-
Mmene Timapezela Ndalama Zoyendetsela Nchito za UfumuUfumu wa Mulungu Ukulamulila
-
-
10 Coyamba, timapeleka mwa kufuna kwathu cifukwa cakuti timakonda Yehova ndipo timafuna “kucita zinthu zomukondweletsa.” (1 Yoh. 3:22) Yehova amasangalala kwambili ndi mtumiki wake amene amapeleka ndi mtima wonse. Tiyeni tikambilane mau a mtumwi Paulo okhudza zopeleka za Akristu. (Ŵelengani 2 Akorinto 9:7) Mkristu woona sacita kukakamizidwa kupeleka zopeleka. M’malo mwake, iye amapeleka cifukwa cakuti “watsimikizila mumtima mwake” kuti atelo.c Izi zikutanthauza kuti iye akaona kuti pafunika thandizo amacitapo kanthu kuti athandize. Munthu wotelo amakondedwa ndi Yehova cifukwa cakuti “Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.” Baibulo lina linamasulila mau a pa lembali kuti: “Mulungu amakonda anthu amene amakonda kupatsa.”
-
-
Mmene Timapezela Ndalama Zoyendetsela Nchito za UfumuUfumu wa Mulungu Ukulamulila
-
-
c Katswili wina anakamba kuti mau acigiriki amene anawamasulila kuti “watsimikizila” amatanthauza kuti “munthuyo amayamba waganizila coyamba.” Iye ananenanso kuti: “Ngakhale kuti kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka, tiyenela kuganizila ndi kulinganiza copeleka cathu pasadakhale.”—1 Akor. 16:2.
-