CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 6-7
Tizipimila Ena Mowolowa Manja
Munthu wowolowa manja amapeleka mokondwela nthawi yake, mphamvu zake, na zinthu zake kuti athandize ena na kuwalimbikitsa.
Mau a Cigiriki amene anawamasulila kuti “khalani opatsa” atanthauza kucita cinthu mosalekeza
Ngati tikhala opatsa, ena adzatikhuthulila m’matumba athu “muyezo wabwino, wotsendeleka, wokhuchumuka ndi wosefukila.” Mau amenewa angatanthauze cizoloŵezi ca ogulitsa malonda amene amaikapo mbasela pa zinthu zimene munthu wagula