LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr20 August
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
  • Tumitu
  • AUGUST 3-9
  • AUGUST 10-16
  • AUGUST 17-23
  • AUGUST 24-30
  • AUGUST 31–SEPTEMBER 6
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
mwbr20 August

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

AUGUST 3-9

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 13-14

“Cilimikani ndi Kuona Cipulumutso ca Yehova”

w13 2/1 4

Mose Anali Munthu Wacikhulupililo Colimba

N’kutheka kuti Mose sanali kudziŵa kuti Mulungu alekanitsa madzi a Nyanja Yofiila, kuti Aisiraeli awoloke pothaŵa adani awo. Komabe, iye anali na cikhulupililo conse kuti Mulungu acita cinacake kuti ateteze anthu ake. Mose anafuna kuti Aisiraeli anzake akhalenso na cikhulupililo cimeneci. Baibo imati: “Pamenepo Mose anauza anthuwo kuti: ‘Musacite mantha. Cilimikani ndi kuona cipulumutso ca Yehova cimene akucitileni lelo.’” (Ekisodo 14:13) Kodi Mose anathandizadi Aisiraeli anzakewo kukhala na cikhulupililo colimba? Inde, cifukwa Baibo limanena za Aisiraeli onse osati Mose yekha kuti: “Mwa cikhulupililo, anthu a Mulunguwo anawoloka Nyanja Yofiila ngati kuti akudutsa pamtunda pouma.” (Aheberi 11:29) Conco cikhulupililo cimene Mose anali naco sicinathandize iye yekha koma cinathandizanso Aisiraeli anzake.

w18.09 26 ¶13

Wamphamvuzonse Koma Woganizila Ena

13Ŵelengani Ekisodo 14:​19-​22. Yelekezelani kuti muli m’khamu la Aisiraeli. Asilikali a Farao akubwela ku mbali imodzi, ndipo ku mbali ina kuli Nyanja Yofiila. Ndiyeno Mulungu akucitapo kanthu kuti akupulumutseni. Akucititsa mtambo woima njo ngati cipilala kucoka kutsogolo kwanu n’kukaima kumbuyo kwanu, kuchinga Aiguputo na kuwacititsa kukhala mu mdima. Koma mukuona kuti khamu lonse la Aisiraeli likuunikilidwa na kuwala kwa mtambowo. Kenako mukuona Mose akutambasula dzanja lake kulata panyanja, ndipo cimphepo camphamvu ca kum’maŵa cikugaŵa nyanjayo n’kupanga cinjila cacikulu. Tsopano imwe, abululu anu, ziŵeto zanu, ndi anthu ena mukuyamba kuyenda pansi pakati pa nyanjayo. Ndipo mukudabwa kuona kuti pansipo palibe matika kapena cinyontho. M’polimba komanso pouma bwino, cakuti mukwanitsa kuyenda mosavutikila. Conco, aliyense, ngakhale okalamba akuyenda bwino-bwino mpaka kukafika ku tsidya lina la nyanjayo.

w09 3/15 7¶2-3

Musaiŵale Yehova

Pamene Aiguputo amavutika kuyenda na magaleta awo, Aisiraeli onse anafika ku tsidya lina, kum’mawa kwa nyanjayo. Tsopano Mose anatambasulila dzanja lake ku Nyanja Yofiila. Atacita zimenezi, Yehova anagwetsa makoma aŵili a madzi aja. Ndipo madzi ambili anacititsa Farao ndi ankhondo ake kumila. Palibe mdani ngakhale mmodzi amene anapulumuka. Ndipo Aisiraeli anamasuka.​—Eks. 14:26-28; Sal. 136:13-15.

Mbili ya zimene zinacitikazi inacititsa mantha mitundu yapafupi kwa nthawi yaitali. (Eks. 15:​14-​16) Patapita zaka 40, Rahabi wa ku Yeriko, anauza amuna aŵili Aciisiraeli kuti: “Ife tagwidwa ndi mantha cifukwa ca inu . . . Tinamva za mmene Yehova anaphwetsela madzi a Nyanja Yofiila pamaso panu, mutatuluka m’dziko la Iguputo.” (Yos. 2:9, 10) Inde, ngakhale anthu osalambila Mulungu woona sanaiŵale mmene Yehova anapulumutsila anthu ake. Conco n’zoonekelatu kuti Aisiraeli anali na zifukwa zambili zokumbukilila Yehova.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-1 1117

Msewu Waukulu, Njila

Kuyambila nthawi zakale misewu ikulu-ikulu na njila, kuphatikizapo misewu ingapo ya amalonda, inali kugwilizanitsa mizinda na maufumu m’dziko la Palesitina. (Num. 20:17-19; 21:21, 22; 22:5, 21-23; Yos. 2:22; Ower. 21:19; 1 Sam. 6:9, 12; 13:17, 18.) Msewu umene unali kuonedwa kukhala wofunika kwambili, unali wocokela ku Iguputo kupita ku mizinda ya Afilisiti ya Gaza na Asikeloni, ndipo pambuyo pake unali kukhotela kumpoto cakum’mawa kuloŵela ku Megido. Unali kukafika ku Hazori, kumpoto kwa Nyanja ya Galileya, na kupitilila mpaka ku Damasiko. Msewu umenewu wopitila m’cigawo ca Filisitiya, ndiwo unali njila yaifupi kwambili yocokela ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa. Koma mokoma mtima Yehova anatsogolela Aisiraeli kutuluka mu Iguputo mwa kuseŵenzetsa njila ina, kuopela kuti angataye mtima cifukwa ca mantha akaukilidwa na Afilisiti.​—Eks. 13:17.

it-1 782 ¶2-3

Ekisodo

Kodi Nyanja Yofiila inagawidwa pa malo ati kuti Aisiraeli awoloke?

Tiyenela kudziŵa kuti Aisiraeli ataima kaciŵili mkati mwa ulendo wawo, ku Etamu “m’malile a cipululu,” Mulungu analamula Mose kuti “abwelele ndi kumanga msasa pafupi ndi Pihahiroti . . . pafupi ndi nyanja.” Kucita zimenezi kunapangitsa Farao kukhulupilila kuti Aisiraeli “asokonezeka ndipo akungoyendayenda.” (Eks. 13:20; 14:1-3) Akatswili amene amakhulupilila kuti Aisiraeli anadutsa njila yochedwa el Haj, amakamba kuti mawu aciheberi amene anamasulidwa kuti “abwelele” ni otsindika, ndipo satanthauza cabe “kupatuka” kapena “kupitila njila ina,” koma amatanthauza kubwelela ndithu kapena kukoneka kwambili monga ufuna kubwelela. Iwo amakamba kuti Aisiraeli atafika pa malo ena ake kumpoto kwa nyanja yofiila, anabwelela n’kuyamba kuyenda m’dela la kum’mawa kwa mapili ochedwa Jebel ʽAtaqah, amene ali kumadzulo kwa Nyanja Yofiila. Popeza Aisiraeli anali cigulu, sakanakwanitsa kuthawa pamalo amenewo mwamsanga ngati kuti owathamangitsa anali kucokela kumpoto, cifukwa anali atatsekelezedwa na nyanja mbali imodzi kwinaku mapili.

Zimene Ayuda a m’nthawi ya atumwi anali kukhulupilila n’zogwilizana na kafotokozedwe kameneka ka ulendo wa Aisiraeli. Kuposa pamenepa, cofunika kwambili n’cakuti kafotokozedwe kameneka kamagwilizana na mmene nkhaniyi imafotokozeledwela m’Baibo. Koma zimene akatswili ambili amakamba pankhaniyi sizigwilizana na zimene Baibo imakamba. (Eks. 14:9-16) Komanso zioneka kuti Aisiraeli sanawolokele pafupi kwambili na mapeto a kumpoto a nyanja yofiila, cifukwa akanatelo, cikanakhala capafupi kwa asilikali a Farao kungozungulila nyanjayo n’kuwapeza kutsidya lina.​—Eks. 14:22, 23.

AUGUST 10-16

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 15-16

“Tamandani Yehova mwa Kuimba Nyimbo”

w95 10/15 11 ¶11

N’cifukwa Ninji Tiyenela Kuwopa Mulungu Woona Tsopano?

1 Kuwononga kwa Yehova magulu ankhondo Aciigupto kunam’kweza pamaso pa alambili ake ndipo kunacititsa dzina lake kudziŵika konse-konse. (Yoswa 2:9, 10; 4:23, 24) Inde, dzina lake linakwezedwa pamwamba pa milungu yopanda mphamvu, yonyenga ya Iguputo, imene inalephela kupulumutsa alambili ake. Cidalilo cawo mwa milungu yawo na mwa munthu wokhoza kufa ndiponso mwa mphamvu ya zankhondo cinawagwilitsa mwala kwambili. (Salimo 146:3) N’cifukwa cake Aisiraeli anasonkhezeleka kuimba zitamando zimene zinaonetsa mantha abwino kwa Mulungu wamoyo, amene amawombola anthu ake mwamphamvu!

w95 10/15 11-​12 ¶15-​16

N’cifukwa Ninji Tiyenela Kuwopa Mulungu Woona Tsopano?

15Tikanaima na Mose tili otetezeka, mosakayikila tikanasonkhezeleka kuimba kuti: “Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova? Ndinu woyela kopambana, ndani angafanane ndi inu? Ndinu woyenela kuopedwa ndi kukuimbilani nyimbo zotamanda. Inu ndinu wocita zodabwitsa.” (Ekisodo 15:11) Mawu otelo abwelezedwa m’zaka mazana ambili kuyambila pamenepo. M’buku lomaliza la Baibo, mtumwi Yohane akufotokoza kagulu ka atumiki okhulupilika odzozedwa a Mulungu kuti: “Iwo akuimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, yakuti: “Nchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse. Njila zanu ndi zolungama ndi zoona, inu Mfumu yamuyaya. Kodi ndani sadzakuopani, inu Yehova? Ndani sadzalemekeza dzina lanu? Pakuti inu nokha ndinu wokhulupilika.”​—Chivumbulutso 15:2-4.

16Motelo lelolinonso pali alambili omasulidwa amene amayamikila nchito za Mulungu na malamulo ake. Anthu ocokela m’mitundu yonse amasulidwa mwauzimu, apatutsidwa ku dzikoli loipitsidwa cifukwa amadziŵa malamulo olungama a Mulungu na kuwacita. Caka ciliconse, masauzande ambili a anthu amathaŵa dziko loipali kukakhala na gulu loyela, lolungama la alambili a Yehova. Posacedwapa, pambuyo pa kupelekedwa kwa ziweluzo za Mulungu zoopsa pa cipembedzo conyenga na dongosolo loipali, iwo adzakhala na moyo kosatha m’dziko latsopano lolungama.

it-2 454 ¶1

Nyimbo

Nthawi zambili, anthu ku Isiraeli anali kuimba nyimbo molandizana mawu. Panali kukhala magulu aŵili ndipo gulu lina linali kuimba mzele wina, lina linali kutsilizitsa mzele wina. Zioneka kuti kuimba kumeneko m’Malemba kumachedwa ‘kuthilila mang’ombe.’ (Eks. 15:21; 1 Sam. 18:6, 7) Kuimba kumeneko kumaonekala na mmene masalimo analembedwela, monga Salimo 136. Magulu aŵili akuluakulu a oimba zitamando m’nthawi ya Nehemiya, anali kuimba mwa njila imeneyi pamene anali kucita cikondwelelo ca kumangidwa kwa mpanda wa Yerusalemu.​—Neh. 12:31, 38, 40-42.

it-2 698

Mneneli Wamkazi

Miriamu ni mkazi woyamba kusankhidwa monga mneneli wamkazi m’Baibo. Mwacionekele Mulungu anali kupeleka mauthenga kupitila mwa iye, mwina kupitila m’nyimbo zouzilidwa. (Eks. 15:​20, 21) Conco, timaŵelenga za iye na Aroni kuti anauza Mose kuti: “Kodi [Yehova] sanalankhulenso kudzela kwa ife?” (Num. 12:2) Yehova iye yekha, kupitila mwa Mika, anakamba kuti anatumiza “Mose, Aroni ndi Miriamu” kuti atsogolele Aisiraeli powatulutsa mdziko la Iguputo. (Mika 6:4) Ngakhale kuti Miriamu anali na mwayi woseŵenzetsedwa na Mulungu monga cipangizo, ubwenzi wake na Mulungu sunali wolimba kwambili kuyelekeza na m’bale wake Mose. Pamene analephela kusunga malo ake oyenela, analangidwa na Mulungu.​—Num. 12:1-15.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w11 9/1 14

Kodi Mudziŵa?

Pamene Aisiraeli anali m’cipululu, kodi cingakhale cifukwa citi cimene Yehova anasankhila kuwapatsa zinzili?

Pa nthawi imene Aisiraeli anali pa ulendo wawo wocokela ku Iguputo, Mulungu anawapatsa nyama yambili kaŵili konse ndipo nyama yake inali zinzili.​—Ekisodo 16:13; Numeri 11:31.

Zinzili ni mbalame zing’onozing’ono zotalika pafupi-fupi masentimita 18 kucoka kumutu kufika kumcila ndipo zimalemela pafupi-fupi magalamu 100. Zinzili zimapezeka m’madela ambili a kumadzulo kwa Asia ndi Ulaya maka-maka ikakhala nyengo imene zimaswana. Zinzili zili m’gulu la mbalame zimene zimakonda kusamuka-samuka, ndipo nyengo yozizila, mbalamezi zimasamukila kumpoto kwa Africa na ku Arabia. Posamuka, zimakhala cigulu ndipo zimauluka kupitila cakum’mawa m’mbali mwa nyanja ya Mediterranean ndipo zimapitilanso m’dela la Sinai.

Malinga na zimene buku lina limanena, zinzili “zimauluka bwino komanso mwamsanga ndipo mphepo ikakhala kuti ikuyenda bwino, zimauluka mosavuta. Koma mphepo ikayamba kulowela mbali ina, kapena zinzilizi zikatopa na kuuluka, zonse zimatela pansi ndipo zimangokhala osayenda.” (The New Westminster Dictionary of the Bible) Zikatele, ulendo wawo umaima cifukwa zimafunika kupuma kwa tsiku lonse kapena masiku aŵili. Pa nthawi imeneyi anthu angathe kuzigwila mosavuta. M’zaka zoyambilila za m’ma 1900, caka ciliconse dziko la Egypt linali kugulitsa ku maiko ena zinzili zokwana 3 miliyoni zoti anthu akadye.

Maulendo onse aŵili amene Aisiraeli anadya zinzili, inali nyengo yacisanu itangotha kumene. Ngakhale kuti nthawi zambili nthawi imeneyi ni imene zinzili zinali kupezeka m’dela la Sinai, Yehova na amene “anautsa mphepo yamkokomo” imene inacititsa kuti zinzili ziulukile kumsasa wa Aisiraeli.​—Numeri 11:31.

w06 1/15 31

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Patapita nthawi yocepa cabe atalanditsidwa ku Aigupto, Aisiraeli anayamba kung’ung’udza pankhani ya cakudya. Motelo Yehova anawapatsa mana. (Ekisodo 12:17, 18; 16:1-5) Panthawiyi, Mose analangiza Aroni kuti: “Tenga mtsuko ndi kuthilamo mana muyezo umodzi wa omeli ndi kuuika pamaso pa Yehova kuti asungidwe m’mibadwo yanu yonse.” Nkhaniyo imati: “Monga momwe Yehova analamulila Mose, Aroni anaikadi mtsukowo patsogolo pa Umboni [kapena kuti mosungila zolembedwa zofunika] kuti manawo asungidwe.” (Ekisodo 16:33, 34) N’zosakayikitsa kuti panthawiyi Aroni anatenga mana n’kuuika m’mbiya inayake, koma sanauike patsogolo pa Mboni cifukwa anafunika kuyembekeza coyamba kuti Mose apange Likasa na kuikamo miyala yosema ija.

AUGUST 17-23

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 17-18

“Amuna Odzicepetsa Amaphunzitsa Ena Nchito na Kuwagaŵila Maudindo”

w13 2/1 6

Mose Anali Munthu Wacikondi

Mose anali kukondanso Aisiraeli anzake. Aisiraeli anali kudziŵa kuti Yehova anali kugwilitsa nchito Mose powatsogolela, conco iwo anali kupita kwa Mose akakhala na mavuto. Baibo imati: “Anthu anali kubwela ndi kuimilila pamaso pa Mose kuyambila m’mawa mpaka madzulo.” (Ekisodo 18:13-16) Mose ayenela kuti anali kutopa kwambili kumvetsela madandaulo a anthu amenewa. Komabe, iye anali kuwathandiza mosanyinyilika cifukwa cowakonda.

w03 11/1 6 ¶1

Kukhulupilila Ena N’kofunika Kwambili Kuti Munthu Akhale Wosangalala

Amuna ameneŵa anali ataonetsa makhalidwe ena ake auzimu asanaikidwe kukhala pa maudindo amene anthu anafunika kuwakhulupilila. Anali atasonyeza kale umboni wakuti anali kuopa Mulungu, anali kulemekeza kwambili Mlengi ndipo anali kuopa kumukhumudwitsa. Aliyense anatha kuona kuti amuna amenewa anacita zonse zimene akanatha polimbikitsa miyezo ya Mulungu. Anali kudana na phindu lacinyengo, zimene zinaonetsa kuti anali otsatila kwambili makhalidwe abwino, zimene zikanawathandiza kupewa kugwilitsa nchito udindo wawo molakwika. Sakanawagwilitsa fuwa la moto anthu amene anali kuwakhulupilila n’colinga coti ziŵakomele iwo kapena acibale na mabwenzi awo.

w02 5/15 25 ¶5

Kuwongoka Mtima Kumatsogolela Olungama

Mose analinso wodzicepetsa. Pamene anayamba kutopa posamala mavuto a anthu ena, apongozi ake, a Yetero, anamuuza mfundo yothandiza yakuti agaŵe maudindo ena kwa amuna ena oyenelela. Mose pozindikila kuti panali zinthu zina zimene sakanatha kucita, anavomela mwanzelu mfundo imeneyo. (Ekisodo 18:17-26; Numeri 12:3) Munthu wodzicepetsa saumila kugaŵila ena maudindo ndiponso saopa kuti ulamulilo wake ucepa cifukwa cogaŵa maudindo kwa amuna ena oyenelela. (Numeri 11:16, 17, 26-29) M’malo mwake, iye amawathandiza na mtima wonse kuti apite patsogolo mwauzimu. (1 Timoteyo 4:15) Kodi ifenso sitiyenela kucita zimenezo?

w16.09 6 ¶14

“Manja Anu Asakhale Olefuka”

14Aroni na Hura anathandiza Mose mwa kucilikiza manja ake panthawi ya nkhondo. Nafenso tingapeze njila zimene tingathandizile anthu ena. N’ndani amene tingathandize? Tingathandize okalamba, anthu amene ali na vuto la thanzi, amene akutsutsidwa ndi a m’banja mwawo, osungulumwa, ndi ofeledwa. Tingathandizenso acicepele amene akukakamizidwa kucita zoipa, kapena amene afuna kukhala na “umoyo wapamwamba” m’dzikoli, monga kucita maphunzilo apamwamba, kulemela, kapena kufuna kukhala katswili. (1 Ates. 3:1-3; 5:11, 14) Pezani njila za mmene mungaonetsele cikondi ceni-ceni kwa ena mukakhala pa Nyumba ya Ufumu, mu ulaliki, pamene mukudya ndi ena, kapena pamene mukambilana na wina pa foni.

it-1 406

Mabuku a m’Baibo

M’Baibo muli umboni wosatsutsika woonetsa kuti zolemba za Mose zinali zocokela kwa Mulungu, zouzilidwa na iye, zodalilika, komanso zokhala na mfundo zabwino zothandiza pa kulambila koona. Sikuti Mose anadziika yekha kukhala mtsogoleli na mkulu wa asilikali wa Aisiraeli, poyamba Mose anaikana nchito imeneyi. (Eks. 3:10, 11; 4:10-14) M’malo mwake, Mulungu anacita kumusankha na kumupatsa mphamvu zocita zozizwitsa, cakuti ngakhale ansembe ocita zamatsenga a Farao anafika povomeleza kuti Mose anasankhidwa na Mulungu. (Eks. 4:1-9; 8:​16-19) Kuwonjezela apo, sikuti Mose anacita kudzifunila kukhala wodziŵa kulankhula pagulu komanso mlembi. M’malomwake, mwa kumvela lamulo la Mulungu komanso motsogoleledwa na mzimu woyela wa Mulungu, Mose analankhula ndipo analemba mbali youzilidwa ya Baibo.​—Eks. 17:14.

AUGUST 24-30

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 19–20

“Mfundo za Malamulo Khumi Zotithandiza”

w89 11/15 6 ¶1

Kodi Malamulo Khumi Amatanthauzanji kwa Inu?

Malamulo anayi oyambilila amagogomezela maudindo athu kwa Yehova. (Loyamba) Ni Mulungu amene amafunabe tidzipeleke kwa iye yekha. (Mateyu 4:10) (Laciŵili) Palibe mlambili wake na mmodzi yemwe amene ayenela kugwilitsila nchito mafano. (1 Yohane 5:21) (Lacitatu) Kugwilitsila kwathu dzina la Mulungu kuyenela kukhala koyenela ndiponso kolemekezeka, osati konyozeka. (Yohane 17:26; Aroma 10:13) (Lacinayi) Moyo wathu wonse uyenela kuzikidwa pa zinthu zopatulika. Kucita izi kumatithandiza kuti tipumule, kapena ‘kusunga sabata,’ ku njila zodzilungamitsa.​—Aheberi 4:​9, 10.

w89 11/15 6 ¶2-3

Kodi Malamulo Khumi Amatanthauzanji kwa Inu?

(Lacisanu) Khalidwe la kumvela kwa ana kwa makolo awo ni maziko amene amathandizila kuti m’banja mukhale m’gwilizano. Izi zimabweletsa madalitso a Yehova. Ndipo ni ciyembekezo cabwino koposa cotani nanga cimene “lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo” limeneli limapeleka! Sikokha “Kuti zinthu zikuyendele bwino” koma ‘kuti ukhalenso ndi moyo wautali padziko lapansi.’ (Aefeso 6:1-3) Popeza tikukhala “m’masiku otsiliza” a dongosolo ili loipa, kumvela Mulungu kotelo kumapatsa acicepele ciyembekezo ca kusafa konse.​—2 Timoteyo 3:1; Yohane 11:26.

Cikondi ca mnansi cidzatiletsa kusamuvulaza kupitila m’zocita zoipa monga izi (La namba 6) kupha, (La namba 7) cigololo, (La namba 8) kuba, ndipo (La namba 9) kunena mabodza. (1 Yohane 3:10-12; Aheberi 13:4; Aefeso 4:28; Mateyu 5:37; Miyambo 6:16-19) Koma bwanji ponena za zolinga zathu? Lamulo (Lakhumi), loletsa kusilila, limatikumbutsa kuti Yehova amafuna kuti zolinga zathu zizikhala zoongoka nthawi zonse m’maso mwake.​—Miyambo 21:2.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-2 687 ¶1-2

Wansembe

Ansembe Acikhristu. Yehova analonjeza Aisiraeli kuti ngati adzasunga pangano lake adzakhala ‘ufumu wake wa ansembe ndi mtundu wake woyela.’ (Eks. 19:6) Ngakhale n’conco, mzele wa ansembe wa Aroni unali kudzapitiliza mpaka pamene mkulu wansembe adzabwela amene anali kucitilidwa mthunzi. (Aheb. 8:4, 5) Unali kudzakhalapo mpaka pamene pangano la Cilamulo linali kudzatha na kulowedwa m’malo na cipangano catsopnao. (Aheb. 7:11-14; 8:6, 7, 13) Lonjezo limeneli poyamba linapelekedwa ku mtundu wa Isiraeli cabe kuti adzakhala ansembe a Yehova amene adzatumikila m’makonzedwa a Ufumu wa Mulungu umene unalonjezedwa. Mkupita kwa nthawi mwayi umenewu unapatsidwanso kwa anthu a mitundu ina.​—Mac. 10:34, 35; 15:14; Aroma 10:21.

Ni Ayuda ocepa cabe amene anavomeleza Khristu, conco mtunduwo unalephela kutulutsa anthu a ufumu weni-weni wa ansembe na mtundu woyela. (Aroma 11:7, 20) Cifukwa ca kusakhulupilika kwa Aisiraeli, Mulungu anawacenjezelatu za zimenezi kupitila mwa mneneli wake Hoseya zaka zambili m’buyomo. Anati: “Popeza iwo akana kundidziŵa, inenso ndidzawakana kuti azinditumikila ngati wansembe wanga. Popeza iwo aiwala lamulo la ine Mulungu wawo, inenso ndidzaiwala ana awo.” (Hos. 4:6) Mogwilizana na zimenezi, Yesu anauza atsogoleli aciyuda kuti: “Ufumu wa Mulungu udzacotsedwa kwa inu n’kupelekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.” (Mat. 21:43) Ngakhale n’telo, Yesu Khristu, popeza anali pansi pa Cilamulo ali pano padziko lapansi, anazindikila kuti unsembe wa Aroni unali kugwilabe nchito, ndipo anauza anthu amene anawacilitsa matenda a khate kuti apite kwa wansembe na kupeleka zofunika zimene adzamuuza kupeleka.​—Mat. 8:4; Maliko 1:44; Luka 17:14.

w04 3/15 27 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Ekisodo

20:5​—Kodi zikutanthauza ciani kuti Yehova ‘amalanga ana cifukwa ca atate awo’? Munthu aliyense akakula, amaweluzidwa malinga na khalidwe kapena maganizo ake. Koma pamene mtundu wa Isiraeli unayamba kulambila mafano, mibadwo ya m’tsogolo ya mtunduwu inavutika cifukwa ca zimenezi. Ngakhalenso Aisiraeli okhulupilika anavutika na zotsatilapo zake m’lingalilo loti kutsatila zipembedzo zonyenga kwa mtunduwo kunacititsa kuti avutike kwambili kukhalabe okhulupilika.

AUGUST 31–SEPTEMBER 6

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EKSODO 21-22

“Muzionetsa kuti Mumaona Moyo Mmene Yehova Amauonela”

it-1 271

Kukwapula

Mwini kapolo waciheberi anali kuloledwa kukwapula kapolo wake wamwamuna kapena wamkazi na mkwapu ngati kapoloyo anali wosamvela kapena woukila. Koma ngati kapoloyo wafa pokwapulidwa, mwini kapoloyo anali kulandila cilango. Koma ngati kapoloyo sanafe kwa tsiku limodzi kapena masiku aŵili pambuyo pokwapulidwa, umenewu unali umboni woonetsa kut mwini kapoloyo analibe colinga comupha mumtima mwake. Iye anali na ufulu wopeleka cilango, cifukwa kapoloyo anali “cuma cake.” Si capafupi munthu kuwonongelatu katundu wake wofunika, cifukwa kucita zimenezi kungakhale kosapindulitsa. Komanso, ngati kapolo wafa patapita tsiku limodzi kapena masiku angapo, sizikanadziwika kuti anafa cifukwa cokwapulidwa kapena pa zifukwa zina. Conco, ngati kapolo wakhalabe na moyo kwa tsiku limodzi kapena masiku aŵili, mwini kapoloyo sanali kulandila cilango.​—Eks. 21:20, 21.

lvs 95 ¶16

Kodi Mumaona Moyo Mmene Mulungu Amauonela?

16Kwa Yehova, moyo wa munthu aliyense ni wofunika. Ngakhale moyo wa mwana ali m’mimba. Malinga na Cilamulo ca Mose, ngati munthu wina mwangozi wavulaza mzimayi wapakati, cakuti iye n’kumwalila, kapena mwana ali m’mimba, kwa Yehova munthuyo anali kukhala na mlandu wa kupha munthu. Ngakhale kuti inali ngozi, koma cifukwa panafa munthu, moyo wake unafunika kulipilidwa. (Ŵelengani Ekisodo 21:22, 23.) Kwa Mulungu, mwana ali m’mimba ni munthu wamoyo. Ndiye muganiza amamvela bwanji munthu akacotsa mimba? Nanga muganiza amamvela bwanji poona mamiliyoni a makanda amene amatayidwa caka ciliconse mwa kucotsa mimba?

w10 4/15 29 ¶4

Yehova Amafuna Kuti Mukhale Otetezeka

Mfundo za Cilamulo zinali kugwilanso nchito ziŵeto zikavulaza munthu. Ngati ng’ombe yagunda munthu mpaka kumupha, mwiniwake wa ng’ombeyo anayenela kuipha kuti anthu ena atetezeke. Popeza mwini wa ng’ombeyo sanali kudya nyama yotele kapena kuigulitsa, iye anali kuluza kwambili. Nanga ng’ombe ikavulaza munthu, koma mwiniwake osacita cili-conse pofuna kupewa ngozi ina, kodi cinali kucitika n’ciani? Ngati ng’ombe imeneyo yapha munthu, ng’ombeyo inali kuphedwa ndipo mwiniwake anali kuphedwanso. Lamulo limeneli linali kucititsa kuti aliyense amene anali na cizolowezi cosasamalila ziŵeto zake, asinthe.​—Eks. 21:28, 29.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w10 1/15 4 ¶4-5

N’cifukwa Ciani Muyenela Kudzipatulila kwa Yehova?

4Kudzipatulila kwa Mulungu si nkhani yamaseŵela ayi. Limeneli si lonjezo wamba. Koma kodi kudzipatulila kumatithandiza motani? Tiyeni tiyelekezele zimenezi na zimene zimacititsa kuti anthu akhale na ubwenzi wolimba. Kuti munthu ukhale na mnzako wa ponda apa m’pondepo, pamafunika kuti nawenso uzicitapo kanthu. Paubwenzi wotelo mumakhulupililana kwambili ndipo mumakhala okonzeka kuthandizana m’njila zosiyana-siyana. M’Baibo muli zitsanzo za mabwenzi amene anali kugwilizana kwambili. Mwacitsanzo, Davide na Yonatani anafika pocita pangano la ubwenzi wawo. (Ŵelengani 1 Samueli 17:57; 18:1, 3.) Ngakhale kuti zotelezi sizicitikacitika, munthu ukamadziwa kuti mnzako angasunge malonjezo amene mungapangane, ubwenzi wanu umakhala wolimba.​—Miy. 17:17; 18:24.

5Cilamulo cimene Mulungu anapeleka kwa Aisiraeli cinafotokozanso njila ina imene pangano linali kuthandizila anthu. Ngati kapolo amene mbuye wake anali wabwino akufuna kuti azikhalabe naye, anali kucita pangano na mbuye wake kuti adzam’gwilila nchito mpaka kalekale. Cilamulo cinali kukamba kuti: “kapoloyo akanena motsimikiza kuti, ‘Ndimam’konda kwambili mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana anga, ndipo sindikufuna kucoka monga womasulidwa,’ pamenepo mbuye wakeyo azibwela naye pafupi ndi Mulungu woona ndi kufika naye pacitseko kapena pafelemu. Akatelo mbuye wakeyo amuboole khutu ndi coboolela, ndipo iye adzakhala kapolo wake moyo wake wonse.”​—Eks. 21:5, 6.

it-1 1143

Nyanga

Mawu a pa Ekisodo 21:14 angatanthauze kuti ngakhale wansembe anali kuphedwa ngati wapha munthu wina, kapena kuti kugwila nyanga ya guwa lansembe sikunali kuteteza munthu aliyense wopha munthu mnzake mwadala.​—Yelekezelani na 1 Maf. 2:28-34.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani