July 2-8
LUKA 6-7
Nyimbo 109 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Tizipimila Ena Mowolowa Manja”: (10 min.)
Luka 6:37—Ngati timakhululukila anthu, nawonso adzatikhululukila (“Pitilizani kukhululukila anthu macimo awo ndipo macimo anunso adzakhululukidwa” nwtsty mfundo younikila; w08 5/15 peji 9 mapa. 13-14)
Luka 6:38—Tiyenela kukhala na cizoloŵezi cokhala wopatsa (“Khalani opatsa” nwtsty mfundo younikila)
Luka 6:38—Mlingo umene timapimila anthu ena, iwonso adzatipimila umenewo (“m’matumba anu” nwtsty mfundo younikila)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Luka 6:12, 13—Kodi Yesu anapeleka bwanji citsanzo cabwino kwa Akhristu pofuna kupanga zosankha zazikulu? (w07 8/1 peji 6 pala. 1)
Luka 7:35—Kodi mau a Yesu angatithandize bwanji ngati anthu ena atinenela misece? (“ana ake” nwtsty mfundo younikila)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Luka 7:36-50
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Kubwelelako Koyamba: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo.
Phunzilo la Baibo: (6 min. olo kucepelapo) bhs mape. 197-198 mapa. 4-5
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Tengelani Kuwolowa Manja kwa Yehova: (15 min.) Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:
Kodi Yehova na Yesu anaonetsa bwanji kuti ni owolowa manja?
Kodi Yehova amadalitsa bwanji kuwolowa manja kwathu?
Kodi kukhululuka mowolowa manja kumatanthauza ciani?
Kodi tingakhale owolowa manja na nthawi yathu m’njila ziti?
Tingaonetse bwanji kuwolowa manja poyamikila ena?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 27
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 57 na Pemphelo