LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr19 May masa. 1-6
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
  • Tumitu
  • MAY 6-12
  • MAY 13-19
  • MAY 20-26
  • MAY 27–JUNE 2
  • w13 3/15 5 ¶12
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2019
mwbr19 May masa. 1-6

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

MAY 6-12

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 4-6

“Sitikubwelela M’mbuyo”

w04 8/15 25 ¶16-17

Otopa Koma Osalefuka

16 Kusamalila thanzi lathu lauzimu n’kofunika kwambili. Tikakhala paubwenzi wolimba ndi Yehova Mulungu, tingathe kutopa, koma kumulambila sikumatilemetsa. Yehova ndi amene “alimbitsa olefuka, nawonjezela mphamvu iye amene alibe mphamvu.” (Yesaya 40:28, 29) Mtumwi Paulo amene anadzionela yekha kuti mawu amenewa ndi oona, analemba kuti: “Sitifoka koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wam’kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.”—2 Akorinto 4:16.

17 Ganizilani zimene mawu akuti “tsiku ndi tsiku” akusonyeza. Akusonyeza kuti tsiku ndi tsiku tiyenela kugwilitsila nchito zinthu zimene Yehova watipatsa. Mmishonale wina amene wakhala akutumikila mokhulupilika kwa zaka 43 wakhala akutopa ndiponso kukhumudwa. Koma sanalefuke. Iye anati: “Cakhala cizoloŵezi canga kudzuka m’maŵa kwambili n’colinga coti ndisanayambe nchito iliyonse, ndipemphele kwa Yehova ndi kuŵelenga Mawu ake. Cizoloŵezi ca tsiku ndi tsiku cimeneci candithandiza kupilila mpaka pano.” Zoonadi, tingadalile mphamvu zothandiza za Yehova ngati nthaŵi zonse, inde “tsiku ndi tsiku,” timapemphela kwa iye ndi kusinkhasinkha za makhalidwe ake apamwamba ndiponso malonjezo ake.

it-1 724-725

Kupilila

Sitifunika kutaya ciyembekezo cathu codzakhala na moyo wosatha wopanda chimo. Olo otizunza afune kutipha, ife sititaya ciyembekezo cathu. (Aroma 5:4, 5; 1 Ates. 1:3; Chiv. 2:10) Mavuto amene tikumana nawo pali pano, si kanthu tikawayelekezela na kukwanilitsidwa kwa ciyembekezo cathu. (Aroma 8:18-25) Mavuto alionse amene tingakumane nawo, olo akhale aakulu bwanji, ni “akanthawi ndipo ndi opepuka” tikawayelekezela na moyo wosatha umene tidzakhala nawo. (2 Akor. 4:16-18) Kukumbukila kuti mayeselo amene timakumana nawo ni akanthawi, ndiponso kugwila mwamphamvu ciyembekezo cathu, kungatithandize kusagonja pamene takumana na mayeselo, ndipo tidzakhalabe wokhulupilika kwa Yehova Mulungu.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w12 2/1 28-29

“Muzisangalatsa Yehova”

M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulila anakamba nkhani ya mutu umenewu, womwe ndi wocokela m’Malemba. (2 Akorinto 4:7) Kodi cuma cimene cachulidwa palembali ndi ciani? Kodi cuma cimeneci ndi zimene tikudziŵa kapena nzelu zomwe tili nazo? M’bale Splane ananena kuti: “Cuma cimeneci sicikutanthauza zimenezi. Cuma cimene mtumwi Paulo anali kunena palembali ndi ‘utumiki woonetsela poyela coonadi.’” (2 Akorinto 4:1, 2, 5; Cipangano Catsopano mu Chichewa Ca Lelo.) M’bale Splane anakumbutsa ophunzilawo kuti pa miyezi isanu ya maphunzilo awo, anali kukonzekela utumiki wapadela. Ophunzilawo ayenela kuona kuti utumiki umenewu ndi cinthu camtengo wapatali kwambili.

M’bale Splane anafotokozanso kuti “zonyamulila zoumbidwa ndi dothi” zimene zachulidwa palembali zikutanthauza matupi athu. Iye anafotokoza kusiyana kwa conyamulila cadothi ndi cagolide. Zonyamulila zagolide sizigwilitsidwa nchito kaŵili-kaŵili. Koma zonyamulila zadothi n’zimene zimagwilitsidwa nchito nthawi zambili. Munthu akaika zinthu mu conyamulila cagolide, amaganizila kwambili za conyamulilaco kuposa zinthu zimene wanyamulazo. Ndiyeno M’bale Splane anati: “Nanunso musamakaganizile kwambili za inuyo. Monga amishonale colinga canu n’kuthandiza anthu kudziŵa Yehova. Conco, mukakhale ngati zonyamulila zoumbidwa ndi dothi.”

w09 11/15 21 ¶7

Pitilizani Kukulitsa Cikondi Canu Caubale

7 Nanga bwanji ifeyo? Kodi ‘tingafutukule bwanji mtima wathu’ posonyeza cikondi caubale? Mwacibadwa, sizikhala zovuta kuti anthu a msinkhu umodzi kapena a fuko limodzi azikondana. Ndipo anthu amene amakonda zosangalatsa zofanana nthawi zambili amacezela limodzi. Koma ngati zinthu zimene timacitila limodzi ndi Akhristu ena zikutilepheletsa kuceza ndi ena, tiyenela ‘kufutukula mtima wathu.’ N’cinthu canzelu kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndi nthawi zingati pamene ndimapita mu utumiki kapena kucita zinthu zosangalatsa ndi abale ndi alongo amene si anzanga apamtima? Ndikakhala ku Nyumba ya Ufumu, kodi ndimapewa kuceza ndi anthu atsopano cifukwa cokhulupilila kuti payenela kupita kaye nthawi asanakhale anzanga? Kodi ndimapeleka moni kwa acikulile ndi ana omwe mumpingo?’

MAY 13-19

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 7-10

“Utumiki Wathu Wothandiza Pakacitika Tsoka”

w98 11/1 25 ¶1

“Mulungu Akonda Wopeleka Mokondwela”

Coyamba, Paulo anauza Akorinto za Amakedoniya, amene anapeleka citsanzo cabwino popeleka thangato. “M’citsimikizo cacikulu ca cisautso, kuculukitsa kwa cimwemwe cawo, ndi kusauka kwawo kweni-kweni zidaculukila kucolemela ca kuwolowa mtima kwawo.” Amakedoniya sanacite kulimbikitsidwa. M’malo mwake, Paulo anati “eni ake, [a]natiumiliza ndi kutidandaulila za cisomoco.” Kupatsa mokondwela kwa Amakedoniya n’kwapadela kwambili makamaka pamene tikumbukila kuti iwo anali ‘osauka kweni-kweni.’—2 Akorinto 8:2-4.

kr 209 ¶1

Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi

CA M’ma 46 C.E, ku Yudeya kunagwa njala yoopsa. Cakudya cinali cocepa ndiponso cokwela mtengo kwambili moti ophunzila a Khristu aciyuda a kumeneko anali kulephela kugula cakudyaco. Iwo anali kuvutika kwambili ndi njala. Koma Yehova anathandiza ophunzila a Khristu amenewo m’njila yapadela kwambili. Kodi anawathandiza bwanji?

kr 209-210 ¶4-6

Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi

4 M’kalata yake yaciŵili yopita kwa Akorinto, Paulo ananena kuti utumiki wacikhristu uli ndi mbali ziŵili zofunika. Ngakhale kuti kalatayi analembela Akhristu odzozedwa, mawu ake amakhudzanso “nkhosa zina” za Khristu. (Yoh. 10:16) Mbali yoyamba ya utumiki wathu ndi “utumiki wokhazikitsanso mtendele,” kapena kuti nchito yolalikila ndi kuphunzitsa. (2 Akor. 5:18-20; 1 Tim. 2:3-6) Mbali ina ndi utumiki umene timacita pothandiza okhulupilila anzathu. Paulo anakamba momveka bwino kuti umenewu ndi “utumiki wothandiza” ena. (2 Akor. 8:4) M’Baibo muli mawu akuti “utumiki wokhazikitsanso mtendele” ndi akuti “utumiki wothandiza” oyelawo. M’mawu onsewa, liwu lakuti “utumiki” linamasulidwa kucokela ku liwu limodzi lacigiriki lakuti di·a·ko·niʹa. N’cifukwa ciani zimenezi n’zocititsa cidwi?

5 Mwa kugwilitsila nchito liwu lacigiriki lofanana ponena za mautumiki aŵiliwo, Paulo anaonetsa kuti nchito yopeleka thandizo ndi yofanana ndi mautumiki ena amene anali kucitika mumpingo wacikhristu. Asanakambe za mautumiki amenewa, iye anati: “Pali mautumiki osiyanasiyana, koma Ambuye ndi mmodzi. Palinso nchito zosiyanasiyana, . . . Koma nchito zonsezi, mzimu umodzi-modziwo ndiwo umazicita.” (1 Akor. 12:4-6, 11) Paulo anasonyeza kuti mautumiki osiyanasiyana amene amacitika pampingo ndi “utumiki wopatulika.” (Aroma 12:1, 6-8) Ndiye cifukwa cake iye anagwilitsila nchito nthawi yake ‘kutumikila oyela.’—Aroma 15:25, 26.

6 Paulo anathandiza Akhristu a ku Korinto kuzindikila kuti nchito yopeleka thandizo ndi mbali ya kulambila Yehova, ndiponso kuti ndi mbali ya utumiki wawo kwa Iye. Onani kuti iye anakamba kuti Akhristu amene amapeleka thandizo amacita zimenezo cifukwa ‘cogonjela uthenga wabwino wonena za Khristu.” (2 Akor. 9:13) Conco, cimene cimalimbikitsa Akhristu kuthandiza anzawo ndi mtima wawo wofuna kutsatila zimene Khristu anaphunzitsa. Paulo ananena kuti zinthu zabwino zimene Akhristu amacitila abale awo zimaonetsa “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (2 Akor. 9:14; 1 Pet. 4:10) Conco, ponena za nchito yothandiza abale athu amene akuvutika, magazini ya Nsanja ya Olonda ya December 1, 1975 inati: “Tisakayikile kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Khristu amaona utumikiwu kukhala wofunika kwambili.” Zoonadi, nchito yopeleka thandizo ndi mbali yofunika kwambili ya utumiki wopatulika.—Aroma 12:1, 7; 2 Akor. 8:7; Aheb. 13:16.

kr 196 ¶10

Mmene Timapezela Ndalama Zoyendetsela Nchito za Ufumu

10 Coyamba, timapeleka mwa kufuna kwathu cifukwa cakuti timakonda Yehova ndipo timafuna “kucita zinthu zomukondweletsa.” (1 Yoh. 3:22) Yehova amasangalala kwambili ndi mtumiki wake amene amapeleka ndi mtima wonse. Tiyeni tikambilane mawu a mtumwi Paulo okhudza zopeleka za Akhristu. (Ŵelengani 2 Akorinto 9:7) Mkhristu woona sacita kukakamizidwa kupeleka zopeleka. M’malo mwake, iye amapeleka cifukwa cakuti “watsimikizila mumtima mwake” kuti atelo. Izi zikutanthauza kuti iye akaona kuti pafunika thandizo amacitapo kanthu kuti athandize. Munthu wotelo amakondedwa ndi Yehova cifukwa cakuti “Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.” Baibo ina inamasulila mawu a pa lembali kuti: “Mulungu amakonda anthu amene amakonda kupatsa.”

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w16.01/15 9 ¶2

Muzilimbikitsidwa ndi Mphatso ya Mulungu Yosatheka Kuifotokoza

2 Paulo anadziŵa kuti nsembe ya Yesu ndi citsimikizo cakuti Mulungu adzakwanilitsa malonjezo ake onse. (Ŵelengani 2 Akorinto 1:20.) Izi zitanthauza kuti “mphatso [ya Mulungu] yaulele imene sitingathe n’komwe kuifotokoza” imaphatikizapo nsembe ya Yesu, zinthu zonse zabwino zimene Yehova amaticitila, ndiponso kukoma mtima kwake. Mphatso imeneyi ndi yamtengo wapatali kwambili cakuti sitingathe kuifotokoza mokwanila. Kodi tiyenela kumva bwanji tikaganizila mphatso yamtengo wapatali imeneyi? Nanga iyenela kutilimbikitsa kucita ciani pamene tikukonzekela Cikumbutso ca imfa ya Khristu cimene cidzacitika pa Citatu, pa March 23, 2016?

g99 7/8 20-21

Kodi Kunyada N’kulakwa?

M’Malemba Acigiriki acikhristu, velebu lakuti kau·khaʹo·mai, lotanthauza “kunyadila, kukondwela, kudzitamandila,” limagwilitsidwa nchito ponse paŵili m’lingalilo loipa ndi labwino. Mwacitsanzo, Paulo akuti, ndipo ‘tikondwele m’ciyembekezo ca ulemelelo wa Mulungu.’ Komanso akulangiza kuti: “Koma iye wodzitamandila adzitamandile mwa Ambuye.” (Aroma 5:2; 2 Akorinto 10:17) Izi zikutanthauza kunyadila Yehova monga Mulungu wathu, kumene kungatipangitse kukondwelela dzina ndi mbili yake yabwino.

MAY 20-26

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 11-13

“‘Munga M’thupi’ la Paulo”

w08 6/15 3-4

Tingakhale Amphamvu Ngakhale Tili Ndi Zofooka

Mtumiki wokhulupilika Paulo anapempha Yehova kuti amucotsele “munga m’thupi,” kutanthauza vuto losathelapo. Mtumwiyu anacondelela Mulungu katatu konse kuti amucotsele vutoli. Sitikudziŵa kuti vutolo linali lotani, komabe mofanana ndi munga womwe umasoŵetsa mtendele, likanatha kum’landa cimwemwe cake potumikila Yehova. Paulo anayelekezela vutolo ndi kumenyedwa nthawi zonse. Poyankha, Yehova anati: “Kukoma mtima kwa m’cisomo canga kwakukwanila; pakuti mphamvu yanga imakhala yokwanila m’kufooka.” Yehova sanacotse munga m’thupi umenewo. Paulo anapitiliza kulimbana nawo, koma ananena kuti: “Pamene ndili wofooka, m’pamene ndili wamphamvu.” (2 Akor. 12:7-10) Kodi anatanthauza ciani?

w06 12/15 24 ¶17-18

Yehova Amapeleka “Mzimu Woyela kwa Amene Akum’pempha”

17 Poyankha mapemphelo a Paulo, Mulungu anamuuza kuti: “Kukoma mtima kwa m’cisomo canga kwakukwanila; pakuti mphamvu yanga imakhala yokwanila m’kufooka.” Paulo anati: “Conco, ndidzadzitama mosangalala kwambili pa kufooka kwanga, kuti mphamvu ya Khristu ikhalebe pamutu panga ngati hema.” (2 Akorinto 12:9; Salmo 147:5) Cotelo, Paulo anaona kuti kudzela mwa Khristu, Mulungu anamufunyululila citetezo cake camphamvu monga hema. Lelonso, Yehova amayankha mapemphelo athu mwanjila yofananayo. Iye amafunyulula citetezo cake kuti cicingile atumiki ake.

18 N’zoona kuti, hema saletsa mvula kuti isagwe kapena mphepo kuti isawombe, koma amangoteteza ku zinthu zimenezo. N’cimodzi-modzinso citetezo cimene cimapelekedwa ndi “mphamvu ya Khristu.” Siletsa ziyeso kuti zisatigwele kapena kuti tisakumane ndi mavuto ayi. Koma, imatiteteza mwauzimu ku zinthu zovulaza za m’dzikoli ndiponso kwa wolamulila wa dzikoli, Satana, akamatiukila. (Chivumbulutso 7:9, 15, 16) Conco, ngakhale ngati mukulimbana ndi ciyeso cimene ‘sicikukucokani,’ mungakhale ndi cikhulupililo coti Yehova akudziŵa za kuvutika kwanu ndiponso kuti wamva ‘kufuula kwanu.’ (Yesaya 30:19; 2 Akorinto 1:3, 4) Paulo analemba kuti: “Mulungu ndi wokhulupilika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile, koma pamene mukukumana ndi mayeselowo iye adzapeleka njila yopulumukila kuti muthe kuwapilila.” —1 Akorinto 10:13; Afilipi 4:6, 7.

w18.01 9 ¶8-9

“Iye Amapeleka Mphamvu kwa Munthu Wotopa”

8 Ŵelengani Yesaya 40:30. Olo titakhala aluso bwanji, pali zinthu zina zimene sitingakwanitse kucita mwa mphamvu zathu zokha. Tonsefe tiyenela kuivomeleza mfundo imeneyi. Mwacitsanzo, ngakhale kuti mtumwi Paulo anali wocita bwino m’zambili, anali na zofooka zina zimene zinali kumulepheletsa kucita zonse zimene anali kufuna. Pamene iye anafotokozela Mulungu nkhawa yake, Mulunguyo anamuuza kuti: “Mphamvu yanga imakhala yokwanila iweyo ukakhala wofooka.” Paulo anamvetsetsa mfundo imeneyi. N’cifukwa cake anati: “Pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.” (2 Akor. 12:7-10) Kodi pamenepa iye anatanthauza ciani?

9 Paulo anadziŵa kuti panali zambili zimene sakanakwanitsa kucita popanda thandizo locokela kwa Mulungu. Koma mzimu woyela wa Mulungu unam’patsa mphamvu. Kuwonjezela apo, unam’thandiza kucita zinthu zimene sakanatha kucita mwa mphamvu zake zokha. N’cimodzi-modzi na ise. Ngati tidalila Yehova, tidzakhala olimba.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w18.12 8 ¶10-12

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

“Kumwamba kwacitatu” kumene Paulo anachula pa 2 Akorinto 12:2, mwacionekele kutanthauza “kumwamba kwatsopano,” kapena kuti Ufumu wa Mesiya wolamulidwa na Yesu Khristu komanso a 144,000.—2 Pet. 3:13.

Ufumu wa Mesiya umachedwa “kumwamba kwacitatu” cifukwa ni ulamulilo wokwezeka komanso wapamwamba kwambili.

“Paradaiso” wa m’masomphenya, amene Paulo ‘anakwatulidwa n’kukalowamo,’ mwacionekele ni (1) Paradaiso weni-weni wa padziko lapansi amene adzakhalapo kutsogolo, (2) paradaiso wauzimu amene adzakhalapo panthawiyo, amene adzakula kwambili kuposa paradaiso wauzimu amene alipo masiku ano, komanso (3) “paradaiso wa Mulungu” wa kumwamba. M’dziko latsopano, maparadaiso onse atatuwa adzakhalapo pa nthawi imodzi.

it-2 177

Kupsompsona

“Kupsompsonana kwaubale.” “Kupsompsonana kwaubale” (Aroma 16:16; 1 Akor. 16:20; 2 Akor. 13:12; 1 Ates. 5:26) kapena kuti ‘kupsompsonana mwa cikondi caubale’ (1 Pet. 5:14), kumene Akhristu oyambilila anali kucita, kuyenela kuti kunali kucitika pakati pa amuna kapena akazi okha-okha. Akhristu oyambilila, aoneka kuti anatengela mtundu wa moni umenewu kwa Aheberi akale, amene anali kupatsana moni mwa kupsompsonana. Olo kuti Malemba siyakamba zambili zokhudza nkhaniyi, “kupsompsonana kwaubale” kapena kuti ‘kupsompsonana mwa cikondi caubale,’ mosakayikila kunali kuonetsa cikondi cacikulu na mgwilizano umene unali mu mpingo wacikhristu.—Yoh. 13:34, 35.

MAY 27–JUNE 2

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AGALATIYA 1-3

“Ndinamutsutsa Pamasom’pamaso”

w17.04 27 ¶16

Kodi Mumacita Zinthu Mogwilizana ndi Cilungamo ca Yehova?

16 Ŵelengani Agalatiya 2:11-14. Petulo anagwela mumsampha woopa anthu. (Miy. 29:25) Iye anali kudziŵa bwino mmene Yehova anali kuonela Akhristu amitundu ina. Koma anaopa kuti Akhristu aciyuda odulidwa a mumpingo wa ku Yerusalemu adzaleka kumulemekeza akaona kuti akuyanjana ndi Akhristu amitundu ina. Mtumwi Paulo, amenenso analipo pa msonkhano umene unacitika ku Yerusalemu mu 49 C.E., anakumana ndi Petulo ku Antiokeya, ndipo anam’dzudzula cifukwa ca zaciphamaso zimene anacita. (Mac. 15:12; Agal. 2:13) Kodi Akhristu amitundu ina anacita ciani ataona zinthu zopanda cilungamo zimene Petulo anawacitila? Kodi anakhumudwa? Kodi Petulo analandidwa maudindo atacita colakwa cimeneci?

w13 3/15 5 ¶12

Anthu Okonda Yehova ‘Alibe Cowakhumudwitsa’

12 Nayenso Petulo analakwitsa zinthu zina cifukwa coopa anthu komabe sanasiye kukhala wokhulupilika kwa Yesu ndi Yehova. Mwacitsanzo, iye anakana Mbuye wake, osati kamodzi koma katatu. (Luka 22:54-62) Pa nthawi inanso, Petulo analephela kucita zinthu ngati Mkhristu. Iye anayamba kusala Akhristu a mitundu ina ngati kuti Akhristu aciyuda ndi amene anali ofunika kwambili. Apatu Petulo analakwitsa. Koma mtumwi Paulo ankadziŵa kuti Akhristu sayenela kusalana. Conco zisanafike posokoneza anthu ena mu mpingo, Paulo anamudzudzula mosapita m’mbali. (Agal. 2:11-14) Kodi Petulo anakhumudwa cifukwa ca kunyada n’kusiya kutumikila Mulungu? Ayi. Iye anaganizila bwino uphungu wa Paulo, kuutsatila ndipo anapitilizabe pa mpikisano wokalandila moyo.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w14 9/15 16 ¶20-21

Tumikilani Mulungu Mokhulupilika Panthawi ya “Masautso Ambili”

20 Nanga bwanji za kuukila mwakabisila? Mwacitsanzo, tingagonjetse bwanji maganizo olefula? Njila imodzi yaikulu imene tingacitile zimenezo ndiyo kuganizila mozama za dipo. N’zimene mtumwi Paulo anacita. Iye nthawi zina anali kudzimva monga munthu wovutika. Koma anadziŵa kuti Khristu sanafele anthu angwilo, koma ocimwa monga iye. Ndiye cifukwa cake analemba kuti: “Moyo umene ndikukhala tsopano, ndikukhala mokhulupilila Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ndi kudzipeleka yekha cifukwa ca ine.” (Agal. 2:20) Paulo anakhulupililadi dipo, ndipo anazindikila kuti limagwilanso nchito kwa iye.

21 Nafenso tingapindule kwambili ngati tikhulupilila kuti dipo ndi mphatso yathu yocokela kwa Yehova. Koma zimenezi sizitanthauza kuti sitidzakumana ndi zinthu zokhumudwitsa. Ena adzapitilizabe kupilila masautso a mwakabisila mpaka m’dziko latsopano. Ndipo tizikumbukila kuti: Amene adzalandila mphoto ndi aja amene amapilila. Tsiku lililonse timayandikila nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzabwela. Ufumuwo ukadzabwela, padziko padzakhala mtendele, ndipo anthu onse adzakhala angwilo. Conco, kaya tikumane ndi masautso ambili motani, tiyeni ticite zimene tingathe kuti tikaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.

it-1 880

Kalata kwa Agalatiya

Mawu amene Paulo anakamba akuti “Kalanga ine, Agalatiya opusa inu,” saonetsa kuti anali kuganizila cabe za mtundu wa anthu ochedwa Agaliki, amene anacokela kumpoto kwa Galatiya. (Agal. 3:1) M’malomwake, Paulo anali kudzudzula anthu a m’mipingoyo amene analola kusoceletsedwa na Ayuda osunga mwambo pakati pawo. Iwo anali kudziyesa olungama cifukwa cotsatila cilamulo ca Mose m’malo mwa “kukhala olungama cifukwa ca cikhulupililo” cozikidwa pa cipangano catsopano. (2:15–3:14; 4:9, 10) Mu “mipingo ya ku Galatiya” (1:2) imene Paulo analembela kalatayi, munali anthu a mitundu yosiyana-siyana, Ayuda na amene sanali Ayuda. Pa anthu amene sanali Ayuda, panali ena odulidwa otembenukila ku Ciyuda, na anthu akunja osadulidwa, ndipo mosakayikila panalinso ena ocokela kumadzulo kwa Europe. (Mac. 13:14, 43; 16:1; Agal. 5:2) Iye anatomola anthuwo kuti Akhristu a ku Galatiya cifukwa anali kukhala m’dela lochedwa Galatiya. Paulo polemba kalatayi, anali kuganizila za anthu a kum’mwela kwa cigawo ca Roma, amene anali kuwadziŵa bwino, osati anthu a kumpoto kwa cigawoco, amene mwina anali asanawacezelepo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani