LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Ndandanda ya Mlungu wa May 27
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013 | May
    • Ndandanda ya Mlungu wa May 27

      MLUNGU WA MAY 27

      Nyimbo 6 ndi Pemphelo

      □ Phunzilo la Baibo la Mpingo:

      bt Mutu 23 ndime 16-19 ndi bokosi patsamba 188 (Mph. 30)

      □ Sukulu ya Ulaliki:

      Kuŵelenga Baibo: Yohane 12-16 (Mph. 10)

      Na. 1: Yohane 12:20-36 (Mph. 4 kapena zocepelapo)

      Na. 2: Kodi Nsembe ya Yesu Inagwila Nchito Coyamba Kwa Ndani, Ndipo Colinga Cake Cinali Cotani?—rs tsa. 124 ndime 2-3 (Mph. 5)

      Na. 3: N’cifukwa Ciani M’pomveka Kunena Kuti Yehova Ndi “Mulungu Amene Amapatsa Mtendele”?—Aroma 15:33 (Mph. 5)

      □ Msonkhano wa Nchito:

      Nyimbo 98

      Mph. 5: Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba. Nkhani. Onetsani mmene tingayambitsile phunzilo pa Ciŵelu coyamba mu June, mwa kugwilitsila nchito nkhani ili kucikuto cakumapeto kwa Nsanja ya Olonda. Limbikitsani onse kutengako mbali.

      Mph. 15: Kuthilila Mbeu Zimene Tinabzala. (1 Akor. 3:6-9) Nkhani yokambilana yozikidwa pa mafunso otsatila: (1) N’ciani cimakusangalatsani popanga maulendo obwelelako? (2) Kodi n’ciani cimavuta ena kupanga maulendo obwelelako? (3) Kodi angalimbane nao bwanji mavuto amenewa? (4) Ndi kuti kumene tingapeze thandizo ngati zimativuta kupanga maulendo obwelelako? (5) Kodi mumacita ciani kuti mukumbukile munthu amene anasonyeza cidwi ndi kuti mukumbukile nkhani imene munakambilana naye, cofalitsa cimene munam’siila, ndi zinthu zina zokhudza munthuyo? (6) Kodi mumakonzekela bwanji maulendo anu obwelelako? (7) N’cifukwa ciani ndi bwino kukhala ndi ndandanda mlungu uliwonse ya maulendo obwelelako?

      Mph. 10: “Pemphani Zimene Mufuna.” Kukambilana. Funsani omvela kuti afotokoze mmene apindulila mwa kugwilitsila nchito zofalitsa zimene zinatulutsidwa posacedwapa m’cinenelo cao.

      Nyimbo 101 ndi Pemphelo

  • Pemphani Zimene Mufuna
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013 | May
    • Pemphani Zimene Mufuna

      Kwa zaka zambili, mwina munali kulalikila ndi kuphunzitsa coonadi ca m’Mau a Mulungu mwa kugwilitsila nchito zofalitsa m’cinenelo cimene anthu ambili amakamba cimene si cinenelo canu kapena cinenelo ca anthu acidwi amene mumakumana nao. Tidziŵa kuti timagwila zinthu msanga ndipo timazimvetsa pamene tiphunzila m’cinenelo cathu. Ndiye cifukwa cake, timayesetsa kutembenuza ndi kusindikiza zofalitsa n’colinga cakuti zofalitsa zimenezi zipezeke m’zinenelo zambili kuposa kale lonse. Kodi mumazengeleza kufunsila mabuku oonjezeka maka-maka amene anatuluka pa msonkhano posacedwapa m’cinenelo canu? Kodi mukupempha zimene mufuna kuti muzilalikila mogwila mtima m’gawo lanu? Pansipa pali zofalitsa zimene zipezeka m’Cinyanja ndi m’Cisoli zimene zatuluka posacedwapa:

      ◻ Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!

      ◻ Ndani Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?

      ◻ Mvetselani kwa Mulungu

      ◻ Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya

      Nthawi Imene Mungasunge Zofalitsa: Anthu a m’gawo lanu mwina amadziŵa zinenelo zambili koma amakamba cinenelo cimodzi masiku onse. Mukamalalikila, mungakumane ndi anthu, mabanja amene pocita zinthu zao za tsiku ndi tsiku amagwilitsila nchito cinenelo cosiyana ndi canu kapena cinenelo codziŵika kumaloko. Kodi munafufuza kuti mudziŵe ngati zofalitsa zathu zipezeka m’cinenelo cimeneco? Mpingo ungasungeko zofalitsa zocepa zimene timagwilitsila nchito mu utumiki zimene zipezeka m’cinenelo cimeneco, monga tumapepala twa uthenga, tumabuku tumene tunatulutsidwa posacedwapa, ndi buku la Baibo Imaphunzitsa. Ofalitsa angagaŵile zofalitsa zimenezi kulikonse kumene akumana ndi anthu amene amaŵelenga cinenelo cimeneco.

      Mmene Mungaodele Zofalitsa Zimenezi: Ngati mpingo sumakhala ndi zofalitsa m’cinenelo cimene munthu wacidwi amaŵelenga, kodi mungaode bwanji zofalitsa m’cinenelo cimeneco? Ofalitsa ayenela kufunsa mtumiki wa mabuku kuti adziŵe zofalitsa zimene zili m’cinenelo cimeneco, kotelo kuti aode zofalitsazi pa oda yotsatila ya mpingo.

      Tiyeni tipitilizebe kugwilitsila nchito bwino zofalitsa zathu kuti tithandize anthu “kaya akhale a mtundu wotani,” a cinenelo cotani, kuti “apulumuke ndi kukhala odziŵa coonadi molondola.”—1 Tim. 2:3, 4.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani