LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakupindulileni Motani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • Phunzilo 10. Munthu akuyang’ana pa lemba limene Mboni ikumuonetsa m’Baibo pa msonkhano wa Mboni za Yehova.

      PHUNZILO 10

      Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakupindulileni Motani?

      Kodi munayamba mwaitanilidwa ku msonkhano wa Mboni za Yehova? Ngati mukalibe kusonkhanapo nawo, mungadodome kupitako kwa nthawi yoyamba. Mungadzifunse kuti: ‘Kodi cimacitika n’ciyani ku misonkhano imeneyi? N’cifukwa ciyani ili yofunika? Ndipo n’cifukwa ciyani niyenela kupitako?’ M’phunzilo lino, muona kuti kusonkhana pamodzi na anthu ena kungakuthandizeni kumuyandikila Mulungu, komanso kungakupindulileni kwambili.

      1. Kodi cifukwa cacikulu cimene Mboni za Yehova zimasonkhanila pamodzi n’ciyani?

      Onani cifukwa cacikulu cosonkhanila pamodzi cimene wolemba Baibo wina anachula. Iye anati: “Pamsonkhano, ndidzatamanda Yehova.” (Salimo 26:12) A Mboni za Yehova nawonso amakondwela ngako kusonkhana capamodzi. Kuzungulila dziko lonse lapansi, iwo amasonkhana wiki iliyonse kuti atamande Mulungu, kuimba nyimbo, na kupemphela. Kangapo m’caka, amakumananso pa misonkhano ikulu-ikulu kuti alambile Mulungu.

      2. Kodi mudzaphunzila ciyani ku misonkhano yathu?

      Pa misonkhano yathu timaphunzila zocokela m’Mawu a Mulungu, ‘kuwafotokozela ndi kumveketsa tanthauzo lake.’ (Ŵelengani Nehemiah 8:8.) Kumeneko, mudzaphunzila za Yehova na makhalidwe ake abwino. Pamene muphunzila zimene Mulungu wacita cifukwa cokukondani, inunso mudzayamba kumukonda kwambili. Mudzadziŵanso mmene angakuthandizileni kuti mukhale na moyo wokhutilitsa.—Yesaya 48:17, 18.

      3. Kodi mungapindule bwanji poceza na anthu ena ku misonkhano?

      Yehova amatilangiza kuti “tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.” (Aheberi 10:24, 25) Ku misonkhano yathu, mudzapeza anthu amene amakondana zenizeni. Amenenso amafunitsitsa kuphunzila zambili ponena za Mulungu, monga inu. Mudzamva kuti poceza amakambilana mfundo zolimbikitsana zocokela m’Baibo. (Ŵelengani Aroma 1:11, 12.) Mudzadziŵananso na anthu ena, okwatila komanso osakwatila, amene akukhalabe acimwemwe ngakhale akukumana na mavuto osiyana-siyana. Izi ndiye zifukwa zina zimene Yehova amafunila kuti tizisonkhana pamodzi nthawi zonse.

      KUMBANI MOZAMILAPO

      Dziŵani mmene misonkhano ya Mboni za Yehova imacitikila, na cifukwa cake muyenela kuyesetsa kumapezekapo.

      4. Misonkhano ya Mboni za Yehova

      Akhristu oyambilila anali kukumana nthawi zonse kuti alambile Yehova. (Aroma 16:3-5) Ŵelengani Akolose 3:16, na kukambilana funso ili:

      • Kodi Akhristu oyambilila anali kum’lambila bwanji Yehova?

      Masiku ano, a Mboni za Yehova nawonso amasonkhana pamodzi nthawi zonse pamalo awo olambilila. Kuti muone mmene misonkhano yawo imacitikila, tambani VIDIYO. Pambuyo pake onani cithunzi ca msonkhano wa mpingo, na kukambilana mafunso aya.

      VIDIYO: N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? (2:13)

      • Kodi mwaona kufanana kotani pa zimene zimacitika pa Nyumba ya Ufumu, na zimene mwaŵelenga pa Akolose 3:16?

      • Pa zimene mwaona mu vidiyo kapena pa cithunzici, n’ciyani cina cimene cakusangalatsani?

      Ŵelengani 2 Akorinto 9:7, na kukambilana funso ili:

      • N’cifukwa ciyani misonkhano ya Mboni za Yehova ni yaulele?

      Pamodzi na mphunzitsi wanu, onani zimene zidzaphunzilidwa pa msonkhano wotsatila.

      • Kodi ni mbali iti ya msonkhano imene idzakusangalatsani kwambili kapena kukuthandizani?

      Kodi mudziŵa?

      Pa jw.org, mungapeze malo na nthawi zocitila misonkhano padziko lonse.

      Zithunzi zoonetsa pa Nyumba ya Ufumu msonkhano usanayambe, uli mkati komanso utatha. Zocitikazi zabwelezedwa pa zithunzi A mpaka D. A. M’bale akukamba nkhani ya m’Baibo pa pulatifomu nthawi ya msonkhano. B. Mlongo apeleka ndemanga pa msonkhano pa mbali ya mafunso na mayankho. C. M’bale akambilana na banja lina pambuyo pa msonkhano. D. M’bale agwilila citseko m’bale wacikulile ku msonkhano kuti aloŵe.
      1. Ku misonkhano yathu kumakhala nkhani zokambidwa, zitsanzo za ulaliki, na mavidiyo. Timayambila nyimbo na pemphelo, kumalizilanso nyimbo na pemphelo

      2. Pa mbali zina za pulogilamu, omvetsela amapemphedwa kupelekapo ndemanga

      3. Aliyense ni wolandilidwa—mabanja, mbeta, okalamba, ngakhale ana

      4. Misonkhano yathu ni yaulele. Mboni za Yehova sizilipilitsa poloŵa kapena kupititsamo mbale ya zopeleka

      5. Kupezeka pa misonkhano kumafuna kulimbika

      Ganizilani citsanzo ca makolo a Yesu pamodzi na ana awo monga banja. Kuti akapezeke ku msonkhano wa pacaka, anali kuyenda mtunda wa makilomita 100 kudutsa m’mapili, kucokela ku Nazareti kupita ku Yerusalemu. Ŵelengani Luka 2:39-42, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi muganiza ulendo wa ku Yerusalemu umenewu unali wopepuka?

      • N’cifukwa ciyani inunso muyenela kulimbikila kuti muzipezekako ku misonkhano?

      • Kodi m’pake kucita kuivutikila misonkhano? Cifukwa ciyani?

      Zithunzi za Yosefe, Mariya, Yesu, na mng’ono wake wa Yesu akukonzekela kunyamuka ulendo. 1. Yosefe akukwezeka matumba pa bulu, pamene Mariya akulonga zakudya. 2. Mapu yoonetsa njila yocokela ku Nazareti kupita ku Yerusalemu.

      Baibo imanena kuti kusonkhana pamodzi kuti tilambile Mulungu n’kofunika kwambili. Ŵelengani Aheberi 10:24, 25, na kukambilana funso ili:

      • N’cifukwa ciyani tiyenela kupezeka ku misonkhano nthawi zonse?

      ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “N’kosafunikila kucita kupita ku misonkhano. Ukhoza kumangoŵelenga Baibo kunyumba.”

      • Ni lemba liti, kapena citsanzo ca m’Baibo, cimene cionetsa zimene Yehova amafuna?

      CIDULE CAKE

      Kupezeka ku misonkhano kudzakuthandizani kudziŵa zambili za Yehova, kulimbitsa ubwenzi wanu na iye, komanso kum’lambila pamodzi na ŵena.

      Mafunso Obweleza

      • N’cifukwa ciyani Yehova amatilimbikitsa kuti tizisonkhana pamodzi?

      • Kodi mudzaphunzila ciyani ku misonkhano ya Mboni za Yehova?

      • Kodi mungathandizikenso m’njila zina ziti popezeka ku misonkhano?

      Colinga

      FUFUZANI

      Bwanji ngati mumadodoma zakuti mukapezeke ku msonkhano? Onani mmene munthu wina amene anali kumva motelo anayambila kukonda misonkhano.

      Sitidzaiŵala Moni Umene Anatipatsa (4:16)

      Onani zimene mnyamata wina anali kucita kuti azikondwela nayo misonkhano komanso kuti apitilize kupezekako.

      N’naikonda Ngako Misonkhano! (4:33)

      Onani mmene ena amaionela nkhani yosonkhana.

      “N’cifukwa Ciani Mufunika Kupezeka ku Misonkhano ku Nyumba ya Ufumu?” (Nkhani ya pawebusaiti)

      Onani mmene mmodzi wa m’gulu la zigaŵenga anasinthila umoyo wake atapezeka ku msonkhano wa Mboni za Yehova.

      “Kulikonse Kumene Ndinali Kupita Ndinali Kukhala ndi Mfuti Yanga” (Nsanja ya Mlonda, July 1, 2014)

  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulila Pali Pano!
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 5. Dziko linasintha kucokela mu 1914

      Tambani VIDIYO..

      VIDIYO: Dziko Linasintha Kucokela mu 1914 (1:10)

      Yesu ananenelatu zimene zidzacitika padziko lapansi, zoonetsa kuti iye wakhala Mfumu. Ŵelengani Luka 21:9-11, na kukambilana funso ili:

      • Mwa zocitika zimenezi, kodi ni ziti zimene mwaonapo kapena kumvako?

      Mtumwi Paulo anafotokoza mmene anthu adzakhalila m’masiku otsiliza a ulamulilo wa anthu. Ŵelengani 2 Timoteyo 3:1-5, na kukambilana funso ili:

      • Mwa makhalidwe amenewa, ni ati amene mukuona mwa anthu masiku ano?

      Cithunzi coonetsa zocitika za m’dziko na makhalidwe a anthu m’masiku otsiliza. 1. Mkulu wa asilikali wakweza manja m’mwamba akulankhula paguwa mokweza mawu. 2. Zimango zogumuka cifukwa ca civomezi. 3. Ndeke za nkhondo. 4. Anthu akuyenda pabwalo atavala mamasiki. 5. Nyumba zansanjika ziŵili zochedwa Twin Towers zikuyaka moto zitaphulitsidwa na zigaŵenga. 6. Munthu akuseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo. 7. Mwamuna wakweza nkhonya akufuulila mkazi wake mwamphamvu. 8. Mankhwala osokoneza bongo osiyana-siyana komanso moŵa wamitundu-mitundu. 9. Azimayi aŵili ovala zovala za mufashoni komanso zokoloŵeka-koloŵeka, ndipo akudzijambula. 10. DJ akuliza nyimbo ndipo gulu la anthu likuvina. 11. Munthu wocita zacipolowe akuponya botolo loyaka moto kuti likaphulike.

      6. Kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila kuyenela kutilimbikitsa kucitapo kanthu

      Ŵelengani Mateyu 24:3, 14, na kukambilana mafunso aya:

      • Ni nchito iti yofunika imene ikuonetsa kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila pali pano?

      • Kodi mungacite ciyani kuti mutengeko mbali pa nchito imeneyi?

      Ufumu wa Mulungu unayamba kale kulamulila, ndipo posacedwa udzayamba kuyendetsa zinthu zonse padziko lapansi. Ŵelengani Aheberi 10:24, 25, na kukambilana funso ili:

      • Kodi aliyense wa ife ayenela kucita ciyani pamene ‘tikuona kuti tsikulo likuyandikila’?

      Cithunzi: 1. Wophunzila Baibo ali pa msonkhano wa Mboni za Yehova. 2. Wophunzila ameneyonso akulalikila munthu wina wodziŵana naye.

      Ngati mudziŵa zinthu zimene zingathandize anthu ena na kuwapulumutsa, kodi mungacite ciyani?

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani