Zimene muyenela kucita kuti mupindule kwambili na maphunzilo a Baibo amenewa
Coyamba ŵelengani mawu oyamba pa masamba 2 na 3, kenako tambani VIDIYO.
GAWO LOYAMBA
Pokonzekela phunzilo lililonse, ŵelengani gawo loyamba. Mafunso a zilembo zakuda kwambili (A) komanso malemba (B) amatsindika mfundo zazikulu. Ndipo onani kuti malemba ena ni olemba kuti “ŵelengani.”
GAWO LAPAKATI
Ciganizo coyamba (C) pansi pa kamutu kakuti Kumbani Mozamilapo cifotokoza zimene mudzakambilana. Timitu ting’ono-ting’ono (D) tionetsa mfundo zazikulu zokambilana. Pamodzi na mphunzitsi wanu, ŵelengani malemba, yankhani mafunso, komanso tambani mavidiyo.
Kacithunzi ka VIDIYO kamapititsa ku vidiyo kapena odiyo yomveketsa bwino nkhani yochulidwayo. Mavidiyo ena amaonetsa nkhani zimene zinacitikadi. Ena ni a zitsanzo cabe, koma zoimilako zocitika zenizeni.
Onani zinthuzi na timawu take (E), ndiponso ganizilani mmene mungayankhile pa mbali yakuti Anthu Ena Amakamba Kuti (F).
GAWO LOTHELA
Cidule Cake na Mafunso Obweleza (G) ndizo mbali zomaliza phunzilo. Lembani deti imene mwatsiliza phunzilo. Mbali yakuti Colinga (H) ikupatsani zofunika kucita. Ndipo pa mbali yakuti Fufuzani (I) pali zimene mungasankhe kuŵelenga kapena kutamba.
Zamkatimu
|
|
|
|
Mopezela mavesi m’Baibo
Baibo inapangidwa posanja mabuku ang’ono-ang’ono okwana 66. Ili na zigawo ziŵili: Malemba a Ciheberi na Ciaramu (“Cipangano Cakale”) komanso Malemba a Cigiriki Acikhristu (“Cipangano Catsopano”).
Posonyeza malemba m’buku lino, tawalemba motele: Dzina la buku la m’Baibo (A), ndiyeno caputala (B), kenako vesi kapena mavesi (C).
Mwacitsanzo, Yohane 17:3 itanthauza buku la Yohane, caputala 17, vesi 3.