NYIMBO 34
N’dzayenda mu Umphumphu Wanga
Yopulinta
(Salimo 26)
1. Mlengi wanga, ine nikupempha
Kuti mufufuze za mu mtima mwanga.
Muniyese, O niweluzeni;
Mudzapeza kuti nidalila imwe.
(KOLASI)
Koma ine, nikulonjezani
Kuti nidzakhala wokhulupilika.
2. Sinikhala na anthu ocimwa,
Nimapewa onse ocita zoipa.
Conde m’saniononge pamodzi
Ndi anthu ankhanza, ozonda co’nadi.
(KOLASI)
Koma ine, nikulonjezani
Kuti nidzakhala wokhulupilika.
3. Nimakonda nyumba yanu M’lungu.
Nimasangalala kulambila imwe.
Nidzakulambilani mokondwa,
Nidzaimba nyimbo zokutamandani.
(KOLASI)
Koma ine, nikulonjezani
Kuti nidzakhala wokhulupilika.
(Onaninso Sal. 25:2.)