LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w16 April masa. 15-20
  • N’cifukwa Ciani Tiyenela Kusonkhana?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Tiyenela Kusonkhana?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MISONKHANO NDI YOFUNIKA KWA IFE
  • PAMISONKHANO TIMATHANDIZA ENA
  • TIDZAKONDWELETSA YEHOVA
  • PITILIZANI KUSONKHANA NDI ABALE
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakupindulileni Motani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Kupezeka pa Misonkhano Kumaonetsa Kuti Ndife Anthu Otani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kodi Mudzaona Ciani Mukabwela ku Misonkhano Yathu?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Kusonkhana Pamodzi Kuti Tilambile Mulungu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
w16 April masa. 15-20
Corinna ndi mlongo wina akuyenda ulendo wautali kuti akasonkhane ku Siberia

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kusonkhana?

‘Iwo anapitiliza kulabadila.  . . ndi kugaŵana zinthu’ [‘kusonkhana pamodzi.’ NWT]—MACHITIDWE 2:42.

NYIMBO: 20, 119

POGWILITSILA NCHITO KABOKOSI KAKUTI “CIFUKWA CAKE TIFUNIKA KUPEZEKA PAMISONKHANO,” FOTOKOZANI . . .

  • mmene timapindulila ndi misonkhano yampingo.

  • mmene timalimbikitsila ena tikapezeka pa misonkhano.

  • mmene Yehova amamvelela tikapezeka pa misonkhano.

1-3. (a) Kodi Akristu amaonetsa bwanji kuti amafunitsitsa kupezeka pamisonkhano? (Onani cithunzi pamwambapa.) (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino?

PAMENE Corinna anali ndi zaka 17, amai ake anamangidwa, kenako anawatenga ndi kupita nao kutali. Kumeneko anali kuwagwilitsa nchito ya ukapolo. Pambuyo pake, Corinna nayenso anam’tenga ndi kupita naye ku Siberia, kutali kwambili ndi kwao. Kumeneko anali kugwila nchito pa famu ndipo anali kum’zunza monga kapolo. Nthawi zina, anali kumukakamiza kupita kukaseŵenza ngakhale pamene kwazizila kwambili, ndipo sanali kum’patsa zovala za mphepo. Ngakhale zinali conco, Corinna ndi mlongo wina anacita zonse zotheka kuti acoke ku famu ndi kupita kumisonkhano ya mpingo.

2 Corinna anati: “Tinacoka m’madzulo kumene tinali kuseŵenzela ndi kupita ku sitesheni ya sitima imene inali pa mtunda wa makilomita 25. Sitima inanyamuka 02:00 usiku, ndipo tinayenda maola 6 tisanafike potsikila. Titatsika, tinayenda mtunda wa makilomita 10 kuti tikafike pamalo osonkhanila.” Corinna anali wosangalala kwambili ndipo sanaone kuti analakwitsa kupanga ulendo wautali umenewo. Iye anati: “Pamisonkhano, tinaphunzila Nsanja ya Mlonda ndi kuimba nyimbo za Ufumu. Panthawi imeneyi, tinalimbikitsidwa ndipo cikhulupililo cathu cinalimba kwambili.” Alongo aŵiliwa anabwelela ku famu pambuyo pa masiku atatu, koma bwana wao sanadziŵe kuti anali atacokapo.

3 Nthawi zonse, anthu a Yehova amakondwela kusonkhana pamodzi. Mwacitsanzo, Akristu oyambilila anali kukonda kukumana pamodzi kuti alambile Yehova ndi kuphunzila za iye. (Machitidwe 2:42) Mwacionekele, inunso mumayembekezela mwacidwi tsiku la misonkhano kuti mukasonkhane. Koma mofanana ndi abale ndi alongo ena, mwina inunso mumalephela kupezeka pamisonkhano nthawi zina. Mwina n’cifukwa cakuti mumagwila nchito kwa maola ambili, mumakhala ndi zocita zambili, kapena mumakhala olema. Kodi n’ciani cingatithandize kuti tizipezeka pamisonkhano nthawi zonse?[1] (Onani mau akumapeto.) Kodi tingawalimbikitse bwanji maphunzilo athu a Baibulo kuti azipezeka pamisonkhano nthawi zonse? Nkhani ino ifotokoza mmene kupezeka pamisonkhano (1) kumatipindulitsila, (2)  kumapindulitsila ena, ndi (3) mmene kumakondweletsela Yehova.[2]—Onani mau akumapeto.

MISONKHANO NDI YOFUNIKA KWA IFE

4. Kodi misonkhano imatithandiza bwanji kuphunzila za Yehova?

4 Pamisonkhano timaphunzila zambili. Msonkhano uliwonse umatithandiza kudziŵa zambili ponena za Yehova. Mwacitsanzo, posacedwapa m’mipingo yambili, abale ndi alongo anali kuphunzila buku lakuti Yandikirani kwa Yehova pa Phunzilo la Baibulo la Mpingo. Munali kumva bwanji pamene tinali kuphunzila makhalidwe a Yehova? Nanga munali kumva bwanji pamene munali kumvetsela ndemanga za Akristu anzanu zoonetsa mmene amakondela Yehova? N’zoonekelatu kuti zimenezi zinakucititsani kum’konda kwambili Yehova. Pamisonkhano, timaphunzila zinthu mwa kumvetsela mwachelu nkhani za m’Baibulo, zitsanzo, ndi mbali ya kuŵelenga Baibulo. (Nehemiya 8:8) Ndipo ganizilani mfundo zatsopano zimene timaphunzila mlungu uliwonse tikamakonzekela mbali ya kuŵelenga Baibulo, ndi kumva zimene ena anapindula pa kuŵelenga Baibulo kumeneko.

5. Kodi misonkhano yakuthandizani bwanji kuti muzicita zimene mumaphunzila m’Baibulo? Nanga yakuthandizani bwanji kunola luso lanu mu ulaliki?

5 Misonkhano imatiphunzitsa kuti tizicita zimene timaphunzila m’Baibulo. (1 Atesalonika 4:9, 10) Mwacitsanzo, kodi pali Phunzilo la Nsanja ya Mlonda limene linakulimbikitsani kuonjezela utumiki wanu, kuongolela mapemphelo anu, kapena kuyesetsa kukhululukila abale ndi alongo anu? Msonkhano wa mkati mwa mlungu umatiphunzitsa mmene tingalalikilile uthenga wabwino ndi mmene tingathandizile ena kumvetsetsa coonadi ca m’Baibulo.—Mateyu 28:19, 20.

6. Kodi misonkhano yathu imatithandiza bwanji kuti tikhalebe olimba?

6 Misonkhano imatilimbikitsa. Cifukwa cakuti tikukhala m’dziko la Satana, nthawi zina cikhulupililo cathu cingafooke, tingakhale ndi nkhawa kapena kukhumudwa. Koma misonkhano yathu imatilimbikitsa ndi kutipatsa mphamvu kuti tipitilize kutumikila Yehova. (Ŵelengani Machitidwe 15:30-32.) Nthawi zambili, timakambilana mmene malonjezo a m’Baibulo akhala akukwanilitsidwila. Izi zimatithandiza kukhala otsimikiza kuti malonjezo a Yehova amtsogolo adzakwanilitsidwa. Abale ndi alongo athu amatilimbikitsa pamisonkhano mwa kukamba nkhani, kupeleka mayankho, ndi kuimba nyimbo mocokela pansi pa mtima. (1 Akorinto 14:26) Ndipo tikamakambilana nao misonkhano isanayambe kapena itatha, timalimbikitsidwa cifukwa timadziŵa kuti tili ndi mabwenzi ambili amene amatikonda.—1 Akorinto 16:17, 18.

Misonkhano yathu imatilimbikitsa ndi kutipatsa mphamvu kuti tipitilize kutumikila Yehova

7. N’cifukwa ciani kupezeka pamisonkhano yathu n’kofunika?

7 Pamisonkhano, Mulungu amatithandiza ndi mzimu woyela. Yesu amagwilitsila nchito mzimu woyela potsogolela mipingo. Ndipo anatiuza kuti tiyenela ‘kumva zimene mzimu ukunena ku mipingo.’ (Chivumbulutso 2:7) Mzimu woyela ungatithandize kulimbana ndi ziyeso ndi kulalikila molimba mtima. Ungatithandizenso kusankha zinthu mwanzelu. Ndiye cifukwa cake tiyenela kucita zimene tingathe kuti tizipezeka pamisonkhano ndi kulandila thandizo la Mulungu kudzela mwa mzimu wake.

PAMISONKHANO TIMATHANDIZA ENA

8. Kodi kupezeka pamisonkhano, kupeleka mayankho, ndi kuimba nyimbo zimathandiza bwanji Akristu anzathu? (Onaninso Bokosi lakuti “Amamvelako Bwino Akapezeka Pamisonkhano.”)

8 Pamisonkhano, timakhala ndi mwai woonetsa kuti timakonda abale ndi alongo athu. Anthu ambili mumpingo akukumana ndi mavuto aakulu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tiyeni tiganizilane.” (Aheberi 10:24, 25) Tingasonyeze kuti timakonda abale athu mwa kupezeka pamisonkhano kuti tilimbikitsane. Tikasonkhana, timaonetsa kuti timafuna kuceza ndi abale athu ndiponso kudziŵa mmene zinthu zilili paumoyo wao. Ndipo timawalimbikitsanso mwa kupeleka mayankho ndi kuimba nyimbo mocokela pansi pamtima.—Akolose 3:16.

9, 10. (a) Fotokozani mmene mau a Yesu a pa Yohane 10:16 amatithandizila kumvetsa cifukwa cake kupezeka pamisonkhano n’kofunika kwambili. (b) Kodi kupezekapo kwathu pamisonkhano kungathandize bwanji anthu amene anakanidwa ndi mabanja ao?

9 Tikamapezeka pamisonkhano, timathandiza kuti mpingo ukhale wogwilizana. (Ŵelengani Yohane 10:16.) Yesu anakamba kuti iye ali monga m’busa, ndipo otsatila ake ali ngati gulu la nkhosa. Ganizilani izi: Ngati nkhosa ziŵili zili pa phili, zina ziŵili zili m’cigwa, ndipo ina imodzi ili kwina kwake, kodi tingati nkhosa zisanu zimenezi ndi gulu? Iyai, cifukwa gulu la nkhosa limakhala pamodzi ndipo limatsatila m’busa. Mofananamo, sitiyenela kutalikilana ndi abale athu mwa kuphonya misonkhano. Tiyenela kusonkhana pamodzi kuti tikhale mbali ya “gulu limodzi” ndi kutsatila “m’busa mmodzi.”

10 Misonkhano imatithandiza kukhala ogwilizana monga anthu a m’banja limodzi amene amakondana. (Salimo 133:1) Ena mumpingo anakanidwa ndi abale ao akuthupi kuphatikizapo makolo. Koma Yesu analonjeza kuti adzawapatsa banja lina limene lidzawakonda ndi kuwasamalila. (Maliko 10:29, 30) Ngati mumasonkhana nthawi zonse, mukhoza kukhala tate, mai, m’bale, kapena mlongo wa Mkristu wina mumpingo wanu. Mfundo imeneyi imatilimbikitsa kupezeka pamisonkhano nthawi zonse.

AMAMVELAKO BWINO AKAPEZEKA PAMISONKHANO

“POSACEDWAPA, ndinayamba kudwala matenda amene amacititsa kuti ndizivutika kufika pamisonkhano. Koma ndikakhala ndi mwai wopezekapo, ndimasangalala ndi cakudya cakuuzimu cimene Yehova amakonza. Popita kumisonkhano ndimakhala kuti sindikumvela bwino cifukwa ca matenda a shuga, vuto la mtima, ndi kuŵaŵa kwa nkhongono. Koma pambuyo pamisonkhano, ndimamvelako bwino.

“Tsiku loyamba kumva nyimbo nambala 68, ya mutu wakuti ‘Pemphero la Munthu Wovutika,’ ikuimbidwa pamisonkhano, ndinakhudzika kwambili cakuti ndinagwetsa misozi. Nyimboyo inaimbidwa bwino kwambili. Makina amene amandithandiza kuti ndizimvetsela bwino, anandithandiza kumva mau a anthu onse amene anali kuimba ndipo ndinaimba nao pamodzi. Kukamba zoona, ndinasangalala kwambili kupezekapo.”—George, wa zaka 58.

TIDZAKONDWELETSA YEHOVA

11. Kodi pamisonkhano timakhala ndi mipata iti yolambila Yehova?

11 Pamisonkhano, timalambila Yehova. Popeza iye ndiye anatilenga, tiyenela kumuyamikila, kumulemekeza, ndi kumutamanda. (Ŵelengani Chivumbulutso 7:12.) Tingacite zimenezi pamisonkhano pamene tipemphela kwa Yehova, kumuimbila, ndi kupeleka ndemanga. Ndi mwai waukulu kulambila Yehova mlungu uliwonse.

Yehova amadziŵa kuti timafuna kupezeka pamisonkhano ndipo amayamikila kuyesayesa kwathu

12. Kodi Yehova amamva bwanji tikamvela lamulo lakuti tizipezeka pamisonkhano?

12 Yehova ndiye anatilenga ndipo tifunika kumumvela. Iye anatilamula kuti tizisonkhana, makamaka pamene mapeto akuyandikila. Conco, tikamvela lamulo limeneli, Yehova amakondwela. (1 Yohane 3:22) Iye amadziŵa kuti timafuna kupezeka pamisonkhano ndipo amayamikila kuyesayesa kwathu.—Aheberi 6:10.

13, 14. Kodi kupezeka pamisonkhano kumatithandiza bwanji kuyandikila Yehova ndi Yesu?

13 Tikamasonkhana, timasonyeza kuti tifuna kuyandikila Yehova ndi Mwana wake. Pamisonkhano, timaphunzila Baibulo ndipo Yehova amatiuza zimene tiyenela kucita, ndi mmene tiyenela kukhalila paumoyo. (Yesaya 30:20, 21) Ngakhale anthu ena amene satumikila Yehova, akabwela kumisonkhano yathu, amadziŵa kuti mzimu wa Mulungu umatitsogolela. (1 Akorinto 14:23-25) Yehova amatsogolela misonkhano yathu ndi mzimu wake woyela, ndipo zimene timaphunzila zimacokela kwa iye. Conco tikapezeka pamisonkhano, timamvetsela kwa Yehova ndi kuona cikondi cake, ndipo timamuyandikila kwambili.

14 Yesu, amene ndi mutu wa mpingo anati: “Kulikonse kumene aŵili kapena atatu asonkhana m’dzina langa, ine ndidzakhala pakati pao.” (Mateyu 18:20) Baibulo limakambanso kuti Yesu ‘amayenda pakati’ pa mipingo. (Chivumbulutso 1:20–2:1) N’zoonekelatu kuti Yehova ndi Yesu amakhala nafe pamisonkhano ndipo amatilimbikitsa. Muganiza kuti Yehova amamvela bwanji akaona kuti mukucita zimene mungathe kuti muyandikile iye ndi Mwana wake?

15. Ngati tipezeka pamisonkhano, kodi timaonetsa bwanji kuti tifuna kumvela Mulungu?

15 Tikamapezeka pamisonkhano, timaonetsa kuti tifuna kumvela Yehova. Yehova satikakamiza kuti tizicita zimene amafuna. (Yesaya 43:23) Cotelo, tikamamvela lamulo lake lakuti tizipezeka pamisonkhano, timaonetsa kuti timamukonda ndi kuti timakhulupilila kuti iye ndiye ali ndi ufulu wotiuza zocita. (Aroma 6:17) Mwacitsanzo, kodi mungacite ciani ngati abwana anu afuna kuti muzigwila nchito kwa maola ambili cakuti mukulephela kupezeka pamisonkhano nthawi zonse? Mwina boma lingalamule kuti ngati anthu asonkhana kuti alambile Yehova, ayenela kulipila ndalama, kumangidwa, kapena kupatsidwa cilango cina cacikulu. Nthawi zina, munthu amangosankha mwadala kucita zinthu zina m’malo mopita kumisonkhano. Pa zocitika zonsezi, tiyenela kudzisankhila zocita. (Machitidwe 5:29) Koma nthawi zonse tikasankha kumvela Yehova, iye amakondwela.—Miyambo 27:11.

PITILIZANI KUSONKHANA NDI ABALE

16, 17. (a) Tidziŵa bwanji kuti Akristu oyambilila anali kuona misonkhano kukhala yofunika kwambili? (b) Kodi m’bale George Gangas anali kuiona bwanji misonkhano yacikristu?

16 Kuyambila pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Akristu anali kukumana nthawi zonse kuti alambile Yehova. ‘Anapitiliza kulabadila zimene atumwi anali kuphunzitsa. Iwo anali kugaŵana zinthu’ [‘kusonkhana pamodzi.’ NWT] (Machitidwe 2:42) Anapitilizabe kukumana pamodzi ngakhale pamene anali kuzunzidwa ndi Boma la Aroma ndiponso atsogoleli acipembedzo aciyuda. Ngakhale kuti sicinali copepuka, io anacita zonse zotheka kuti apitilize kusonkhana.

17 Masiku ano, atumiki a Yehova amakonda misonkhano ndiponso amaona kuti ndi yofunika kwambili. M’bale George Gangas, amene anatumikila m’Bungwe lolamulila kwa zaka zoposa 22, anati: “Ndimasangalala kwambili kusonkhana pamodzi ndi abale cifukwa ndimalimbikitsidwa. Ndimakonda kufika mwamsanga pa Nyumba ya Ufumu, ndipo ndimakhala mmodzi wa anthu othela kucoka. Ndimasangalala kuceza ndi anthu a Mulungu. Ndikakhala pamodzi ndi abale ndi alongo, ndimamva ngati ndikuceza ndi banja langa, m’paladaiso wauzimu. Cinthu cimene ndimakonda kwambili ndi kusonkhana.”

18. Kodi misonkhano mumaiona bwanji? Nanga ndinu ofunitsitsa kucita ciani?

18 Kodi inunso mumakonda misonkhano? Ngati mwayankha kuti inde, pitilizani kucita zimene mungathe kuti muzisonkhana pamodzi ndi abale anu ngakhale zitakhala zovuta. Mukatelo, mudzasonyeza kuti muli ndi maganizo monga a Davide amene anati: “Yehova, ine ndimakonda nyumba imene inu mumakhala.”—Salimo 26:8.

^ [1] (ndime 3) Abale ndi alongo ena amalephela kufika pamisonkhano pa zifukwa zina zomveka. Mwacitsanzo, ena akudwala matenda aakulu. Abale ndi alongonu, dziŵani kuti Yehova amamvetsa mavuto amene mukukumana nao ndipo amayamikila zonse zimene mumacita kuti mum’lambile. Akulu angawathandize anthu amenewa kuti azimvetsela misonkhano. Angacite zimenezi mwa kulumikiza misonkhano kudzela pa foni kapena kuwajambulila misonkhanoyo.

^ [2] (ndime 3) Onani bokosi lakuti “Cifukwa Cake Tiyenela Kupezeka Pamisonkhano.”

CIFUKWA CAKE TIYENELA KUPEZEKA PAMISONKHANO
Msonkhano wa mpingo

  1. Timaphunzitsidwa ndi Yehova.

  2. Timalimbikitsidwa.

  3. Timalandila thandizo la mzimu woyela wa Mulungu.

  4. Timakhala ndi mwai woonetsa kuti timakonda abale ndi alongo athu.

  5. Timayamba kukonda kwambili abale athu.

  6. Timalambila Yehova.

  7. Timaonetsa kuti tifuna kuyandikila Yehova ndi Mwana wake.

  8. Timaonetsa kuti timafuna kumvela Yehova.

KUFOTOKOZA MAU ENA

  • Timakumana pamodzi kuti tilambile Mulungu: Timakonda Yehova ndiponso timafuna kumumvela. Conco timafuna kumutamanda pamodzi ndi abale athu. Pamisonkhano yathu, timapemphela kwa Yehova, kumuimbila, ndi kupeleka ndemanga. Zimenezi zimam’kondweletsa

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani