LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr18 April masa. 1-5
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
  • Tumitu
  • APRIL 2-8
  • APRIL 9-15
  • APRIL 16-22
  • APRIL 23-29
  • APRIL 30–MAY 6
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
mwbr18 April masa. 1-5

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

APRIL 2-8

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 26

“Pasika na Cikumbutso—Kulingana na Kusiyana Kwake”

nwtsty Zithunzi

Cakudya ca pa Pasika

Zakudya zimene zinali zofunika ngako pa mwambo wa Pasika zinali: nkhosa yowocha (nyamayo siinali kufunika kuthyoledwa fupa lililonse) (1); mkate wopanda cofufumitsa (2); na ndiyo zoŵaŵa zamasamba (3). (Eks. 12:5, 8; Num. 9:11) Mwacionekele zakudya zoŵaŵa zamasamba zinali kukumbutsa Aisiraeli umoyo woŵaŵa wa ukapolo ku Iguputo. Yesu anaseŵenzetsa mkate wopanda cofufumitsa monga coimila thupi lake langwilo. (Mat. 26:26) Ndipo mtumwi Paulo anacha Yesu kuti “nsembe yathu ya Pasika.” (1 Akor. 5:7) M’zaka 100 zoyambilila vinyo (4) unali kukhalapo pa cakudya ca Pasika. Yesu anaseŵenzetsa vinyo kuimila magazi ake, amene anali kudzakhetsedwa monga nsembe.—Mat. 26:27, 28.

nwtsty mfundo zounikila pa Mat. 26:26

ukuimila: Liu la Cigiriki lakuti e·stinʹ (limene liu lake leni-leni ndi “ni”) palembali lipeleka lingalilo la “kuonetsa, kuphiphilitsila; kutanthauza.” Tanthauzo la liuli atumwi analimvetsa cifukwa pa cocitika ici thupi langwilo la Yesu anali kuliona, ndipo anali atatsala pang’ono kudya mkate wopanda cofufumitsa. Conco, mkate sunali thupi leni-leni la Yesu. N‘zocititsa cidwi kuti pa Mat. 12:7, anaseŵenzetsa liu la Cigiriki limeneli, ndipo m’ma Baibo ambili analimasulila kuti “kutanthauza.”

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 26:28

magazi . . . a pangano: Pangano latsopano la pakati pa Yehova na Akhristu odzozedwa, linayamba kugwila nchito cifukwa ca nsembe ya Yesu. (Aheb. 8:10) Palembali, Yesu anaseŵenzetsa mau amene Mose anaseŵenzetsa pamene anali m’khalapakati, pokhazikitsa pangano la Cilamulo ndi Aisiraeli pa Phili la Sinai. (Eks. 24:8; Aheb. 9:19-21) Molingana na mmene magazi a ng’ombe na mbuzi anatheketsela pangano la Cilamulo pakati pa Mulungu na mtundu wa Aisiraeli, magazi a Yesu anatheketsa pangano latsopano limene Yehova anapanga na Isiraeli wauzimu. Pangano limenelo linayamba kuseŵenza pa Pentekosite, mu 33 C.E.—Aheb. 9:14, 15.   

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 26:17

Pa tsiku loyamba la cikondwelelo ca mikate yopanda cofufumitsa: Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Cofufumitsa cinali kuyamba pa Nisani 15, pambuyo pa tsiku la Pasika (Nisani 14). Cikondweleloci cinali kutenga masiku 7. (Onani gawo 19 mu Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu) Komabe, m’nthawi ya Yesu, mwambo wa Pasika unali kugwilizana kwambili na cikondweleloci cakuti nthawi zina masiku onse 8, kuŵelengela pamodzi na Nisani 14, anali kuwacha “cikondwelelo ca mikate yopanda cofufumitsa.” (Luka 22:1) Pa vesiyi, mau akuti, “Pa tsiku loyamba la,” m’mau ena tingakambe kuti “lisanafike tsiku la.” (Yelekezelani na Yoh. 1:15, 30. Palembali, liu la Cigiriki lotanthauza “loyamba” [proʹtos] linamasulidwa kuti “ndisana” m’ciganizo colinganako cakuti “anakhalapo ine ndisanabadwe [proʹtos].”) Conco, malinga na Cigiriki coyambilila komanso cikhalidwe ca Ayuda, pa Nisani 13 m’pamene ophunzila a Yesu anamufunsa funso lili palembali. M’masana pa Nisani 13, ophunzila anakonzekela Pasika, imene inacitika “cakumadzulo ndithu” pamene tsiku la Nisani 14 linali kuyamba.—Maliko 14:16, 17.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 26:39

kapu iyi indipitilile: Baibo nthawi zambili imaseŵenzetsa mophiphilitsa liu lakuti “kapu” potanthauza cifunilo ca Mulungu, kapena “cifunilo cake” pa munthu. Mwacionekele, Yesu anali na nkhawa yaikulu yakuti imfa yake idzabweletsa citonzo pa Mulungu, cifukwa anthu anamunamizila kuti anali kunyoza Mulungu na kuukila boma. Izi ndizo zinamusonkhezela kupemphela kuti “kapu” imeneyo imupitilile.   

APRIL 9-15

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 27-28

“Pitani Mukapange Ophunzila—Cifukwa ciani, Kuti, ndipo Motani?”

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 28:19

mukaphunzitse anthu: Liu la Cigiriki lakuti ma·the·teuʹo lingatanthauze “kuphunzitsa” uli na colinga copanga ophunzila kapena otsatila. (Yelekezelani na Mat. 13:52, pamene anaseŵenzetsa liu lakuti “akaphunzitsidwa.”) Mau akuti “muziwabatiza” ndi “kuwaphunzitsa” aonetsa zimene munthu afunika kucita potsatila lamulo lakuti “mukaphunzitse anthu.”

anthu a mitundu yonse: Kumasulila kwake kweni-kweni ni “mitundu yonse,” koma vesiyi ionetsa kuti liuli litanthauza anthu a mtundu uliwonse. Zili conco cifukwa liu la Cigiriki lofotokoza anthu amene tifunika kuwabatiza limatanthauza anthu osati “mitundu.” Lamulo lakuti mukaphunzitse “anthu a mitundu yonse” linali latsopano. Yesu akalibe kuyamba utumiki wake, Malemba amaonetsa kuti anthu a mitundu ina anali kulandilidwa pakati pa Aisiraeli ngati afuna kutumikila Yehova. (1 Maf. 8:41-43) Komabe, m’lamulo ili, Yesu analamula ophunzila ake kuti afunikanso kulalikila anthu ena osati cabe Ayuda. Mwa ici, iye anaonetsa kuti nchito yopanga ophunzila ifunika kucitika kulikonse padzikoli.—Mat. 10:1, 5-7; Chiv. 7:9.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 28:20

kuwaphunzitsa: Liu la Cigiriki lomasulidwa kuti “kuphunzitsa” limaphatikizapo kulangiza, kufotokoza, kupeleka zifukwa, na kupeleka umboni. Kuphunzitsa anthu kusunga zinthu zonse zimene Yesu anatilamula ni nchito yofunika kucitika mosalekeza. Iphatikizapo kuphunzitsa ena zimene Yesu anatiphunzitsa, kucita zimene anatiphunzitsa, na kutengela citsanzo cake.—Yoh. 13:17; Aef. 4:21; 1 Pet. 2:21.   

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 27:51

nsalu yochinga: Nsalu yokongola imeneyi inali kulekanitsa Malo Oyela Koposa na Malo Oyela m’kacisi. Zolemba za Ayuda zionetsa kuti nsalu yaikulu imeneyi inali mamita 18 m’litali, mamita 9 m’lifupi komanso masentimita 7.4 kutikama kwake. Pamene Yehova anang’amba pakati nsalu imeneyi, sanangoonetsa mkwiyo wake kwa amene anapha Mwana wake, koma anaonetsanso kuti lomba khomo loloŵela kumwamba linatseguka.—Aheb. 10:19, 20.

nyumba yopatulika: Liu lake la Cigiriki ni na·osʹ. Apa liuli litanthauza nyumba ya pakati pa kacisi, mmene munali Malo Oyela na Oyela Koposa.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 28:7

mukauze ophunzila ake kuti wauka kwa akufa: Azimayiwa anali ophunzila oyamba kuuzidwa za kuuka kwa Yesu. Ndi amenenso anauzidwa kuti akadziŵitseko ophunzila ena. (Mat. 28:2, 5, 7) Malinga na miyambo ya Ayuda yosacokela m’Malemba, khoti siinali kulola umboni wocokela kwa mkazi. Mosiyana na izi, mngelo wa Yehova analemekeza azimayiwa mwa kuwapatsa nchito yokondweletsa imeneyi.   

APRIL 16-22

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MALIKO 1-2

“Macimo Ako Akhululukidwa”

nwtsty mfundo younikila pa Maliko 2:9

Capafupi n’citi: Cingakhale cosavuta munthu kukamba kuti angakhululukile munthu, cifukwa sipakhala umboni wotsimikizila zokamba zake. Koma kukamba kuti nyamuka ndipo . . . Uyende, kunafuna kuti Yesu acite cozizwitsa kuti onse aone umboni wakuti anali na mphamvu zokhululukila macimo. Lembali komanso la Yes. 33:24 aonetsa kuti timadwala cifukwa ca ucimo.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Maliko 1:11

panamveka mau ocokela kumwamba: Mabuku a Uthenga wabwino aonetsa kuti Yehova anakamba mwacindunji na anthu katatu. Aka kanali koyamba.—Onani mfundo zounikila pa Maliko 9:7; Yoh. 12:28.

ndiwe Mwana wanga: Pamene anali colengedwa cauzimu kumwamba, Yesu anali Mwana wa Mulungu. (Yoh. 3:16) Kucokela pamene Yesu anabadwa monga munthu, anali “mwana wa Mulungu” monga mmene Adamu analili asanacimwe. (Luka 1:35; 3:38) Komabe, cioneka kuti zimene Mulungu anakamba pavesiyi zinatanthauza zambili zokhudza Yesu. Pamene Mulungu anakamba mau amenewa na kupatsa Yesu mzimu woyela, mosakayikila anaonetsa kuti Yesuyo “wabadwanso” monga Mwana wake wauzimu. Apa Yesu anali na ciyembekezo cobwelela kumwamba ndi kudzozedwa na mzimu wa Mulungu kuti adzakhale Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe.—Yelekezelani Yoh. 3:3-6; 6:51; Luka 1:31-33; Aheb. 2:17; 5:1, 4-10; 7:1-3.   

ndimakondwela nawe: Kapena kuti “umanikondweletsa ngako; nimasangalala nawe kwambili.” Mau amodzi-modziwa ni amene alinso pa Mat. 12:18, ogwidwa kucokela pa Yes. 42:1 amene akamba za Mesiya wolonjezedwa kapena kuti Khristu. Kudzozedwa kwa Yesu na zimene Mulungu anakamba zokhudza iye zinapeleka umboni wosatsutsika wakuti Yesu ni Mesiya wolonjezedwa.   

nwtsty mfundo younikila pa Maliko 2:28

Mbuye wa Sabata: Tanthauzo la mau awa lipita kwa Yesu iye mwini (Mat. 12:8; Luka 6:5), kuonetsa kuti iye ndiye anali kudzathetsa Sabata mwa kucita nchito imene Atate wake wakumwamba anamupatsa. (Yelekezelani na Yoh. 5:19; 10:37, 38.) Pa Sabata, Yesu anacita zina mwa zozizwitsa zake zazikulu, zimene zinaphatikizapo kucilitsa odwala. (Luka 13:10-13; Yoh. 5:5-9; 9:1-14) Mwacionekele, izi zinacitila cithunzi mpumulo umene Yesu adzabweletsa akadzayamba kulamulila mu Ufumu wake, umene udzakhala ngati mpumulo wa sabata.—Aheb. 10:1.

APRIL 23-29

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MALIKO 3-4

“Kucilitsa pa Sabata”

nwtsty mfundo younikila pa Maliko 3:5

mokwiya ndi kumva cisoni kwambili: Ni Maliko yekha amene analemba mmene Yesu anamvelela ataona kuuma mtima kwa atsogoleli a cipempedzo pa cocitika ici. (Mat. 12:13; Luka 6:10) Petulo, munthu amene anali kukhudzika mtima ngako, ayenela kuti ndiye anafotokozela Maliko momveka bwino mmene Yesu anamvelela.—Onani “Mfundo zokhudza buku la Maliko.”

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo zounikila pa Maliko 3:29

wanyoza mzimu woyela: Kunyoza kutanthuza kutukwana, kukamba mau oipa, kapena opeputsa Mulungu kapena zinthu zopatulika. Popeza mzimu woyela umacokela kwa Mulungu, kuutsutsa mwadala, kapena kukana kuti sugwila nchito ni kunyoza Mulungu. Pa Mat. 12:24, 28 na pa Maliko 3:22 paonetsa kuti atsogoleli acipembedzo aciyuda anaona mzimu wa Mulungu ukugwila nchito mwa Yesu pamene anali kucita zozizwitsa; koma iwo anakamba kuti imeneyo inali mphamvu ya Satana Mdyelekezi.

mlandu wa chimo losatha: Cioneka kuti mauwa atanthauza chimo locita mwadala limene limabweletsa mavuto osatha; palibe nsembe imene ingaphimbe chimo laconco.

APRIL 30–MAY 6

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MALIKO 5-6

“Yesu Ali na Mphamvu Zoukitsa Okondedwa Athu Amene Anamwalila”

nwtsty mfundo younikila Maliko 5:39

sanamwalile ayi, koma akugona: Baibo, kambili imayelekezela imfa na tulo. (Sal. 13:3; Yoh. 11:11-14; Mac. 7:60; 1 Akor. 7:39; 15:51; 1 Ates. 4:13) Yesu anali kudziŵa kuti adzaukitsa kamtsikanako. Conco, iye ayenela kuti anakamba izi cifukwa anali kufuna kuonetsa anthu kuti monga mmene timautsila munthu akagona, naonso akufa angaukitsidwe. Mphamvu imene Yesu anautsila kamtsikana inacokela kwa Atate wake, “amene amapeleka moyo kwa akufa ndipo amanena za zinthu zimene palibe ngati kuti zilipo.”—Aroma 4:17.   

nwtsty mfundo younikila pa Maliko 5:19

ukawauze: Malangizo a Yesu a nthawi zonse anali akuti anthu asalengeze za zozizwitsa zake. (Maliko 1:44; 3:12; 7:36) Koma apa Yesu analangiza munthu amene anacilitsa kuti akauze abululu ake zimene zacitika. Ayenela kuti anacita izi cifukwa anauzidwa kuti acoke m’delalo, ndipo sakanakhala na mwayi wocitila umboni. Cinanso, zikanathandiza kucepetsako mkwiyo wa anthu cifukwa ca nkhani imene inafala ya kufa kwa nkhumba.

nwtsty mfundo younikila Maliko 6:11

sansani fumbi kumapazi anu: Ophunzila akasansa mfumbi ku mapazi awo, zinali kuonetsa kuti alibe mlandu pa tsoka limene Mulungu akanagwetsela anthuwo. Mau olinganako apezekanso pa Mat. 10:14;na pa Luka 9:5. Maliko na Luka anawonjezelapo mau akuti kuti ukhale umboni kwa [kapena kuti, “wokhudza”] iwo. Paulo na Baranaba anacita zimenezi ku Antiokeya wa ku Pisidiya. (Mac. 13:51) Paulo anacitanso zolinganako na izi ku Korinto mwa kukutumula zovala zake na kukamba kuti, “Magazi anu akhale pamitu panu. Ine ndilibe mlandu.” (Mac. 18:6) Ophunzila ayenela kuti anali kudziŵa tanthauzo la kusansa fumbi kumapazi; Ayuda opembedza amene anali kuyenda kumaiko a anthu a mitundu ina anali kukutumula fumbi ku nsapato zawo asanaloŵe m’dela lokhala Ayuda. Koma Yesu sanali kutanthauza izi pamene anali kupeleka malangizo awa kwa ophunzila ake.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani