Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
SEPTEMBER 7-13
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 23–24
“Usatsatile Khamu la Anthu”
Kodi Mudziŵa Bwino Zoona Zake?
7 Kodi mumakonda kutuma imelo kapena mameseji kwa anzanu? Ngati n’conco, ndiye kuti mukamvela nkhani inayake yocititsa cidwi imene yangofalitsidwa kumene, mwina mumalakalaka kukhala woyamba kuuzako anzanu nkhaniyo. Komabe, musanatume meseji kapena imelo, dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhani imene nifuna kutumayi ni ya zoona? Kodi nidziŵadi zoona pa nkhaniyi?’ Ngati mulibe umboni, simuyenela kuitumiza, cifukwa mosadziŵa, mungafalitse nkhani yabodza pakati pa abale. M’malomwake, muyenela kungoifafaniza.
8 Palinso vuto lina limene lingakhalepo ngati tili na cizoloŵezi cothamangila kutumila ena imelo kapena mameseji amene talandila. Ku maiko ena, cipembedzo ca Mboni za Yehova n’coletsedwa. M’maiko aconco, otsutsa angafalitse mwadala nkhani zabodza pofuna kutiyofyeza kapena kuticititsa kuyamba kukayikilana. Ganizilani zimene zinacitika m’dziko limene kale linali kuchedwa Soviet Union. Gulu la apolisi acisinsi, lochedwa KGB, linafalitsa nkhani yabodza yakuti abale ena oyang’anila pa nthambi anapandukila gulu la Yehova. Ambili anakhulupilila nkhaniyo cakuti anadzilekanitsa na gulu la Yehova. Zinali zomvetsa cisoni kwambili! Koma cokondweletsa n’cakuti ambili anabwelela. Ngakhale zinali conco, ena sanabwelele. Cikhulupililo cawo cinasweka ngati ngalawa. (1 Tim. 1:19) Kodi tingapewe bwanji vuto ngati limeneli? Musamafalitse nkhani zofooketsa kapena zopanda umboni. Musamangokhulupilila zilizonse zimene mwamva. Koma muziyesetsa kudziŵa zoona zeni-zeni pa nkhaniyo.
it-1 11 ¶3
Aroni
N’zocititsa cidwi kuti pa zophophonya zake zonse zitatu, zionetsa kuti Aroni si ndiye anali woyambitsa zolakwazo. M’malomwake, zioneka kuti iye analola mikhalidwe na cisonkhezelo ca ena kum’cititsa zinthu zosayenela. Pa colakwa cake coyamba, iye akanaseŵenzetsa lamulo lakuti: “Usatsatile khamu pocita zoipa.” (Eks. 23:2) Ngakhale n’conco, dzina lake m’Malemba imaseŵenzetsedwa m’njila yolemekezeka, ndipo Mwana wa Mulungu ali pano padziko, anacita zinthu molemekeza unsembe wa Aroni.—Sal. 115:10, 12; 118:3; 133:1, 2; 135:19; Mat. 5:17-19; 8:4.
it-1 343 ¶5
Khungu
Kusoŵa cilungamo poweluza milandu cifukwa ca katangale kunali kuimilidwa na khungu, ndipo m’cilamulo muli mfundo zambili zoletsa ciphuphu, mphatso, kapena tsankho, cifukwa zinthu zimenezi zingacitse khungu woweleza na kum’cititsa kupeleka ciweluzo cokondela. Cilamulo cinali na mfundo yakuti: “ciphuphu cimacititsa khungu anthu a maso akuthwa.” (Eks. 23:8) Mfundo ina inali yakuti: “ciphuphu cimacititsa khungu maso a anthu anzelu.” (Deut. 16:19) Cotelo kaya woweluza ni wacilungamo na wozindikila zinthu kwambili, mozindikila kapena mosazindikila iye angakhudzidwe na mphatso yocokela kwa munthu woimbidwa mlandu. Lamulo la Mulungu lionetsa kuti kuwonjezela pa mphatso, woweluza akanatha kuweluza mopanda cilungamo cifukwa ca mmene anali kuonela zinthu kapena mmene anali kumvelela, lamulolo linati: “Musamakondele munthu wosauka, ndiponso musamakondele munthu wolemela.” (Lev. 19:15) Conco, mmene iye anali kumvelela, kapena mmene khamu la anthu linali kuonela zinthu, sizinafunike kupangitsa woweluza kupeleka cigamulo copondeleza olemela, cabe cifukwa cakuti ni olemela.—Eks. 23:2, 3.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
“Musaiŵale Kuceleza Alendo”
4 Yehova anapempha Aisraeli kuti azikomela mtima alendo. (Ŵelengani Ekisodo 23:9.) Aisraeli anali kudziŵa “mmene zimakhalila ukakhala mlendo.” Ngakhale asanapite ku ukapolo, Aheberi anali kunyalanyazidwa ndi Aiguputo cifukwa ca kusiyana mtundu kapena kusankhana cipembedzo. (Gen. 43:32; 46:34; Eks. 1:11-14) Ngakhale kuti Aisraeli anali kuvutitsidwa pamene anali kudziko lacilendo, Yehova anawauza kuti aziona mlendo wokhala pakati pawo “ngati mbadwa.”—Lev. 19:33, 34.
it-2 393
Mikayeli
1. Kupatulapo Gabirieli, Mikayeli ndiye mngelo yekha amene amachulidwa ndi dzina m’Baibo, ndipo ndiye yekha amene amachulidwa kuti “mkulu wa angelo.” (Yuda 9) Dzinali limachulidwa koyamba m’caputa 10 m’buku la Danieli, pamene Mikayeli akufotokozedwa monga “mmodzi mwa akalonga aakulu”, iye anabwela kudzathandiza mngelo amene anatsekelezedwa na “kalonga wa ufumu wa Perisiya.” Mikayeli anachedwa “kalonga wa anthu [a Danieli],” “kalonga wamkulu amene waimilila kuti athandize anthu a mtundu [wa Danieli].” (Dan. 10:13, 20, 21; 12:1) Izi zitsimikizila kuti Mikayeli ndiye anali mngelo amene anatsogolela Aisiraeli m’cipululu. (Eks. 23:20, 21, 23; 32:34; 33:2) Zimenezi zikucilikizidwanso na mfundo ina yakuti “Mikayeli mkulu wa angelo anasemphana maganizo ndi Mdyelekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose.”—Yuda 9.
SEPTEMBER 14-20
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 25-26
“Cimene Cinali Cofunika Kwambili m’Cihema”
it-1 165
Likasa la Cipangano
Kapangidwe Kake. Cinthu coyamba cimene Yehova anapatsa Mose, pomuuza kuti amange cihema, inali pulani ya kapangidwe ka Likasa, cifukwa ndiye cinali cinthu cofunika kwambili m’cihema, komanso mu msasa wonse wa Aisiraeli. M’litali linali mikono iwili na hafu, m’lifupi mkono umodzi ndi hafu, mu msinkhu wake mkono umodzi ndi hafu (c. 111 × 67 × 67 cm; 44 × 26 × 26 in.). Likasalo linapangidwa na mtengo wa mthethe, ndipo linakutidwa na golide woyengedwa bwino mkati na kunja komwe. Komanso, analikongoletsa na “mkombelo wagolide” mozungulila kumwamba kwake. Mbali yaciŵili ya Likasa, civundikilo cake, cinali ca golide weni-weni, osati thabwa lokutidwa na golide. Pamwamba pa civundikiloco anaikapo akelubi aŵili agolide, aliyense anaikidwa kothela kwa civundikiloco moyang’ana mnzake, nkhope zawo zitawelama, atatambasula mapiko awo pamwamba pa Likasalo. (Eks. 25:10, 11, 17-22; 37:6-9) Civundikilo cimeneco, cinali kuchulidwanso kuti ‘mpando wa cifundo,’ kapena ‘civundikilo cophimba macimo.’—Eks. 25:17; Aheb. 9:5.
it-1 166 ¶2
Likasa la Cipangano
Mu Likasa anali kusungilamo zinthu zopatulika. Zinthu zimenezo zinali zikumbutso kapena umboni. Mwa zinthuzo, zofunika kwambili zinali miyala iŵili ya umboni, kapena kuti Malamulo Khumi. (Eks. 25:16) Pambuyo pake, anaikamonso ‘mtsuko wagolide wokhala ndi mana, ndi ndodo ya Aroni imene inaphuka ija.’ Koma zinadzacotsedwamo panthawi inayake kacisi wa Solomo asanamangidwe. (Aheb. 9:4; Eks. 16:32-34; Num. 17:10; 1 Maf. 8:9; 2 Mbiri 5:10) Mose atatsala pang’ono kumwalila, anapatsa Alevi ansembe “buku . la cilamulo” na malangizo akuti azilisungila ‘pambali pa likasa la pangano la Yehova Mulungu wawo [osati mkati mwake], kuti likhale mboni ya Mulungu yowatsutsa.’—Deut. 31:24-26.
it-1 166 ¶3
Likasa la Cipangano
Loimila kukhalapo kwa Mulungu. M’mbili yake yonse, Likasa linali kuimila kukhalapo kwa Mulungu. Yehova analonjeza kuti: “Ine ndidzaonekela kwa iwe pamenepo ndi kulankhula nawe kucokela pamwamba pa civundikilo, pakati pa akelubi awiliwo amene ali pamwamba pa likasa la umboni.” “Ndidzaonekela mu mtambo pamwamba pa civundikiloco.” (Eks. 25:22; Lev. 16:2) Samueli analemba kuti Yehova “akukhala pa akelubi” (1 Sam. 4:4); conco akelubi anali “cifanizilo ca galeta” la Yehova. (1 Mbiri 28:18) Mogwilizana na zimenezi, “nthawi zonse Mose akalowa m’cihema cokumanako kukalankhula ndi Mulungu, anali kumva mawu kucokela pamwamba pa likasa la umboni akulankhula naye. Mawuwo anali kucokela pacivundikilo cimene cinali pa Likasa la umboni, pakati pa akelubi aŵili. Mulungu anali kulankhula naye motelo.” (Num. 7:89) Patapita nthawi, nayenso Yoswa na mkulu wa ansembe “Pinihasi anali kufunsila kwa Yehova pa tsogolo pa Likasa. (Yos. 7:6-10; Ower. 20:27, 28) Komabe, ni mkulu wa ansembe yekha amene anali kuloŵa m’malo Oyela Koposa na kuona Likasa, tsiku limodzi pa caka, osati kukakamba na Yehova, koma kukacita mwambo Wophimba Macimo Patsikulo.—Lev. 16:2, 3, 13, 15, 17; Aheb. 9:7.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 432 ¶1
Mkelubi
Cihema cimene cinamangidwa m’cipululu cinali na zifanizilo za akelubi. Mwacitsanzo, pa civundikilo ca Likasa, panali akelubi aŵili a golide, wina mapeto a uku, winanso mapeto a aku. Anali ogwada moyang’anana, atawelamila civundikiloco monga akulambila. Aliyense anali na mapiko aŵili atawatambasula m’mwamba kuphimba civundikiloco kukhala ngati kuti akuciteteza. (Eks. 25:10-21; 37:7-9) Kuwonjezela apo, nsalu zamkati zophimba cihemaco, na nsalu yolekanitsa malo Oyela na Malo Oyela Koposa anajambulapo zifanizilo za akelubi.—Eks. 26:1, 31; 36:8, 35.
it-2 936
Mkate Wacionetselo
Mikate 12 inali kuikidwa pa tebulo m’malo Oyela m’cihema kapena m’kacisi, ndipo anali kuikapo yatsopano pa Sabata lililonse. (Eks. 35:13; 39:36; 1 Maf. 7:48; 2 Mbiri 13:11; Neh. 10:32, 33) Mawu a Ciheberi akuti mkate waciwonetselo amatanthauza mkate woonetsa pa nkhope. Liwu lakuti nkhope nthawi zina limatanthauza “pamaso.” (2 Maf. 13:23) Conco, mkate wacionetselo unali kukhala pamaso pa Yehova nthawi zonse monga copeleka kwa iye. (Eks. 25:30) Mkate wacionetselo umachulidwanso kuti “mkate wosanjikiza” (2 Mbiri 2:4), “mitanda ya mkate woonetsa” (Maliko 2:26), komanso “mitanda ya mkate” (Aheb. 9:2).
SEPTEMBER 21-27
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EKSODO 27-28
“Kodi Tingaphunzile Ciani pa Zovala za Ansembe?”
it-2 1143
Tumimu na Urimu
Akatswili ambili a Baibo amakhulupilila kuti Urimu na Tumimu zinali zinthu za maele. Zimachedwa “maele opatulika” pa Ekisodo 28:30 m’Baibo imene James Moffatt anamasulila. Ena amaganiza kuti Urimu na Tumimu tunali tuzinthu tutatu, koyamba kanali kolembedwa mawu akuti “inde,” kena mawu akuti “ayi,” ndiponso kena kanali kosalembedwa ciliconse. Ndiye anali kutuponya pansi kuti apeze yankho pa funso limene lafunsidwa. Koma ngati maelewo aonetsa kaja kosalembedwa kalikonse ndiye kuti palibe yankho. Ena amaganiza kuti mwina tunali tumiyala tuŵili twafulati, koyela kumbali ina ndiponso kakuda kumbali inayo. Akatuponya pansi tumiyalato, tonse tuŵili tukaonetsa mbali yoyela, yankho inali “inde.” Tukaonetsa mbali yakuda yankho inali “ayi.” Ndipo tukaonetsa mbali yakuda na mbali yoyela ndiye kuti palibe yankho. Pa nthawi ina, pamene Sauli anafunsila kupitila mwa wansembe kuti apitilize kumenyana na Afilisiti kapena ayi, sanalandile yankho iliyonse. Poganiza kuti mmodzi mwa asilikali ake acimwa, anacondelela kuti: “Mulungu wa Isiraeli inu, tiyankheni kudzela mwa Tumimu!” Sauli na Yonatani anapatulidwa pakati pa anthu amene analipo, pambuyo pake, anacita maele kuti asankhepo mmodzi. M’nkhaniyi mawu akuti “tiyankheni kudzela mwa Tumimu,” amveka monga kuti panalibe kugwilizana na kucita maele, komabe angaonetsenso kuti panaliko kugwilizana kwinawake pakati mbali ziŵili zimenezi.—1 Sam. 14:36-42.
it-1 849 ¶3
Mphumi
Mkulu wa Ansembe wa Aisiraeli. Mu Isiraeli ‘nduwila’ ya mkulu wa ansembe, imene inali kukhala pamphumi pake inali na kacitsulo kaphanthiphanthi kagolide, “cizindikilo copatulika ca kudzipeleka.” Pa kacitsuloko panali mawu ‘olemba mocita kugoba,’ akuti “Ciyelo n’ca Yehova.” (Eks. 28:36-38; 39:30) Monga woimila wamkulu wa Aisireali pankhani yolambila Yehova, panali poyenela kuti mkulu wa ansembe azisunga ciyelo pa utumiki wake, ndipo mawu amenewo anali monga cikumbutso kwa Aisiraeli onse kuti afunika kusunga ciyelo potumikila Yehova nthawi zonse. Nduwila inacitilanso mthunzi Mkulu wa Ansembe Yesu Khristu, komanso kupatulidwa kwake na Yehova kuti atumikile monga wansembe wosungitsa ciyelo ca Mulungu.—Aheb. 7:26.
w08 8/15 15 ¶17
Lemekezani Yehova mwa Kusonyeza Ulemu
17 Tifunikila kuonetsa ulemu wapadela polambila Yehova. Lemba la Mlaliki 5:1 limati: “Samala mayendedwe ako ukapita kunyumba ya Mulungu woona.” Mose na Yoswa analamulidwa kuvula nsapato zawo pamalo opatulika. (Eks. 3:5; Yos. 5:15) Iwo amafunika kucita zimenezi poonetsa ulemu. Ansembe aciisiraeli analamulidwa kuvala zovala za miyendo kuti ‘abise malisece.’ (Eks. 28:42, 43) Zimenezi zinathandiza kuti azivala modzilemekeza akamatumikila pa guwa la nsembe. Aliyense m’banja la wansembe amafunikila kutsatila malamulo a Mulungu okhudza kudzilemekeza.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w12 8/1 26 ¶1-3
Kodi Mudziŵa?
Kodi miyala yamtengo wapatali imene inali kuikidwa pacovala pacifuŵa ca mkulu wa ansembe ku Isiraeli anali kuitenga kuti?
Aisiraeli ali m’cipululu atacoka ku Iguputo, Mulungu anawalamula kuti apange covala pacifuŵa ca mkulu wa ansembe. (Ekisodo 28:15-21) Covala pacifuŵaco cinali na miyala ya rube, topazi, emarodi, nofeki, safiro, yasipi, lesemu, sibu, ametusito, kulusitalo, onekisi ndi yade. Kodi zinali zotheka kuti Aisiraeli apeze miyala yamtengo wapataliyi?
Kale anthu anali kucita cidwi na miyala yamtengo wapatali ndipo anali kuigwilitsa nchito pa malonda. Mwacitsanzo, kale anthu a ku Iguputo anali kupeza miyala yamtengo wapatali kucokela kumadela akutali monga kumene masiku ano kumachedwa ku Iran, Afghanistan, ndiponso ku India. M’dziko la Iguputo munali kupezekanso miyala yosiyana-siyana yamtengo wapatali. Mafumu a ku Iguputo anali kuyang’anila miyala yonse imene inali kupezeka m’zigawo zonse zimene anali kulamulila. Yobu anafotokoza zinthu zosonyeza kuti anthu a m’nthawi yake anali kukumba migodi na ngalande pofufuza miyala yamtengo wapatali. Panali miyala yosiyana-siyana imene inali kukumbidwa, koma Yobu anangochula miyala ya safiro ndi topazi.—Yobu 28:1-11, 19.
Nkhani imene ili m’buku la Ekisodo imanena kuti Aisiraeli “anatenga zinthu zambili za Aiguputo” pamene anali kucoka m’dzikolo. (Ekisodo 12:35, 36) Conco n’kutheka kuti miyala imene Aisiraeli anaika pacovala pacifuwa ca mkulu wa ansembe anaitenga ku Iguputo.
it-1 1130 ¶2
Ciyelo
Ziŵeto na Zokolola. Ziŵeto zamphongo zoyamba kubadwa monga, ng’ombe, nkhosa, na mbuzi, zinali zopatulika kwa Yehova, ndipo sanali kufunika kuziwombola. Zinali kupelekedwa nsembe, ndipo gawo lina linali kupatsidwa kwa ansembe. (Num. 18:17-19) Zipatso zoyamba kuca komanso cakhumi zinali zopatulika, cifukwa zonse zinali nsembe na mphatso zogwilitsidwa nchito pa utumiki wa pa cihema. (Eks. 28:38) Zinthu zonse zopatulidwa kwa Yehova, sanali kuziona mopepuka, kapena kuziseŵenzetsa pa nchito wamba, kapena mosazilemekeza. Citsanzo ni lamulo lokhudza cakhumi. Ngati munthu wapatula pambali cakhumi kuti akacipeleke, tinene kuti wapatula tiligu, ndiyeno iye kapena munthu wina wa m’banja lake mosadziŵa watapapo pa tiliguyo kuti akaseŵenzetse, mwina kukaphika, munthuyo anali kupatsidwa mlandu wophwanya lamulo la Mulungu lolemekeza zinthu zopatulika. Malinga na Cilamulo, munthuyo anafunikila kukapeleka malipilo ku cihema okwana 20 pesenti ya zinthuzo. Kuwonjezela apo, anafunikilanso kupeleka nkhosa yamphongo yopanda cilema monga nsembe. Mwa ici, anthu anali kulemekeza kwambili zinthu zopatulika za Yehova.—Lev. 5:14-16
SEPTEMBER 28–OCTOBER 4
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EKSODO 29-30
Kupatsa Yehova Copeleka
it-2 764-765
Kuŵelenga Anthu
Pa Phili la Sinayi. Kuŵelenga anthu koyamba kumene Yehova analamula kunacitika pamene Aisiraeli anamanga msasa pa phili la Sinayi. Kunacitika m’mwezi waciŵili m’caka caciŵili ca ulendo wawo wocokela ku ukapolo ku Iguputo. Pofuna kuthandiza Mose pa nchitoyi, panasankhidwa atsogoleli ocokela m’fuko lililonse kuti aliyense ayang’anile nchito yoŵelenga anthu a fuko lake. Amuna onse oyambila zaka 20 kukwela m’mwamba, oyenelela kupita kunkhondo, anaŵelengedwa. Kuwonjezela apo, cilamulo cinakamba kuti munthu woŵelengedwa aliyense anafunikila kupeleka hafu ya sekeli ($1.10) yocilikiza utumiki wa pa cihema. (Eks. 30:11-16; Num. 1:1-16, 18, 19) Onse oŵelengedwa anakwana 603,550, kupatulapo Alevi, amene analibe coloŵa ca malo. Iwo sanali kupelekako msonkho wa pacihema, ndipo sanali kukhala asilikali.—Num. 1:44-47; 2:32, 33; 18:20, 24.
it-1 502
Copeleka
Panalinso zopeleka zina zofunika malinga na Cilamulo. Pamene Mose anaŵelenga Aisiraeli, mwamuna aliyense wa zaka 20 kukwela m’mwamba, anafunika kupeleka dipo la moyo wake, “hafu ya sekeli [mwina $1.10] yolingana ndi sekeli la kumalo oyela.” Cinali ‘copeleka kwa Yehova’ kuti aphimbe macimo ya miyoyo yawo ndiponso kuti “cikagwilitsidwe nchito pa utumiki wa pacihema cokumanako.” (Eks. 30:11-16) Malinga na katswili wolemba mbili ya Ayuda dzina lake Josephus (The Jewish War, VII, 218 [vi, 6]), “msonkho wopatulika” umenewu anali kuupeleka pa caka.—2 Mbiri 24:6-10; Mat. 17:24.
w11 11/1 12 ¶1-2
Kodi Mudziŵa?
Kodi ndalama zoyendetsela nchito pakacisi wa Yehova ku Yerusalemu zinali kucokela kuti?
Ndalama zoyendetsela nchito za pakacisi zinali kucokela ku misonkho imene anthu anali kupeleka, maka-maka msonkho wa cakhumi. Koma panalinso misonkho ina imene anthu anali kupeleka. Mwacitsanzo, pa nthawi imene anali kumanga cihema, Yehova anauza Mose kuti Mwiisiraeli aliyense amene anaŵelengedwa, apeleke hafu ya sekeli lasiliva ngati “copeleka kwa Yehova.”—Ekisodo 30:12-16.
Zikuoneka kuti Myuda aliyense anali kufunika kupeleka ndalama za msonkho wapakacisi umenewu caka ciliconse. Msonkho umenewu ndi umene Yesu anauza Petulo kuti apeleke pogwilitsa nchito ndalama imene anaipeza m’kamwa mwa nsomba.—Mateyu 17:24-27.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 1029 ¶4
Dzanja
Kuika Manja. Anthu anali kuika manja pa munthu, kapena pa cinthu, pa zifukwa zosiyana-siyana. Koma kacitidwe kameneka kanali umboni woonetsa kuti munthuyo kapena cinthuco n’covomelezeka. Pa mwambo wolonga ansembe, Aroni na ana ake aamuna anaika manja awo pa mutu wa ng’ombe yamphongo, komanso pa nkhosa ziŵili zamphongo zokapelekedwa nsembe. Mwa ici, anavomeleza kuti ziŵeto zimenezo zinali kupelekedwa nsembe m’malo mwa iwo cifukwa anali kudzakhala ansembe a Yehova Mulungu. (Eks. 29:10, 15, 19; Lev. 8: 14, 18, 22) Posankha Yoswa monga womuloŵa mmalo molamulidwa na Mulungu, Mose anaika manja ake pa Yoswa, amene “anali wodzazidwa ndi mzimu wa nzelu,” ndiponso anali wokonzeka kuwatsogolela bwino Aisiraeli. (Deut. 34:9) Manja anali kuikidwa pa anthu powatsimikizila kuti alandila madalitso. (Gen. 48:14; Maliko 10:16) Yesu Khristu anacilitsa anthu ena mwa kuwakhudza kapena kuwaika manja pamutu. (Mat. 8:3; Maliko 6:5; Luka 13:13) M’zocitika zina, anthu anali kulandila mphatso ya mzimu woyela mwa kuikidwa manja na atumwi.—Mac. 8:14-20; 19:6.
it-1 114 ¶1
Kudzozedwa, Kudzoza
M’cilamulo cimene Yehova anapatsa Mose, anamuuza mopangila mafuta odzozela. Mafutawo anali na msakanizo wapadela wa zinthu izi, “mule, sinamoni wonunkhila bwino, kalamasi wonunkhila, kasiya, komanso mafuta a maolivi. (Eks. 30:22-25) Unali mlandu waukulu ngati munthu wagwilitsila nchito zimenezi kupangila mafuta kuti awaseŵenzetse pa colinga cosaloleka. (Eks. 30:31-33) Izi zinali kuonetsa kufunika na kupatulika kwa amene asankhidwa kucita utumikiwu mwa kuwadzoza na mafuta opatulika.