CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 31-32
Pewani Kupembedza Mafano
32:1, 4-6, 9, 10
Cioneka kuti Aisiraeli anatengela maganizo a Aiguputo pa nkhani ya kulambila mafano. Masiku ano, munthu angalambile mafano m’njila zosiyana-siyana, ndipo zina zingakhale zovuta kuzizindikila. N’zoonekelatu kuti sitingayambe kulambila mafano eni-eni ooneka. Koma kungakhale kupembedza mafano ngati tilola zilakolako zathu zadyela kutilepheletsa kulambila Yehova na mtima wonse.
Ni zinthu ziti pa umoyo wanga wa tsiku na tsiku zimene zinganiceutse pa kulambila Yehova? Nanga ningacite ciani kuti zinthuzo zisamanilamulile?