Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
NOVEMBER 4-10
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 YOHANE 1-5
“Musamakonde Dziko Kapena Zinthu za M’dziko”
w05 1/1 10 ¶13
Tsatilani Citsanzo Cimene Yesu Anatipatsa
Ena angaganize kuti si zinthu zonse za m’dzikoli zomwe zili zoipa. Ngakhale zili conco, dzikoli ndi zokonda zake zingatidodometse kuti tisatumikile bwino Yehova. Ndipo palibe ciliconse ca m’dzikoli cimene colinga cake n’kutilimbikitsa kuyandikana ndi Mulungu. Conco tikayamba kukonda zinthu za m’dzikoli, ngakhale zinthu zimene pazokha si zoipa, ndiye kuti tili pangozi. (1 Timoteo 6:9, 10) Ndiponso, zinthu zambili m’dzikoli n’zoipadi ndipo zingawononge maganizo athu. Ngati tionela mafilimu kapena mapulogalamu a pa TV omwe amasonyeza ciwawa, kukonda cuma, kapena ciwelewele, tingayambe kuona zinthu zimenezo ngati zabwino n’kuyamba kukopeka nazo. Ngati timaceza ndi anthu amene colinga cawo cacikulu m’moyo ndico kukhala opeza bwino kapena kupeza mwayi wabwino wa mabizinezi, zinthu zimenezo zikhozanso kusanduka zofunika kwambili pamoyo wathu.—Mateyu 6:24; 1 Akorinto 15:33.
Ganizilani za Mtundu wa Munthu Amene Muyenela Kukhala
Cinthu cina cimene cingatithandize kukana “zinthu za m’dziko” ndi kukumbukila mawu ouzilidwa a Yohane akuti: “Dziko likupita limodzi ndi cilako-lako cake, koma wocita cifunilo ca Mulungu adzakhala kosatha.” (1 Yoh. 2:17) Dongosolo la Satana lingaoneke monga kuti silidzatha. Koma lidzatha ndithu. Zinthu zilizonse zimene dziko la Satana lingapeleke n’zosakhalitsa. Kukumbukila mfundo imeneyi kungatithandize kupewa misampha ya Mdyelekezi.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nw13 9/1 10 ¶14
Zikumbutso za Yehova Ndi Zodalilika
Malemba Acigiriki Acikhristu ali ndi zikumbutso zambili zotilimbikitsa kuti tizikondana. Yesu anakamba kuti lamulo laciŵili lalikulu ndi lakuti “uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Mat. 22:39) Yakobo m’bale wa Yesu anakambanso kuti cikondi ndi “lamulo lacifumu.” (Yak. 2:8) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Okondedwa, sindikukulembelani lamulo latsopano, koma lamulo lakale limene mwakhala nalo kuyambila pa ciyambi.” (1 Yoh. 2:7, 8) Kodi Yohane anatanthauza ciani pamene anakamba kuti “lamulo lakale”? Anali kutanthauza za lamulo la kukonda anzathu. Lamulo limeneli linali “lakale” m’lingalilo lakuti Yesu analipeleka “kuyambila pa ciyambi,” kutanthauza zaka makumi angapo m’mbuyomo. Koma linalinso “latsopano” cifukwa cakuti ophunzilawo anafunika kuonetsa cikondi codzimana pa nthawi zovuta. Pokhala ophunzila a Khristu, kodi sitimayamikila macenjezo amene amatiteteza kuti tisakhale ndi mzimu wodzikonda wofala m’dzikoli, umene ungacititse kuti cikondi cathu pa abale cicepe?
it-1 862 ¶5
Cikhululukilo
N’koyenela kupempha cikhululukilo kwa Mulungu m’malo mwa anthu ena, ngakhale m’malo mwa mpingo wonse. Izi n’zimene Mose anacitila mtundu wa Aisiraeli. Iye anavomeleza macimo amene mtunduwo unacita na kupempha cikhululukilo, ndipo Yehova anamvela pemphelo lake. (Num. 14:19, 20) Nayenso Solomo popatulila kacisi, anapempha Yehova kuti azikhululukila anthu ake akacimwa ndipo pambuyo pake n’kuleka kucita zoipa. (1 Maf. 8:30, 33-40, 46-52) Ezara, moimila Ayuda amene anabwela kucoka ku ukapolo, anapeleka pemphelo lovomeleza zolakwa zawo. Pemphelo lake locokela pansi pa mtima komanso lolimbikitsa, linakhala na zotuluka zabwino cakuti anthu anasintha zocita zawo kuti Yehova awakhululukile. (Ezara 9:13–10:4, 10-19, 44) Yakobo anakamba kuti munthu wodwala mwauzimu afunika kupempha thandizo kwa akulu mu mpingo kuti amupemphelele, ndipo “ngati anacita macimo, adzakhululukidwa.” (Yak. 5:14-16) Komabe, pali “chimo lobweletsa imfa,” limene ni kucimwila mzimu woyela, kutanthauza cizoloŵezi cocita chimo linalake mwadala. Chimo lotelo lilibe cikhululukilo. Mkhristu safunika kupemphelela anthu amene amacimwa mwanjila imeneyi.—1 Yoh. 5:16; Mat. 12:31; Aheb. 10:26, 27.
NOVEMBER 11-17
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 YOHANE 1:1-14; YUDA 1-25
“Tifunika kumenya Nkhondo kuti Tikhalebe m’Coonadi”
w04 9/15 11-12 ¶8-9
“Tadzilimbikani mwa Ambuye”
Malemba amatiuza njila zimene Satana amakonda kugwilitsila nchito, conco timawadziŵa macenjela ake. (2 Akorinto 2:11) Mdyelekezi polimbana ndi Yobu amene anali wolungama, anagwilitsila nchito mavuto aakulu a zacuma, imfa za anthu amene anali kuwakonda, kutsutsidwa ndi a m’banja lake, matenda, ndiponso kudzudzulidwa popanda cifukwa comveka ndi anthu omwe anali kunamizila kuti ndi anzake. Yobu anafooledwa kwambili n’kuyamba kuganiza kuti Mulungu wamutaya. (Yobu 10:1, 2) Ngakhale kuti Satana masiku ano sangacititse mwacindunji mavuto amenewa, Akhristu ambili timakumana ndi mavuto ngati amenewa, ndipo Mdyelekezi angapezelepo mwayi pamenepo.
M’nthawi zamapeto zino zinthu zimene zingatisokoneze mwauzimu zaculuka kwambili. Tikukhala m’dziko limene anthu amaona kuti cuma ndiye cofunika kwambili kuposa zolinga zauzimu. Nthaŵi ndi nthaŵi zinthu monga mawailesi ndi manyuzipepala zimasonyeza kuti ciwelewele cimabweletsa cimwemwe osati mavuto. Ndipo anthu ambili tsopano ‘ni okonda zokondweletsa munthu, osati okonda Mulungu.’ (2 Timoteyo 3:1-5) Ngati ‘sitilimba cifukwa ca cikhulupililo’ maganizo ngati amenewa angathe kutigwetsa mwauzimu.—Yuda 3.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 279
Maphwando a Cikondi
Baibo siifotokoza zambili zokhudza maphwando a cikondi amenewa, ndiponso siifotokoza ngati maphwandowo anali kucitika kaŵili-kaŵili kapena ayi. (Yuda 12) Sikuti ni Ambuye Yesu Khristu kapena atumwi ake amene analamula kuti maphwandowo azicitika. Zionekanso kuti dongosolo locita maphwando amenewa silinali lacikhalile ndipo panalibe lamulo lakuti Akhristu azicita maphwandowo. Ena amakamba kuti pa nthawiyo, Akhristu olemela anali kukonza phwando na kuitana okhulupilila anzawo osauka. Pa phwandolo, ana amasiye, akazi amasiye, olemela, ndiponso osauka, onse anali kudyela pamodzi zakudya zosiyana-siyana monga abale na alongo.
it-2 816
Mwala
Liwu lina lacigiriki, lakuti spi·lasʹ, lioneka kuti limatanthauza mwala kapena thanthwe lobisika pansi pa madzi. Yuda anaseŵenzetsa mawuwa pokamba za anthu ena amene anabwela mu mpingo wacikhristu ali na zolinga zoipa. Monga mmene miyala yobisika inali kukhalila yoopsa ku ngalawa, anthu amenewo anali kuika ena pa ciwopsezo mu mpingo. Pokamba za iwo, Yuda anati: “Anthu amenewa ali ngati miyala ikulu-ikulu yobisika m’madzi.”—Yuda 12.
‘Mulungu Anakondwela Naye’
Kodi ulosi wa Inoki unali wabwanji? Unali wakuti: “Taonani! Yehova anabwela ndi miyanda-miyanda ya oyela ake, kudzapeleka ciweluzo kwa onse, ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu cifukwa ca nchito zawo zonyoza Mulungu zimene anazicita mosaopa Mulungu, komanso cifukwa ca zinthu zonse zonyoza koopsa zimene ocimwa osaopa Mulungu anamunenela.” (Yuda 14, 15) Mwina mungadabwe kuti mu ulosi umenewu, Inoki anakamba monga kuti Mulungu anali atacita kale zimene ulosiwu unakamba. Umu ndi mmene maulosi ambili analembedwela pambuyo pake. Inoki anakamba ulosi umenewu monga kuti wacitika kale cifukwa zimene anali kukamba zinali zakuti zidzacitikadi zivute zitani.—Yesaya 46:10
‘Mulungu Anakondwela Naye’
Cikhulupililo ca Inoki ciyenela kutilimbikitsa kudzifufuza kuti tione ngati timaona dzikoli monga mmene Mulungu amalionela. Uthenga waciweluzo umene Inoki analengeza ni cenjezo kwa anthu onse masiku ano monga mmene zinalili m’nthawi ya Inoki. Mogwilizana ndi cenjezo la Inoki, Yehova anabweletsa cigumula camadzi cimene cinawononga anthu osaopa Mulungu m’masiku a Nowa. Koma zimene zinacitikazo ni citsanzo ca ciwonongeko cacikulu cimene cidzabwela m’tsogolo. (Mateyu 24:38, 39; 2 Petulo 2:4-6) Molingana ndi masiku akale, masiku ano, Mulungu pamodzi ndi a angelo ake oyela ambili-mbili, ni okonzeka kupeleka ciweluzo kwa anthu osaopa Mulungu. Aliyense wa ife ayenela kumvela cenjezo la Inoki na kucenjezako ena. Tikacita zimenezo, acibale athu angaleke kugwilizana nafe ndipo tingayambe kuona kuti tilibe anzathu. Koma kumbukilani kuti Yehova sanamusiye Inoki, ndipo sangasiyenso atumiki ake okhulupilika masiku ano.
NOVEMBER 18-24
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 1-3
“Ndikudziŵa Nchito Zako”
w12 10/15 14 ¶8
Kodi Mumaonetsa Mzimu Wotani?
Tikhoza kupewa mzimu umenewu tikamakumbukila kuti Baibulo limasonyeza kuti Yesu ali ndi “nyenyezi 7” m’dzanja lake lamanja. “Nyenyezi” zimenezi kweni-kweni zimaimila oyang’anila odzozedwa koma zingaimilenso oyang’anila onse m’mipingo. Yesu angatsogolele “nyenyezi” za m’dzanja lake m’njila iliyonse imene akufuna. (Chiv. 1:16, 20) Popeza Yesu ndi Mutu wa mpingo, amadziwa ciliconse cokhudza akulu mu mpingo. Ngati pali mkulu wina amene ayenela kudzudzulidwa, Yesu amene ali ndi maso “ngati lawi la moto” adzaonetsetsa kuti zimenezi zicitike m’nthawi ndiponso njila yoyenela. (Chiv. 1:14) Pamene tikudikila Yesu, cofunika kucita ndi kulemekeza anthu amene aikidwa ndi mzimu woyela. Paja Paulo analemba kuti: “Muzimvela amene akutsogolela pakati panu ndipo muziwagonjela. Iwo amayang’anila miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvela ndi kuwagonjela kuti agwile nchito yawo mwacimwemwe, osati modandaula, pakuti akatelo zingakhale zokuvulazani.”—Aheb. 13:17.
w12 4/15 29 ¶11
Yehova Amatiteteza Kuti Tidzapulumuke
Masomphenya amene ali m’caputa 2 ndi 3 ca buku la Chivumbulutso amasonyeza Yesu Khristu monga Mfumu akuyendela mipingo 7 ya ku Asia Minor. Masomphenyawa amasonyeza kuti Khristu ankaona zinthu zeni-zeni zimene zinali kucitika m’mipingoyo. M’mipingo ina iye anali kuchula ngakhale maina a anthu. Mpingo uliwonse anali kuuyamikila pa zimene ukucita bwino kapena kupeleka malangizo oyenela. Kodi zimenezi zikutanthauza ciani? Pa kukwanilitsidwa kwa masomphenyawa, mipingo 7 ikuimila Akhristu odzozedwa kuyambila mu 1914 koma malangizo amene anapelekedwa ku mipingo imeneyi amagwila nchito ku mipingo yonse ya anthu a Mulungu masiku ano. Conco tikhoza kunena kuti Yehova akutsogolela anthu ake pogwilitsa nchito Mwana wake. Kodi tingalole bwanji kuti Yehova azititsogolela?
w01 1/15 20-21 ¶20
Yendelani Limodzi ndi Gulu la Yehova
Kuyendela limodzi ndi gulu la Yehova lopita patsogolo kumafuna kuti tizindikile udindo wopatsidwa ndi Mulungu wa Yesu Khristu monga “mutu wa Eklesia.” (Aefeso 5:22, 23) Mfundo inanso yofunika ndi ya pa Yesaya 55:4, pomwe timaŵelenga kuti: “Taonani, [ine Yehova] ndam’peleka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolela ndi wolamulila anthu.” Ndithudi Yesu akuidziŵa bwino nchito yotsogolela. Akudziŵanso nkhosa zake ndi zocita zawo. Kweni-kweni, atapenda mipingo isanu ndi iŵili ya ku Asiyamina, iye akunena kasanu konse kuti: “Ndidziŵa nchito zako.” (Chivumbulutso 2:2, 19; 3:1, 8, 15) Yesu amadziŵanso zosoŵa zathu, monga momwe Atate wake, Yehova, amacitila. Asanapeleke Pemphelo Lacitsanzo, Yesu anati: “Atate wanu adziŵa zomwe muzisoŵa, inu musanayambe kupempha iye.”—Mateyu 6:8-13.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
Ufumu wa Mulungu Udzawononga Adani Ake
Kulekanitsa nkhosa ndi Mbuzi. Adani a Ufumu wa Mulungu adzaona cocitika cina cimene cidzaonjezela mantha ao. Yesu anati: “Adzaona mwana wa munthu akubwela m’mitambo ndi mphamvu yaikulu ndiponso ulemenelo.” (Maliko 13:26) Zimenezi zidzaonetsa kuti Yesu wabwela kudzalekanitsa nkhosa ndi mbuzi. Mu ulosi wina wonena za masiku otsiliza, Yesu anafotokoza mwatsanetsane zimene zidzacitika panthawiyo. Mfundo zimenezo timazipeza m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi. (Ŵelengani Mateyu 25:31-33, 46.) Anthu amene amacilikiza Ufumu mokhulupilika adzaweluzidwa monga “nkhosa” ndipo ‘adzatukula mitu yao’ pozindikila kuti ‘cipulumutso cao cayandikila.’ (Luka 21:28) Koma aja amene amatsutsa Ufumu wa Mulungu, adzaweluzidwa monga “mbuzi” ndipo “adzadziguguda pacifuwa cifukwa ca cisoni” podziŵa kuti ‘adzaonongedwa kothelatu.’—Mat. 24:30; Chiv. 1:7.
w09 1/15 31 ¶1
Mfundo Zazikulu za M’buku la Chivumbulutso—Gawo 1
2:7—Kodi “paradaiso wa Mulungu” n’ciani? Popeza kuti mawu amenewa akuuza Akhristu odzozedwa, paradaiso wochulidwa palembali akutanthauza moyo wabwino wakumwamba. Akhristu odzozedwa okhulupilika adzapatsidwa mwayi wodya “za mu mtengo wa moyo.” Iwo adzalandila moyo wosafa.—1 Akor. 15:53.
NOVEMBER 25–DECEMBER 1
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 4-6
“Amuna Anayi Okwela pa Mahosi”
Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?
Kodi wokwela pa hosi yoyela n’ndani? Yankho ipezeka m’buku imodzi-modzi ya m’Baibo ya Chivumbulutso. M’caputa cina m’bukuli, iye amachedwa “Mawu a Mulungu.” (Chivumbulutso 19:11-13) Yesu Khristu ndiye amachedwa Mawu, cifukwa ni wokambilako Mulungu. (Yohane 1:1, 14) Amachedwanso kuti “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,” komanso kuti “Wokhulupilika ndi Woona.” (Chivumbulutso 19:16) N’zoonekelatu kuti monga mfumu yankhondo, iye ali na mphamvu zoculuka, koma saseŵenzetsa mphamvuzo molakwa kapena mosayenela. Koma pakubuka mafunso ena.
wp17.3 4 ¶5
Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?
Kodi ni liti pamene amuna amenewa anakwela pa mahosi na kuyamba kuthamanga? Onani kuti wokwela pa hosi yoyamba, Yesu, anayamba ulendo wake pamene anapatsidwa cisoti cacifumu. (Chivumbulutso 6:2) Kodi Yesu anaikidwa liti kukhala Mfumu kumwamba? Iye sanaikidwe pambuyo pobwelela kumwamba ataukitsidwa. Baibo imaonetsa kuti anafunika kuyembekezela. (Aheberi 10:12, 13) Yesu anafotokozela ophunzila ake mmene angadziŵile kuti nthawi ya kuyembekezela yasila, ndi kuti wayamba kulamulila kumwamba. Anakamba kuti kuciyambi kwa ulamulilo wake, zinthu padzikoli zidzaipila-ipila. Panali kudzakhala nkhondo, njala, ndi milili. (Mateyu 24:3, 7; Luka 21:10, 11) Nkhondo yoyamba ya dziko lonse itayamba mu 1914, umboni unaonekelatu wakuti mtundu wa anthu waloŵa m’nthawi yovuta imene Baibo imakamba kuti “masiku otsiliza.”—2 Timoteyo 3:1-5.
Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?
Wokwela pa hosi imeneyi akuimila nkhondo. Onani kuti sakucotsa mtendele m’maiko ocepa cabe, koma padziko lonse. Mu 1914, kwa nthawi yoyamba, padziko panabuka nkhondo imene inakhudza maiko onse. Pambuyo pake, panabukanso nkhondo yaciŵili ya dziko lonse imene inawononga koposa. Malipoti aonetsa kuti anthu opitilila 100 miliyoni afa pankhondo kucokela 1914. Kuwonjezela apo, anthu ena ambili-mbili anapwetekedwa maningi.
wp17.3 5 ¶4-5
odi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?
“Nditayang’ana, ndinaona hachi yakuda. Wokwelapo wake anali ndi sikelo m’dzanja lake. Kenako ndinamva mawu ngati ocokela pakati pa zamoyo zinayi zija. Mawuwo anali akuti: ‘Kilogalamu imodzi ya tiligu, mtengo wake ukhala dinali imodzi, ndipo makilogalamu atatu a balele, mtengo wake ukhala dinali imodzi. Koma musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo.’”—Chivumbulutso 6:5, 6.
Wokwela pa hosi imeneyi akuimila njala. Lembali likuonetsa kucepekela kwa cakudya cakuti kilogalamu imodzi ya tiligu ingagulidwe ndi dinali imodzi, imene inali malipilo a tsiku lathunthu m’zaka 100 zoyambilila. (Mateyu 20:2) Ndalama imodzi-modziyo ingagule makilogalamu atatu a balele, cakudya cimene anthu sanali kucikonda poyelekeza ndi tiligu. Kodi banja lalikulu lingadye masiku angati cakudya cimeneco? Anthu akucenjezedwa kuti asawononge ngakhale cakudya cimene anali kudya nthawi zonse, monga mafuta a maolivi ndi vinyo.
wp17.3 5 ¶8-10
Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?
Wokwela pa hosi yacinayi akuimila imfa imene ikucitika cifukwa ca milili ndi zinthu zina. Pambuyo pa 1914, cimfine ca ku Spain cinapha anthu mamiliyoni ambili. N’kutheka kuti anthu 500 miliyoni anadwalapo matendawa, pafupi-fupi munthu mmodzi pa atatu alionse panthawiyo.
Koma cimfine ca ku Spain cinali ciyambi cabe. Akatswili aonetsa kuti anthu ofika m’mahandiledi miliyoni anafa ndi nthomba m’zaka za m’ma 1900. Mpaka lelo, anthu mamiliyoni ambili amafa ndi matenda a AIDS, TB, na maleliya, ngakhale kuti a zacipatala ayesa-yesa kufufuza mankhwala.
Zoonadi, anthu ambili afa cifukwa ca nkhondo, njala, ndi milili. Manda akupitiliza kutenga anthu, ndipo siyapeleka ciyembekezo ciliconse.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
re 76-77 ¶8
Ulemelelo wa Mpando Wacifumu wa Yehova Wakumwamba
Yohane anali kudziŵa kuti ansembe ndi amene anali kuikidwa kuti azitumikila m’cihema cakale cija. Conco mwina anadabwa kuona zinthu zotsatila zimene anazifotokoza. Iye anati: “Kuzungulila mpando wacifumuwo, panalinso mipando yacifumu yokwanila 24. Pamipando yacifumuyo, ndinaona patakhala akulu 24 ovala malaya akunja oyela, ndi zisoti zacifumu zagolide pamitu pawo.” (Chivumbulutso 4:4) Inde, m’malo mwa ansembe, iye anaona akulu 24, atakhala pamipando yacifumu ndiponso atavala zisoti zacifumu ngati mafumu. Kodi akulu amenewa akuimila ndani? Iwo si enanso koma Akhristu odzozedwa a mumpingo wacikhristu, ataukitsidwa n’kupatsidwa udindo umene Yehova anawalonjeza kumwamba. Kodi tikudziŵa bwanji zimenezi?
re 80 ¶19
Ulemelelo wa Mpando Wacifumu wa Yehova Wakumwamba
Kodi zamoyo zimenezi zikuimila ciani? Masomphenya amene mneneli Ezekieli anaona akutithandiza kupeza yankho. Ezekieli anaona Yehova atakhala pampando wacifumu womwe unali pagaleta lakumwamba, ndipo pafupi ndi galetalo panali zamoyo zooneka mofanana ndi zamoyo zimene Yohane anaona. (Ezekieli 1:5-11, 22-28) Kenako, Ezekieli anaonanso galeta lokhala ndi mpando wacifumu lomwe lija limodzi ndi zamoyo zija. Koma pa nthawi ino, iye ananena kuti zamoyozo zinali akerubi. (Ezekieli 10:9-15) Conco, zamoyo zinayi zimene Yohane anaona ziyenela kuti zikuimila akerubi ambili-mbili a Mulungu. Ndipotu akerubi ndi zolengedwa za udindo waukulu m’gulu la Mulungu la zolengedwa zauzimu. Yohane ayenela kuti sanadabwe ataona akerubi ataima pafupi kwambili ndi Yehova. Izi zili conco cifukwa kale pamene Aisiraeli anali kulambila Mulungu kucihema, akerubi aŵili agolide anaikidwa pamwamba pa civundikilo ca likasa la pangano, lomwe linkaimila mpando wacifumu wa Yehova. Mawu a Yehova anamveka kucokela pakati pa akerubi aŵili amenewa popeleka malamulo ku mtunduwo.—Ekisodo 25:22; Salimo 80:1.
cf 36 ¶5-6
“Taona! Mkango wa Fuko la Yuda”
Mkango ni nyama yolimba mtima kwambili. Kodi munayamba mwaonapo maso ndi maso mkango waukulu waumuna? Ngati munauona, mwina mkangowo unali m’malo osungilako nyama zakuchile otetezedwa na mpanda. Komabe kuona mkango maso na maso, ngakhale uli mumpanda, n’kocititsa mantha. Mukamayang’anizana maso na maso na nyama yaikulu komanso yamphamvu imeneyi, simungaganize kuti mkangowo ungathaŵe ciliconse cifukwa ca mantha. Baibo imanena kuti ‘mkango ndi wamphamvu kwambili pa nyama zonse zakuchile ndiponso suopa ciliconse n’kubwelela m’mbuyo.’ (Miyambo 30:30) Khristu ndi wolimbanso mtima ngati mkango.
Tsopano tiyeni tikambilane njila zitatu zimene Yesu anasonyezela kulimba mtima ngati mkango. Tikambilana mmene anasonyezela kulimba mtima poteteza coonadi, potsatila cilungamo ndiponso pamene anali kutsutsidwa. Tionanso kuti tonsefe, kaya ndife olimba mtima mwacibadwa kapena ayi, tingathe kutsanzila Yesu posonyeza kulimba mtima.