UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khalani Monga Yosefe—Thaŵani Zaciwelewele
Yosefe anatipatsa citsanzo cabwino cimene tingatengele tikayesedwa kuti ticite zaciwelewele. Nthawi iliyonse pamene mkazi wa mbuye wake anamunyengelela kuti agone naye, iye anali kukana. (Gen. 39:7-10) Iye anali kuyankha kuti: “Ndingacitilenji coipa cacikulu conci n’kucimwila Mulungu?” Zimenezi zinaonetsa kuti anali ataganizilapo kale za mmene Yehova amaonela nkhani yokhala wokhulupilika m’cikwati. Ndiyeno pamene ciyeso cinakula, iye anathaŵa m’malo mozengeleza na kulola mkaziyo kumugonjetsa.—Gen. 39:12; 1 Akor. 6:18.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI THAWANI ZACIWELEWELE, PAMBUYO PAKE, YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi Jin anakumana na ciyeso canji?
Ni funso lofunika liti limene Jin anadzifunsa pamene Mee-Kyong anam’pempha kumuthandiza masamu kunyumba?
Kodi pempho la Mee-Kyong linam’khudza bwanji Jin?
Kodi Jin anapeza bwanji thandizo?
Kodi Jin anacita ciani kuti athawe ciwelewele?
Kodi mwaphunzila ciani m’vidiyo imeneyi?