuti zimene tipempha n’zogwilizana na zimene iye amatiuza m’Baibo.

M’busa akupemphelela gulu la asilikali.

“Munthu amene amathaŵitsa khutu lake kuti asamve cilamulo, ngakhale pemphelo lake limakhala lonyansa.”—Miyambo 28:9.

M’nthawi yakale, Mulungu sanali kuyankha mapemphelo a anthu amene sanali kumvela malamulo ake olungama. (Yesaya 1:15, 16) Iye sanasinthe. (Malaki 3:6) Ngati tifuna kuti Mulungu azimvetsela mapemphelo athu, tiyenela kuyesetsa kumvela malamulo ake. Koma bwanji ngati tinacitapo zinthu zinazake zoipa m’mbuyomo? Kodi ndiye kuti basi Yehova sadzamvetselanso mapemphelo athu? Iyai! Iye adzatikhululukila ngati titembenuka na kuyesetsa kucita zinthu zomukondweletsa.—Machitidwe 3:19.

“Aliyense wofika kwa Mulungu ayenela kukhulupilila kuti iye alikodi, ndi kuti amapeleka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.”—Aheberi 11:6.

Mzimayi akuŵelenga Baibo.

Colinga ca kupemphela si cakuti timveleko bwino cabe tikakumana na mavuto kapena tikakhala na nkhawa. Kupemphela ni njila yoonetsela kuti tili na cikhulupililo, ndiponso ni mbali ya kulambila Mulungu. Yakobo, wophunzila wa Khristu anati ngati sitipempha “ndi cikhulupililo,” tisaganize ‘kuti tidzalandila kanthu kwa Yehova.’ (Yakobo 1:6, 7) Kuti tikhale na cikhulupililo mwa Mulungu, tiyenela kupatula nthawi yophunzila mwakhama Baibo kuti tim’dziŵe bwino. Ngati ticita zimenezi, tidzadziŵa bwino cifunilo cake, ndipo tidzayamba kupemphela tili na cikhulupililo cakuti atimvela.

MUSALEKE KUPEMPHELA!

Olo kuti Mulungu sayankha mapemphelo onse, amamva na kuyankha mapemphelo ocokela pansi pa mtima a anthu ambili ofika m’mamiliyoni. Baibo imakamba zimene mungacite kuti Mulungu azikondwela na mapemphelo anu. Nkhani yotsatila idzafotokoza zimenezi.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani