LEMBA LA MWEZI: “LALIKILA MAU. LALIKILA MODZIPELEKA.”—2 Tim. 4:2.
Gwilitsilani Nchito Mipata Imene Muli Nayo Kufalitsa Uthenga wa Ufumu
1. Kodi citsanzo ca Davide citiphunzitsa ciani?
1 Mfumu Davide sanalole zinthu zimene zinam’citikila pa umoyo wake kumusokoneza. Mwacitsanzo, Davide anali kufuna kumanga nyumba ya Yehova. Koma pamene analetsedwa kucita zimenezo, Davide anasintha zolinga zake ndipo anathandiza Solomo kusonkhanitsa zinthu zomangila kacisi. (1 Maf. 8:17-19; 1 Mbiri 29:3-9) M’malo moika maganizo ake pa zinthu zimene sakanatha kucita, iye anaika maganizo ake pa zinthu zimene anaona kuti angakwanitse kucita. Tingatengele bwanji citsanzo ca Davide pamene tifunafuna mipata yofalitsila uthenga wa Ufumu?
2. Kodi tiyenela kudzipenda motani?
2 Citani Zimene Mungathe: Anthu ambili asankha kukhala ndi moyo wosalila zambili n’colinga cakuti acite upainiya wothandiza kapena wanthawi zonse. (Mat. 6:22) Kodi inunso mungacite nao upainiya? Mukapenda mmene zinthu zilili pa umoyo wanu mwapemphelo, mungaone kuti “khomo lalikulu la mwai wa utumiki” lakutsegukilani. Ngati ndi conco, ugwilitsileni nchito mpata umenewo.—1 Akor. 16:8, 9.
3. Ndi mipata ina iti imene tingagwilitsile nchito ngati sitingakwanitse kucita upainiya?
3 Koma bwanji ngati simungakwanitse kucita upainiya? Simuyenela kunyalanyaza mipata ina imene mungakhale nao yolalikila. Mwacitsanzo, ngati mumagwila nchito ndi anthu osakhulupilila, mungagwilitsile nchito mpata umenewu kuwalalikila. Ngati mukudwala ndipo muli ku cipatala, mungathe kulalikila madokotala ndi manesi. Kumbukilani kuti ofalitsa amene sangakwanitse kucita zambili mu utumiki wakumunda cifukwa ca ukalamba kapena matenda, akhoza kupeleka mphindi 15 za mu utumiki wakumunda. Mukamalemba lipoti lanu la utumiki mwezi uliwonse, musaiŵale kuŵelengela nthawi imene munacita ulaliki wamwai, zofalitsa zimene munagaŵila, kupatikizapo tumapepala twauthenga ndiponso tumapepala toitanila anthu ku Cikumbutso ndi kumsonkhano wacigawo. Mungadabwe kuona kuculuka kwa nthawi imene mumagwilitsila nchito mu ulaliki wa mwamwai mukaŵelengetsa nthawi yonseyo bwinobwino.
4. Kodi mwatsimikiza mtima kucita ciani?
4 Mulimonse mmene zinthu zilili pa umoyo wathu, tiyeni tizigwilitsila nchito mpata uliwonse kufalitsa uthenga wabwino. Tikatelo, tidzakhala okondwela kudziŵa kuti tikucita zonse zimene tingathe kaamba ka Ufumu.—Maliko 14:8; Luka 21:2-4.