CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 1-3
Yehova ni “Mulungu Amene Amatitonthoza M’njila Iliyonse”
Njila imodzi imene Yehova amatitonthozela ni kupitila mu mpingo wacikhristu. Kodi tingawatonthoze bwanji anthu ofedwa?
Muziwamvetsela popanda kuwadula mawu
“Lilani ndi anthu amene akulila.”—Aroma 12:15
Kuwatumizilako makhadi owalimbikitsa, imelo kapena kuwalembela meseji.—w17.07 15, bokosi
Apempheleleni na kupemphela nawo pamodzi