LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Mmene Tingakhalile Olekana ndi Dziko
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
    • 3. (a) Kodi Yesu anaziona bwanji ndale za m’nthawi yake? (b) N’cifukwa ciani tinganene kuti otsatila a Yesu odzozedwa amatumikila monga akazembe? (Onani mau a munsi.)

      3 Pamene anali padziko lapansi, Yesu sanali kutenga mbali m’ndale. Koma anaika maganizo ake pa nchito yolalikila za Ufumu wa Mulungu, umene ndi boma lakumwamba limene iye anali kudzalamulila monga Mfumu. (Danieli 7:13, 14; Luka 4:43; 17:20, 21) Conco, pamene anapita kukaonekela pamaso pa Bwanamkubwa waciroma, Pontiyo Pilato, Yesu anati: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Otsatila ake okhulupilika amatengela citsanzo cake mwa kukhala okhulupilika kwa Kristu ndi Ufumu wake, ndi kulalikila za Ufumu umenewo padziko lapansi. (Mateyu 24:14) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Cotelo ndife akazembe m’malo mwa Kristu, . . .  Monga okhala m’malo mwa Kristu tikupempha kuti: ‘Gwilizananinso ndi Mulungu.’”a—2 Akorinto 5:20.

      4. Kodi Akristu onse oona aonetsa bwanji kuti ndi okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu? (Onani bokosi lakuti “Akristu Oyambilila Sanali Kutenga Mbali M’ndale.”)

      4 Popeza akazembe amaimila dziko lina, io saloŵelela m’ndale za m’maiko amene akutumikilamo. Komabe, akazembe amacilikiza boma limene amaimila. N’cimodzimodzi ndi otsatila a Kristu odzozedwa, amene ndi “nzika zakumwamba.” (Afilipi 3:20) Ndipo cifukwa colalikila Ufumu mokangalika, io athandiza mamiliyoni a “nkhosa zina” kuti ‘ayanjanitsidwe ndi Mulungu.’ (Yohane 10:16; Mateyu 25:31-40) Akristu a nkhosa zina amatumikila monga nthumwi za Kristu, pocilikiza abale a Kristu odzozedwa. Magulu onse aŵili amagwilizana pocilikiza Ufumu wa Mesiya, ndipo onse satenga mbali m’ndale.—Ŵelengani Yesaya 2:2-4.

  • Mmene Tingakhalile Olekana ndi Dziko
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
    • a Kuyambila pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Kristu wakhala Mfumu pa mpingo wa Akristu odzozedwa padziko lapansi. (Akolose 1:13) Mu 1914, Kristu analandila mphamvu za ulamulilo pa “ufumu wa dziko.” Conco, Akristu odzozedwa tsopano amatumikilanso monga akazembe a Ufumu wa Mesiya.—Chivumbulutso 11:15.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani