LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bhs nkhani 9 nkhani 94-104
  • Kodi Mapeto A Dziko Ali Pafupi?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mapeto A Dziko Ali Pafupi?
  • Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Ŵelengani mu Zimene Baibo Imaphunzitsa
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • NKHONDO YA KUMWAMBA
  • MASIKU OTSILIZA
  • MAKHALIDWE A ANTHU M’MASIKU OTSILIZA
  • UTHENGA WABWINO M’MASIKU OTSILIZA
  • NANGA INU MUDZACITAPO CIANI?
  • Kodi Ufumu Wa Mulungu N’ciani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Anakamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
bhs nkhani 9 nkhani 94-104

NKHANI 9

Kodi Mapeto A Dziko Ali Pafupi?

1. Kodi pali njila iti cabe yodziŵila za kutsogolo?

‘KODI kuipa kwa zinthu kudzacita kufika pati?’ Mwina munafunsapo conco pamene munali kumvela nyuzi. Mavuto ali paliponse, ndipo nkhanza za anthu zacita kufika pa unkhwalwe weni-weni. Cifukwa ca izi, anthu ambili amaona kuti dziko lomba likufika kumapeto kweni-kweni. Nanga inu muganiza bwanji? Kodi ilipo njila yodziŵila mmene zinthu zidzakhalila kutsogolo? Inde ilipo. Osati njila ya anthu, koma ya Mulungu. Kupitila m’Baibulo, Yehova Mulungu amatiuza za tsogolo la dziko lapansi, ndi tsogolo la ife anthu.—Yesaya 46:10; Yakobo 4:14.

2, 3. Kodi ophunzila a Yesu anali kufuna kudziŵa ciani? Nanga Yesu powayankha anati ciani?

2 N’zoona kuti Baibulo imakamba za mapeto, kapena kusila kwa dziko. Koma siitanthauza kutha kwa dziko limene tipondapo ili iyai, imatanthauza mapeto a zinthu zoipa. Yesu anaphunzitsa anthu kuti Ufumu wa Mulungu udzalamulila dziko lonse lapansi. (Luka 4:43) Ophunzila anafuna kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu udzabwela liti. Conco anafunsa kuti: “Kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti, ndipo cizindikilo ca kukhalapo kwanu ndi ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciani?” (Mateyu 24:3) Yesu powayankha sanawauze tsiku, koma zinthu zimene zidzacitika mapeto akakhala pafupi. Zimene Yesu anakamba n’zimene timaona masiku ano.

3 M’nkhani ino tidzakambilana maumboni otsimikizila kuti mapeto a dziko ali pafupi kweni-kweni. Koma kuti timvetsetse cifukwa cake zinthu zili zoipa conco pa dziko lapansi, tifunika kudziŵa za nkhondo imene inacitika kumwamba.

NKHONDO YA KUMWAMBA

4, 5. (a) Kodi kumwamba kunacitika ciani pamene Yesu anakhala Mfumu? (b) Mogwilizana ndi Chivumbulutso 12:12, cinacitika n’ciani pamene Satana anaponyedwa ku dziko lapansi?

4 M’Nkhani 8 tinaphunzila kuti mu 1914 Yesu anakhala Mfumu kumwamba. (Danieli 7:13, 14) Buku ya Chivumbulutso imatiuza zimene zinacitika. Imati: “Kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli [kutanthauza Yesu] ndi angelo ake anamenyana ndi cinjoka [Satana]. Cinjokaco ndi angelo ake cinamenya nkhondo.”a Koma pa nkhondo imeneyi, Satana ndi ziŵanda zake anagonjetsedwa. Ndipo anawaponyela ku dziko lapansi. Ha, ganizani cabe cisangalalo cimene angelo anakhala naco kumwamba! Koma bwanji kwa anthu pa dziko lapansi? Baibulo imakamba kuti inakhala nthawi yovuta kwambili. Cifukwa? Mdyelekezi anakhala wokwiya ngako, “podziŵa kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa.”—Chivumbulutso 12:7, 9, 12.

5 Mdyelekezi ali nu! kusokoneza dziko lonse ndi mavuto ambili-mbili. Iye walusilatu ndi ukali, podziŵa kuti wangotsala ndi “kanthawi kocepa” kuti Mulungu amuwononge. Lomba tiyeni tikambilane zimene Yesu anati zidzacitika m’masiku otsiliza.—Onani Zakumapeto 24.

MASIKU OTSILIZA

6, 7. Kodi tingati ciani za nkhondo ndi njala masiku ano?

6 Nkhondo. Yesu anati: “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Anthu amene afa m’nkhondo m’nthawi zathu zino ni ambili kupambana pa nthawi ina iliyonse m’mbili yonse ya anthu. Bungwe lina linakamba kuti kucokela mu 1914 mpaka lelo, anthu amene afa m’nkhondo zosiyana-siyana apitilila pa 100 miliyoni. Anthu amene anafa m’nkhondo zimene zinacitika pa zaka 100 cabe, kucokela m’caka ca 1900 mpaka m’caka ca 2000 anali ambili-mbili. Koma ciŵelengelo cawo ni cacikulu kuwilikiza katatu ciŵelengelo ca anthu amene anafa m’nkhondo zonse zimene zinacitika pa zaka 1,900 kumbuyoko. Ganizabe cabe za mavuto osaneneka, kupwetekedwa mtima, ndi cisoni cothetsa nzelu cimene nkhondo zimabweletsa kwa anthu mamiliyoni ambili.

Zithunzi-thunzi zoonetsa masiku otsiliza: bomba iphulika, mwana wodwala ndi njala, ndeke ya nkhondo, ngozi ya

7 Njala. Kupitiliza, Yesu anati: “Kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Ngakhale kuti pa dziko lomba pali cakudya cambili kupambana kale lonse, anthu oculuka alibe cakudya cokwanila. Cifukwa? Sapeza ndalama zokwanila, kapena malo olimapo. Anthu opitilila 1 biliyoni, cakudya cawo pa tsiku sicikwana dola imodzi. Bungwe loona za umoyo (World Health Organization) linakamba kuti, ana mamiliyoni ambili amafa caka ciliconse cifukwa ca njala.

8, 9. Tidziŵa bwanji kuti zimene Yesu anakambilatu za zivomezi ndi matenda n’zoona?

8 Zivomezi. Yesu anakambilatu kuti: “Kudzacitika zivomezi zamphamvu.” (Luka 21:11) Masiku ano, caka ciliconse anthu amayembekeza kuti kudzacitika zivomezi zamphamvu zambili. Kucokela m’caka ca 1900, zivomezi zapha anthu opitilila 2 miliyoni. Ngakhale kuti masiku ano kuli makina ocenjezelatu za civomezi, anthu ambili akali kufa ndi zivomezi.

9 Matenda. Yesu anakambanso kuti kudzakhala “milili,” kutanthauza matenda oopsa ofalikila mwamsanga ndi kupha anthu ambili. (Luka 21:11) Olo kuti madokota apeza mankhwala ocilitsila matenda ambili, pakali matenda ena osacilitsika. Lipoti ina inati caka ciliconse, anthu mamiliyoni ambili amafa ndi matenda monga TB, maleliya, ndi kolela. Ndiponso, madokota atulukilanso matenda ena 30 atsopano, ndipo ena mwa matendawo alibe mankhwala.

MAKHALIDWE A ANTHU M’MASIKU OTSILIZA

Zithunzi-thunzi zoonetsa masiku otsiliza: matenda, anthu okonda ndalama ndi zokondweletsa, mavuto a m’banja, atsilikali ku nkhondo

10. Kodi lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 limakwanilitsika bwanji masiku ano?

10 Pa 2 Timoteyo 3:1-5, Baibulo imati: “Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta.” Mtumwi Paulo analongosola makhalidwe amene anthu ambili adzakhala nawo m’masiku otsiliza. Iye anakamba kuti anthu adzakhala

  • odzikonda

  • okonda ndalama

  • osamvela makolo

  • osakhulupilika

  • osakonda abululu awo

  • osadziletsa

  • oopsa ndi aukali

  • okonda zokondweletsa kupambana Mulungu

  • onamizila kukonda Mulungu koma safuna kumumvela

11. Malinga ndi lemba la Salimo 92:7, n’ciani cidzacitika kwa anthu oipa?

11 Kodi kumene mumakhala mumaona anthu ali ndi makhalidwe amenewa? Kuli konse pa dziko lapansi, anthu ambili ali ndi makhalidwe amenewa. Koma posacedwapa, Mulungu adzacitapo kanthu. Iye anakambilatu kuti: “Anthu oipa akamaphuka ngati msipu, ndipo anthu onse ocita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluŵa, amatelo kuti awonongeke kwamuyaya.”—Salimo 92:7.

UTHENGA WABWINO M’MASIKU OTSILIZA

12, 13. Kodi Yehova watiphunzitsa ciani m’masiku ano otsiliza?

12 Baibulo inakambilatu kuti m’masiku otsiliza, pa dziko padzakhala mavuto ambili-mbili. Koma imakambanso kuti kudzacitikanso zinthu zabwino.

Mboni za Yehova zimalalikila uthenga wa Ufumu pa dziko lonse

“Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Mateyu 24:14

13 Kuimvetsetsa Baibulo. Mneneli Danieli analemba za masiku otsiliza. Iye anati: “Anthu ambili . . . adzadziŵa zinthu zambili zoona.” (Danieli 12:4) Lelolino, Yehova wathandiza anthu ake kumvetsetsa Baibulo kuposa kale lonse. Wacitadi zimenezi makamaka kuyambila mu 1914. Mwacitsanzo, watiphunzitsa kufunika kwa dzina lake, colinga cake ca dziko lapansi, tanthauzo la dipo, zimene zimacitika munthu akafa, ndi za kuuka kwa akufa. Taphunzila kuti ni Ufumu wa Mulungu cabe umene udzacotsapo mavuto onse. Taphunzilanso mmene tingapezele cimwemwe, ndi mmene tingakhalile ndi moyo wokondweletsa Mulungu. Koma kodi atumiki a Mulungu amafunika kucita ciani ndi zimene aphunzila? Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambilane ulosi wina.—Onani Zakumapeto 21 ndi 25.

14. Kodi uthenga wabwino wa Ufumu umalalikidwa kuti? Ndipo umalalikidwa kwa ndani?

14 Nchito yolalikila pa dziko lonse. Za masiku otsiliza Yesu anati: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyu 24:3, 14) Uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa m’maiko opitilila 230, m’zinenelo zopitilila 700. Inde, kuzungulila dziko lonse lapansi, Mboni za Yehova zocokela “fuko lililonse, mtundu uliwonse” zili kaliki-liki, kuthandiza anthu kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu n’ciani, ndi zimene udzacitila ife anthu. (Chivumbulutso 7:9) Iwo amacita zimenezi kwaulele. Ngakhale kuti anthu ambili amawazonda ndi kuwazunza, Yesu anakambilatu kuti palibe cimene cingalepheletse nchito yolalikila.—Luka 21:17.

NANGA INU MUDZACITAPO CIANI?

15. (a) Kodi inu mukhulupilila kuti tili m’masiku otsiliza? Mwayankha conco cifukwa ciani? (b) N’ciani cidzacitika kwa anthu amene amamvela Yehova? Nanga bwanji kwa amene samumvela?

15 Kodi mumakhulupilila kuti tili m’masiku otsiliza? Maulosi ambili a m’Baibulo okamba za masiku otsiliza ali kukwanilitsika. Posacedwa, Yehova adzaimitsa nchito yolalikila uthenga wabwino, ndipo “mapeto” adzafika. (Mateyu 24:14) Kodi mapeto amenewo n’ciani? Ni nkhondo ya Aramagedo, pamene Mulungu adzacotsa zinthu zonse zoipa. Yehova adzagwilitsila nchito Yesu ndi angelo ake amphamvu. Adzawononga aliyense amene amakana kumvela Mulungu ndi Mwana wake. (2 Atesalonika 1:6-9) Pambuyo pake, Satana ndi ziŵanda zake sadzakwanitsa kusoceletsa anthu. Ndipo anthu onse omvela Mulungu ndi kukhalila kumbuyo Ufumu wake, adzadzionela okha ndi maso awo pamene Mulungu adzakwanilitsa madalitso onse amene analonjeza.—Chivumbulutso 20:1-3; 21:3-5.

16. Popeza kuti mapeto ali pafupi, kodi muyenela kucitapo ciani?

16 Posacedwa, dziko lino limene wolamulila wake ni Satana lidzawonongedwa. Conco, ni bwino kumadzifunsa kuti, ‘Kodi ine nifunika kucitapo ciani?’ Yehova amafuna kuti muphunzile zambili m’Baibulo. Conco, kuphunzila Baibulo muyenela kukuona kukhala kofunika kwambili. (Yohane 17:3) A Mboni za Yehova amakhala ndi misonkhano wiki iliyonse. Misonkhano imeneyi imathandiza anthu kumvetsetsa Baibulo. Muzipezeka ku misonkhano imeneyi nthawi zonse. (Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.) Mukaona kuti pali zinthu zina zimene mufunika kusintha mu umoyo wanu, sinthani osadodoma. M’pamene ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimbilako-limbilako.—Yakobo 4:8.

17. N’cifukwa ciani anthu ambili adzadabwa pamene mapeto adzafika?

17 Mtumwi Paulo anafotokoza kuti ciwonongeko ca anthu oipa cidzafika modzidzimutsa, “ngati mbala usiku.” (1 Atesalonika 5:2) Yesu anakambilatu kuti anthu ambili adzanyalanyaza umboni woonetsa kuti tili m’masiku otsiliza. Iye anati: “Monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu [kapena kuti masiku otsiliza] kudzakhalile. M’masiku amenewo Cigumula cisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatila ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikila tsiku limene Nowa analoŵa m’cingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kucitika mpaka cigumula cinafika n’kuwaseselatu onsewo. Zidzatelonso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:37-39.

18. Kodi Yesu anapeleka cenjezo lanji?

18 Yesu poticenjeza anati tisalole kuti “kudya kwambili, kumwa kwambili, ndi nkhawa za moyo” ziticenjeneke. Iye anati mapeto adzafika modzidzimutsa, “ngati msampha.” Anakambanso kuti tsikulo “lidzafikila onse okhala pa nkhope ya dziko lonse lapansi.” Ndiyeno anapitiliza kuti: “Khalani maso ndipo muzipemphela mopembedzela nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kucitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:34-36) N’cifukwa ciani kuli kofunika kwambili kumvela cenjezo la Yesu? Cifukwa lomba apa, dziko loipa ili la Satana lidzawonongedwa. Nanga amene adzapulumuka n’ndani? Awo cabe amene Yehova ndi Yesu amawayanja. Ndipo adzalandila moyo wosatha m’dziko latsopano.—Yohane 3:16; 2 Petulo 3:13.

a Mikayeli ndi dzina lina la Yesu Khiristu. Kuti mudziŵe zambili, onani Zakumapeto pa tsamba 23.

MFUNDO ZIKULU

MFUNDO 1: YEHOVA AMATIUZA ZA KUTSOGOLO

“Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambila pa ciyambi. Kuyambila kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinacitike.”—Yesaya 46:10

Timadziŵa ciani za nthawi ya mapeto?

  • Danieli 7:13, 14

    Yesu anakhala Mfumu kumwamba mu 1914.

  • Mateyu 24:3-14

    Yesu anakamba kuti anthu adzakumana ndi mavuto.

  • Chivumbulutso 12:7-9, 12

    Atangoikidwa kukhala Mfumu, Yesu anaponyela Satana ku dziko lapansi. Satana ni wokwiya kwambili cifukwa “wangotsala ndi kanthawi kocepa” kuti Mulungu amuwononge.

MFUNDO 2: TILI M’MASIKU OTSILIZA

Kodi “cizindikilo . . . ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciyani?”—Mateyu 24:3

Kodi pali umboni woonetsa kuti maulosi a m’Baibulo ali kukwanilitsika?

  • Mateyu 24:7; Luka 21:11

    Nkhondo, njala, zivomezi, ndi matenda zicitika kuposa kale lonse.

  • 2 Timoteyo 3:1-5

    Mtumwi Paulo anakambilatu za makhalidwe a anthu m’masiku otsiliza.

  • Danieli 12:4

    Mulungu athandiza anthu kumvetsetsa bwino Baibulo kuposa kale lonse.

  • Mateyu 24:14

    Uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwa pa dziko lonse lapansi.

MFUNDO 3: CITANIPO KANTHU PALI PANO KUTI MUKONDWELETSE YEHOVA

“Tsiku la Yehova lidzabwela ndendende ngati mbala usiku.”—1 Atesalonika 5:2

Popeza kuti mapeto ali pafupi, kodi mufunika kucita ciani?

  • Yohane 17:3

    Phunzilani Baibulo mwakhama.

  • Aheberi 10:24, 25

    Phunzilani zambili mwa kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova.

  • Yakobo 4:8

    Sinthani zinthu mu umoyo wanu kuti mukhale bwenzi la Mulungu.

  • Luka 21:34-36

    Pewani zocenjeneka, ndipo lambilani Yehova ndi mtima wanu wonse.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani