Colinga ca Yehova Cidzakwanilitsika
“Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazicita. Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazicitadi.”—YES. 46:11.
1, 2. (a) Kodi Yehova anatidziŵitsa ciani? (b) Kodi Yesaya 46:10, 11 ndi 55:11 limatitsimikizila ciani?
MAU oyamba m’Baibo ali ndi mfundo yosavuta kumvetsa koma yofunika yakuti: “Pa ciyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Gen. 1:1) Ise anthu timadziŵako zocepa cabe pa zinthu zambili zimene Mulungu anapanga, monga thambo, kuwala, ndi mphamvu yokoka zinthu kuti zigwe pansi. Ndiponso, taonako mbali yocepa cabe ya cilengedwe cake. (Mlal. 3:11) Ngakhale n’conco, Yehova anatidziŵitsa colinga cake cokhudza dziko lapansi ndi anthu. Dziko lapansi linali kudzakhala malo abwino kuti amuna ndi akazi olengedwa m’cifanizilo ca Mulungu akhalemo. (Gen. 1:26) Iwo anali kudzakhala ana ake, ndipo Yehova anali kudzakhala Atate wawo.
2 Monga mmene Genesis caputa 3 imakambila, colinga ca Yehova cinasokonezeka. (Gen. 3:1-7) Koma sikuti basi colinga cake cinalephelelatu. Palibe aliyense angalimbane na Yehova. (Yes. 46:10, 11; 55:11) Conco, ndife otsimikiza kuti colinga ca Yehova ca poyamba cidzakwanilitsika ndendende panthawi yake.
3. (a) N’ziphunzitso zofunika kwambili ziti zimene zatithandiza kumvetsa uthenga wa m’Baibo? (b) N’cifukwa ciani tikukambilananso ziphunzitso zimenezi? (c) Nanga tidzakambilana mafunso ati?
3 Mosakaikila, ife tidziŵa coonadi ca m’Baibo ponena za colinga ca Mulungu cokhudza dziko lapansi ndi anthu. Tidziŵanso udindo waukulu wa Yesu Khiristu pokwanilitsa colinga ca Mulungu. Ziphunzitso zimenezi n’zofunika kwambili, ndipo n’kutheka kuti ni zina mwa mfundo za coonadi zoyambilila zimene tinadziŵa titangoyamba kuphunzila Mau a Mulungu. Conco, nafenso tiyenela kuuzako ena kuti adziŵe ziphunzitso zofunika zimenezi. Pamene tiphunzila nkhani ino monga mpingo, tili mkati moitanila anthu ambili ku Cikumbutso ca imfa ya Khiristu. (Luka 22:19, 20) Amene adzapezekapo adzaphunzila zambili zokhudza colinga ca Mulungu. Pamene kwatsala masiku ocepa kuti ticite Cikumbutso, tiyenela kuganizila mafunso amene tingaseŵenzetse pothandiza ophunzila Baibo ndi anthu oona mtima kucita cidwi ndi cocitika capadela cimeneci. Tidzakambilana mafunso atatu aya: Kodi colinga ca Mulungu ca poyamba cokhudza dziko lapansi ndi anthu cinali ciani? Nanga n’ciani cinalakwika? N’cifukwa ciani nsembe ya dipo la Yesu ndiye inatsegula khomo kuti colinga ca Mulungu cikwanilitsike?
KODI COLINGA CA MLENGI CA POYAMBA CINALI CIANI?
4. Kodi cilengedwe cimaonetsa bwanji ulemelelo wa Yehova?
4 Yehova ni Mlengi wodabwitsa kwambili. Ciliconse cimene anapanga cimagwilizana ndi miyezo yake yapamwamba. (Gen. 1:31; Yer. 10:12) Tingaphunzilepo ciani tikaona mmene cilengedwe cilili cokongola ndi cadongosolo? Tikayang’ana zinthu zonse zimene Yehova anapanga, kaya zazing’ono kapena zazikulu, timacita cidwi ndi mmene zimaonetsela colinga cake. Tonsefe timacita cidwi tikaganizila mmene maselo a thupi la munthu amagwilila nchito modabwitsa. Timacitanso cidwi ndi kukongola kwa dzuŵa likamaloŵa kapena mwana wakhanda amene wangobadwa kumene. Timasangalala ndi cilengedwe cimeneci cifukwa mwacibadwa timakwanitsa kuzindikila zinthu zokongola.—Ŵelengani Salimo 19:1; 104:24.
5. Kodi Yehova anaonetsetsa bwanji kuti cilengedwe conse cikugwila nchito mogwilizana?
5 Monga mmene cilengedwe cionetsela, Yehova mwacikondi anaika malamulo. Anapanga malamulo a zacilengedwe ndi okhudza makhalidwe abwino, pofuna kuti zinthu zonse zizicitika mwadongosolo. (Sal. 19:7-9) Conco, zinthu zonse za m’cilengedwe zili ndi malo ake, ndipo zimagwila nchito mogwilizana ndi mmene Mulungu anafunila. Yehova anaika malamulo a mmene cilengedwe cake ciyenela kugwilila nchito mogwilizana. Mwacitsanzo, mphamvu yokoka zinthu kuti zigwe pansi imapangitsa cifungadziko (atmosphere) kufungatila dziko lapansi, kukhalitsa bata mafunde a panyanja, komanso kucilikiza zamoyo padziko. Cilengedwe conse, kuphatikizapo anthu, cimagwila nchito motsatila malamulo amenewa. Mmene cilengedwe cilili ca dongosolo ni umboni wakuti Mulungu ali nalo colinga cabwino dziko lapansi ndi anthu. Tikakhala mu ulaliki, kodi sitingauzeko ena za amene Anacititsa kuti pakhale dongosolo limeneli?—Chiv. 4:11.
6, 7. Ni mphatso zina ziti zimene Yehova anapatsa Adamu ndi Hava?
6 Yehova anali kufuna kuti mtundu wa anthu ukhale padziko lapansi kwamuyaya. (Gen. 1:28; Sal. 37:29) Mopanda kaso anapatsa Adamu ndi Hava mphatso zosiyana-siyana kuti asangalale ndi moyo. (Ŵelengani Yakobo 1:17.) Yehova anawapatsa ufulu wodzisankhila zocita, kuganiza, kusonyezana cikondi, ndi kusangalala ndi mgwilizano. Mlengi anali kukamba ndi Adamu ndi kumulangiza mmene angaonetsele kumvela. Adamu anaphunzilanso mmene angasamalile zosoŵa zake, ndi mmene angasamalile nyama na dziko lapansi. (Gen. 2:15-17, 19, 20) Ndiponso, Yehova anapanga Adamu ndi Hava m’njila yakuti adzikwanitsa kulaŵa, kukhudza zinthu, kuona, kumva, ndi kununkhiza. Conco, iwo akanasangalala ndi zinthu zambili zokongola m’mudzi wawo wa Paradaiso. Banja loyambalo linali ndi mwayi wogwila nchito yokhutilitsa, yosangalatsa, komanso kutulukila zinthu zatsopano kwamuyaya.
7 N’ciani cina cinali mbali ya colinga ca Mulungu? Mulungu analenga Adamu ndi Hava ndi kuwapatsa mphatso yobeleka ana angwilo. Mulungu anafuna kuti ana awo akhalenso ndi ana anzawo mpaka dziko lonse kudzala ndi anthu. Anafuna kuti Adamu na Hava ndi makolo onse azikonda ana awo, monga mmene Yehova anakondela ana ake aumunthu oyamba angwilo. Dziko lapansi, ndi zonse zili mmenemo, linali kudzakhala malo awo okhalamo a muyaya.—Sal. 115:16.
N’CIANI CINALAKWIKA?
8. Kodi lamulo la pa Genesis 2:16, 17 linali n’colinga canji?
8 Zinthu sizinacitike monga mmene Mulungu anali kufunila. N’cifukwa ciani? Yehova anapatsa Adamu ndi Hava lamulo losavuta kulitsatila, kuti aone ngati iwo anali kuzindikila malile a ufulu wawo. Mulungu anati: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa. Cifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Gen. 2:16, 17) Kwa Adamu ndi Hava, lamulo limeneli linali losavuta kulimvetsetsa kapena kulitsatila. Si paja iwo anali ndi cakudya ca mwana alilenji.
9, 10. (a) Satana anamuneneza ciani Yehova? (b) Kodi Adamu ndi Hava anasankha ciani? (Onani pikica kuciyambi kwa nkhani ino.)
9 Satana Mdyelekezi anaseŵenzetsa njoka kunyenga Hava kuti asamvele Atate wake, Yehova. (Ŵelengani Genesis 3:1-5; Chiv. 12:9) Satana anayambitsa nkhani yaikulu mwa kukamba kuti ana aumunthu a Mulungu analetsedwa kudya “zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu.” Zinali ngati kuti iye akukamba kuti: ‘Kodi simungacite zimene mufuna?’ Cotsatila, anakamba bodza lamkunkhuniza kuti: “Kufa simudzafa ayi.” Ndiyeno, anapangitsa Hava kukhulupilila kuti safunika kumvela Mulungu mwa kukamba kuti: ‘Mulungu akudziŵa kuti tsiku limene mudzadya cipatso ca mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu.’ Mwamacenjela, Satana anaonetsa kuti Yehova sanali kufuna kuti iwo adye cipatsoco kuopela kuti angatseguke mutu. Kuwonjezela apo, Satana anapeleka lonjezo labodza kuti: “Mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.”
10 Tsopano, Adamu ndi Hava anafunika kusankha coyenela kucita. Kodi akanafunika kumvela Yehova kapena njoka? Iwo anasankha kusamvela Mulungu. Mwakutelo, anagwilizana ndi Satana kupandukila Mulungu. Anakana Yehova monga Atate wawo, ndipo anadzikanganula okha ku ulamulilo wake wopeleka citetezo.—Gen. 3:6-13.
11. N’cifukwa ciani Yehova sanalekele cipanduko?
11 Cifukwa copandukila Mulungu, Adamu ndi Hava anakhala opanda ungwilo. Ndipo kupanduka kwawo kunacititsa kuti atalikilane ndi Yehova, ndaŵa ni ‘woyela kwambili cakuti sangaonelele zinthu zoipa.’ Conco, iye sangalekelele khalidwe loipa. (Hab. 1:13) Sembe analekelela khalidwe loipalo, zolengedwa zonse—kumwamba ndi padziko lapansi—zikanakhudzidwa kwambili. Koposa zonse, zikanakhala kuti Mulungu sanacitepo kanthu pa ucimo wa mu Edeni, kukhulupilika kwake kukanakhala kokaikitsa. Koma Yehova ni wokhulupilika ku malamulo ake, ndipo sawaphwanya olo pang’ono. (Sal. 119:142) Mwa ici, ufulu wodzisankhila zocita sunapatse mphamvu Adamu ndi Hava zophwanya lamulo la Mulungu. Zotulukapo za kupandukila Yehova n’zakuti anafa, ndipo anabwelela ku dothi kumene anatengedwa.—Gen. 3:19.
12. N’ciani cinacitikila ana a Adamu?
12 Adamu ndi Hava atadya cipatso, anadziika pamalo akuti sangalandilidwe kukhala m’banja la Mulungu. Mulungu anawacotsa mu Edeni, ndipo analibe ciyembekezo cobwelelanso. (Gen. 3:23, 24) Mwakutelo, Yehova potsatila cilungamo, anacititsa kuti akumane ndi zotulukapo za cosankha cawo. (Ŵelengani Deuteronomo 32:4, 5.) Cifukwa ca kupanda ungwilo, munthu sakanaonetsa bwino-bwino makhalidwe a Mulungu. Adamu sanangotaya cabe tsogolo lake labwino, koma anapatsilanso ana ake kupanda ungwilo, ucimo, na imfa. (Aroma 5:12) Iye anacititsa kuti mbadwa zake zikhale zopanda ciyembekezo ca moyo wosatha. Kuwonjezela apo, Adamu ndi Hava sakanabeleka mwana wangwilo. Nayenso mwanayo sakanabeleka mwana wangwilo. Satana Mdyelekezi atacotsa Adamu ndi Hava kwa Mulungu, anapitilizabe kusoceletsa mtundu wa anthu mpaka lelo.—Yoh. 8:44.
DIPO LINAKONZA ZINTHU
13. Kodi Yehova ali nawo colinga canji anthu?
13 Mulungu anapitiliza kukonda anthu. Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anapanduka, Yehova anafuna kuti mtundu wa anthu ukhale pa ubale ndi iye. Safuna kuti aliyense akawonongedwe. (2 Pet. 3:9) Conco, pambuyo pa cipanduko, mwamsanga Mulungu anapanga makonzedwe akuti anthu akhalenso pa ubwenzi ndi iye, panthawi imodzi-modzi kusungabe miyezo yake yolungama. Kodi Yehova anacita bwanji zimenezi?
14. (a) Mogwilizana ndi Yohane 3:16, kodi Mulungu anacitanji kuti apulumutse anthu? (b) Ni funso liti limene tingakambilane ndi anthu okondwelela?
14 Ŵelengani Yohane 3:16. Anthu ambili amene timawaitanila ku Cikumbutso amaisunga pamtima lemba limeneli. Koma funso n’lakuti, Kodi imfa ya Yesu imacititsa bwanji kuti zikhale zotheka anthu kukapeza moyo wamuyaya? Tili ndi mwayi wothandiza anthu ofuna-funa coonadi kudziŵa yankho la funso lofunika kwambili limeneli pamene tiwaitanila ku Cikumbutso, pamene tipezeka pa Cikumbutso, ndi pamene tibwelelako kwa iwo. Anthu amenewa angakhale ndi cidwi akayamba kumvetsetsa mmene dipo limene Yehova anapeleka limaonetsela cikondi ndi nzelu zake. Ni mfundo ziti zokhudza dipo zimene tingagogomeze?
15. Kodi Yesu asiyana bwanji ndi Adamu?
15 Yehova anapeleka munthu wangwilo kuti akhale dipo. Munthu wangwilo ameneyu anafunika kukhala wokhulupilika kwa Yehova, ndi kukhala wofunitsitsa kupeleka moyo wake kuwombola anthu opanda ciyembekezo. (Aroma 5:17-19) Yehova anatsamutsa moyo wa colengedwa cake coyamba kucoka kumwamba kubwela padziko lapansi. (Yoh. 1:14) Motelo, Yesu anadzakhala munthu wangwilo monga mmene Adamu analili. Koma mosiyana ndi Adamu, Yesu anakhala moyo mogwilizana ndi zimene Yehova anali kuyembekezela kwa munthu wangwilo. Yesu sanacimwepo kapena kuphwanya lamulo limodzi la Mulungu, ngakhale atakumana ndi mayeselo aakulu kwambili.
16. N’cifukwa ciani dipo ni mphatso ya mtengo wapatali?
16 Pokhala munthu wangwilo, Yesu anapulumutsa anthu ku ucimo ndi imfa mwa kuwafela. Iye anakhala moyo ndendende monga mmene Adamu anafunika kukhalila—munthu wangwilo, wokhulupilika kothelatu ndi womvela Mulungu. (1 Tim. 2:6) Yesu anakhala nsembe ya dipo imene inatsegula njila ya ku moyo wosatha kwa “anthu ambili”—amuna, akazi, ndi ana. (Mat. 20:28) Kukamba zoona, dipo ndiye inatsegula khomo kuti colinga ca Mulungu ca poyamba cikwanilitsike. (2 Akor. 1:19, 20) Dipo limapatsa anthu onse okhulupilika ciyembekezo ca moyo wamuyaya.
YEHOVA ANATSEGULA KHOMO KUTI TIBWELELE KWA IYE
17. Kodi dipo idzatheketsa ciani?
17 Yehova anapeleka dipo ya mtengo wapatali. (1 Pet. 1:19) Amakonda anthu kwambili cakuti anali wofunitsitsa kupeleka Mwana wake wobadwa yekha kuti adzatifele. (1 Yoh. 4:9, 10) M’lingalilo leni-leni, Yesu analoŵa m’malo atate wathu waumunthu woyambilila, Adamu. (1 Akor. 15:45) Mwakutelo, Yesu anacita zambili kuposa pa kubwezeletsa cabe moyo. Iye anatipatsa mwayi wobwelela m’banja la Mulungu. Inde, pamaziko a nsembe ya Yesu, Yehova angalandilenso anthu m’banja lake popanda kuphwanya mfundo zake zolungama. Kodi sizolimbikitsa kuganizila nthawi pamene anthu onse okhulupilika adzakhala angwilo? Pamapeto pake, zolengedwa zonse za kumwamba ndi za padziko lapansi zidzakhala zogwilizana monga banja limodzi. Ife tonse tidzakhala ana a Mulungu.—Aroma 8:21.
18. Ni liti pamene Yehova adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense”?
18 Kupanduka kwa Satana sikunaletse Yehova kuonetsa cikondi ku mtundu wa anthu, kapena kulepheletsa anthu opanda ungwilo kukhala okhulupilika kwa Yehova. Kupitila m’dipo limene anapeleka, Yehova adzathandiza ana ake onse kukhala olungama kothelatu. Tangoganizilani mmene umoyo udzakhalila pamene aliyense “woona Mwana ndi kukhulupilila” adzakhala ndi moyo wamuyaya. (Yoh. 6:40) Cifukwa ca cikondi ndi nzelu zake, Yehova adzathandiza banja la anthu kukhala langwilo, monga mmene anali kufunila poyamba. Ndiyeno Yehova, Atate wathu, adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”—1 Akor. 15:28.
19. (a) Kodi kuyamikila dipo kuyenela kutisonkhezela kucita ciani? (Onani danga lakuti “Tiyeni Tipitilize Kufuna-funa Anthu Oyenelela.”) (b) Tidzakambilana mbali iti yokhudza dipo m’nkhani yotsatila?
19 Kuyamikila dipo kuyenela kutisonkhezela kucita zonse zimene tingathe kuti tithandize ena kudziŵa kuti nawonso angapindule ndi mphatso ya mtengo wapatali imeneyi. Anthu afunika kudziŵa kuti dipo ni njila yacikondi imene Yehova anapeleka ku mtundu wa anthu kuti akhale ndi ciyembekezo ca moyo wa muyaya. Komabe, pali zambili zimene dipo lidzakwanilitsa. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene nsembe ya Yesu inathetsela nkhani zimene Satana anayambitsa m’munda wa Edeni.